Gawo #301, December 21, 2022

YOSEFE, KUTUMIKILA NDI CHETE

Nthawi ya Khilisimasi ino okhulupirira dziko lonse lapansi amalingalira za nkhani yodabwitsa ya Mulungu kulowa mu dziko lathuli munjila yobadwa ngati khanda. Ndinkhani yodzala ndi angelo, maloto, zozizwa, ndi zochititsa kaso. Pakatikati pa nkhani tikuona Yosefe ndi Maria ali pa ulendo wa Ku Betelehemu, kupeza malo opumulira amene agonemo usiku omwe Yesu anabadwa. Pomwe muli zinthu zochitika zambiri munkhaniyi ndi maphunziro ambiri a utsogoleri  munkhaniyi, tiyeni tione mbali yomwe Yosefe anatenga munkhaniyi. Chodabwitsa ndichoti, tilibe mau ena aliwonse ochokera kwa munthu wabamboyu. Anatumikira ndi Chete! (Werengani nkhani yake mu buku la Mateyu 1-2 ndi Luka 2) Zimenezi sizikutanthauza kuti sanalankhulepo, kungoti zomwe analankhulazo palibe chomwe chinasungidwa. Uchete wake ukupereka chitsanzo kuti atsogoleri onse aphunzire kutumikira ndi chete.

Kutumikira ndi Chete kumatitengera Ku kumvetsela

Uchete wa Yosefe unamulimbikitsa kuti amvetsere ndi kumvetsela  bwino! Munthawi yomwe amaganizira kuti apange motani ndi  mkazi oti akwatire yemwe wapezeka ndi pakati, anamvetsera pomwe Mulungu ankalankhula naye kudzela mu loto.(Mateyu 1:18-21). Zikadakhala zovutilapo kuti iye amve liwu la Mulungu akadakhala kuti anali atalengeza mokweza zomwe amaganizira kuti achite. Ndondomeko zinali zilipo kale mmalingaliro ake, koma zinali zisanatulukire pakamwa pake ndipo anatha kumvetsela ndi kusintha ndondomeko zakezo. Adamvetselanso pomwe loto lake linawalangiza kuti  athawile Ku Egypto kupewa mkwiyo wa mfumu Herodi. Anawonetsera bwino mau omwe Yakobo, yemwe nkutheka ndi mwana wake, azalembe mtsogolo,

Yakobo 1

19" Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima."

Nkutheka Yakobo anaphunzira zimezezi powonetsetsa bambo ake. Atsogoleri ambiri amika chidwi chawo pa zomwe amalankhula ndikutaya nthawi yawo yambiri kulankhula koposa kumvetsela. Yosefe akuphunzitsa atsogoleri mu utumiki kuti Uchete umatutengera Ku kumvetsela. Atsogoleri mu utumiki amazindikira kuti pomwe akulankhura  sakumvetsera.

Kutumikira ndi Chete kumaonetsera Ena

Mateyu 2

9 Atamva mawu a mfumu, ananyamuka ulendo wawo, ndipo taonani nyenyezi anayiona kummawa ija, inawatsogolera mpaka inayima pamwamba pa nyumba yomwe munali mwanayo.

11 Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye.

Yosefe sanatchulidwepo pa kufika kwa anzeru a kummawa! Ndipo mu malo ambiri Maria akutchulidwa poyamba ndi kulemekezedwa kwambiri. Yosefe mwambiri anaonetsa atsogoleri wamphamvu. Anatenga Maria kukhala mkazi wake atamva kuchokera kwa mngero. Anamutcha dzina loti Yesu ndikupita naye kukamuonetsa mkachisi. Anatsogolera banja lake mmaulendo otuluka mdziko mwawo. Koma anachita ichi ndi mau ochepa, palibe yemwe analemba izi kwa ife. Uchete wake una unaonetsera ena!

Atsogoleri ambiri amazionetsera okha pakulankhula zambiri. Atsogoleri mu utumiki amaphunzira kuti pomwe akhala Chete kulankhula za Iwo okha, ena angathe kuwala. Amakhala achangu kuyamikira ena a pa gulu pawo mmalo moti akope chidwi kwa Iwo wokha. Amazindikira kuti kulankhula kumaonetsera nthawi zambiri olankhulayo pomwe Uchete  umaonetsera ena.

Kutumikira ndi Chete kumalimbikitsa kudzichepetsa

Itatha nkhani ya Yesu mu kachisi pa zaka 12 zakubadwa, sitikumvanso kutchulidwa kulikonse kwa Yosefe. Maria nthawi zina akutchulidwa Yosefe asanatchuludwe komanso nthawi zina akudumphidwa basi. Yosefe anatumikira ndi Chete ndipo sanapange chionetsero chosonyeza kusakondwa pa kusowa kwa kumupatsa ulemu pa utsogoleri wake. Kukhala Chete kwake kukutionetsera kudzichepetsa. Kuthekera kwake komvetsera ndi kuonetsera ena kukuwonetsa mtima  odzichepetsa wa mtsogoleri otumikira.

Atsogoleri ambiri amalankhula ndipo amaonetsetsa kuti aliyense ozungulira adziwe zomwe Iwo achita ndi mmene. dziko lathandizikira ndi Iwo. Koma atsogoleri mu utumiki duuu ndi mokhala chete nthawi zambiri, amatsogokera ndi kudzichetsa. Kukhala chete Kumalimbikitsa kudzichepetsa popanga atsogoleri Kukhala pa malo osaoneyela kwambiri.

Kukhala chete kwa Yosefe ndi chitsanzo chabwino kwa atsogoleri onse muutumiki. Chitsanzo chake mwachidziwikire sikutanthawuzira kuti tisamalankhule. Koma akutipatsa chitsanzo choti titumikire kwambiri pa kulankhula mochepa.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi ndi mochuluka motani ndatsogolera mwachete? Kodi moyo wa Yosefe ukundiuza kuti nditsogolere motani?
  • Kodi ndimakhala wachangu polankhula kapena kumvetsela? Kodi zimenezi zikhudza bwanji utsogoleri wanga? Kodi ndingachite chani kulimbikitsa kuthekera kwanga komvetsera bwino?
  • Kodi pali njila zomwe pakadali pano ndazionetsera ndekha polankhula? Kodi chichite chani kuti ndionetsele ena kwambiri mochuluka?
  • Kodi kuchuluka kwa malankhulidwe komwe ndimachita kumaonetsera motani za mtima wanga? Kodi kumaonetsera kuzikweza kapena kudzichepetsa?

 

Khilisimasi Yabwino kwa wina aliyense! Ndi chamwayi kulemba mau olingalira awa, ndipo ndili oyamika chifuwa mumawerenga. Perekani mphatso kwa abwenzi anu potumiza izi kwa Iwo ndikuwalimbikitsa kuti azilandira!

 

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

 

Mu nkhami yotsatirayi ,tiona mozama mmene Boazi anatumikilira  posunga mau make.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online