Taona kale kuti Boazi anali munthu wa chikhalidwe chabwino. Mtima wake ofuna kutumikira unkatsogolera machitidwe ake pomwe amakhala mwabwino ndi anthu, kulemekeza ofooka , kupereka molowa manja ndi kusunga mau ake. Mu phunziro lotsirizali tiona momwe Boazi anatumikilira popanga zinthu kutheka.
Rute 4
1 Nthawi yomweyo Bowazi anapita ku chipata cha mzinda ndi kukhala pansi kumeneko pabwalo losonkhanira. Tsono anangoona wachibale woyenera kulowa chokolo uja akufika. Ndipo Bowazi anati, “Patukirani kuno, bwenzi langa. Mubwere mudzakhale apa.” Choncho anapatuka nakakhala pansi.
2 Bowazi anayitananso akuluakulu khumi a mu mzindamo nati, “Dzakhaleni pansi apa,” ndipo anadzakhala pansi.
3 Kenaka anamuwuza oyenera kulowa chokolo uja kuti, “Naomi amene wabwera kuchoka ku Mowabu akugulitsa malo amene anali a malemu Elimeleki, mʼbale wathu uja.
Atsogoleri onse ndi anthu ochitapo kanthu;amapanga zinthu kutheka.Boazi akuonetsera momwe atsogoleri mu utumiki amapangitsira zithu kutheka munjira zomwe omaika chidwi chawo pa ena.
Atsogoleri mu Utumiki amapangitsa zinthu kutheka pogwiritsa ntchito nzeru ina.
Rute atabwera kuchokera kwa Boazi usiku, apongozi ake anamuuza.
Rute 3
18 Kenaka Naomi anati, “Mwana wanga, dikira mpaka titaona mmene zinthu zikhalire chifukwa munthuyu salekera pomwepo, mpaka zinthuzi zitakonzeka lero.”
Monga momwe Naomi anayembekezera Boazi anapanga zomwezo pompo pompo.Boazi anapita pa bwalo la mmudzi komwe zinthu zimachitikira.Anafika pa nthawi yoyenera ndipo anali okonzeka kuchita nthawi yomweyo atangofika. Anaitanitsa mkumano ndi kupereka mutu wake wa msonkhanowo momveka bwino. Boazi amachita zomwe atsogoleri amachita mwabwino,kupeza nzeru ina kuti zinthu zitheke.Koma chifukwa chani amachita izi?
Amayankha pa pempho la Rute ,mzimayi wamasiye. Monga wachibale anali ndi udindo pa chikhalidwe chawo kuthandiza Rute yemwe anali ndi chosowa. Ngakhale mwachiziwikile amapezapo mkazi kuchokera pa nzeru imeneyi koma machitidwe ake sadali ozikonda. Atsogoleri mu utumiki amapereka nzeru kuti apangitse zinthu kutheka koma amachita izi kuchokera mu mtima omwe umaika chidwi pa ena kopsosa pa Iwo eni.
Atsogoleri mu utumiki amapangitsa zinthu kutheka popanga ukadziotche.
Kulowa chokolo kunaali kupanga ukadziotche. Wachibale amayembekezeka kutenga chuma cha munthu amene wamwalira, komanso kukwatira mkazi osiyidwayo. Ana obadwa kuchokera kwa ubale umenewu amayenera kukhala a malemu mamuna wa mkaziyo zomwe zimagawa munda wa olowa chokoloyo.Boazi anaipereka nkhaniyo kwa m'bale wake podziwa kuti bambo ameneyu ndi yemwe amayenera kulowa chokolo kwa Naomi.Akadavomera, Rute ndi chuma zikanapita kwa iye mmalo mwa Boazi. Boazi anali ofuna kupanga ukadziotche pomwe wachibaleyu samafuna. Komanso,anali ofuna kuchita zomwe atsogoleri amachita, kupanga ukadziotche kuti zinthu ziyende.Koma atsogoleri mu utumiki, ngati Boazi, amapanga ukadziotche osati ongopindulira iwo okha komanso Iwo amene amawatumikira.
Atsogoleri mu utumiki amapangitsa zinthu kutheka petenga udindo
Pamene wachibale uja anakana ,Boazi anali okonzeka kutenga udindo.
Rute 4
9 Ndipo Bowazi anawuza akuluakuluwo ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zinali za malemu Elimeleki, zonse zimene zinali za malemu Kiliyoni ndiponso za malemu Maloni.
10 Ndatenganso Rute Mmowabu uja mkazi wa malemu Maloni, kuti akhale mkazi wanga, kuti dzina la malemu Maloni lisungike pa cholowa chake, ndipo lisafafanizike pakati pa abale ake ngakhalenso mʼmudzi mwake. Nonsenu ndinu mboni lero lino.”
atsogoleri onse amapanga zinthu kutheka potenga udindo.Boazi, ngati mtsogoleri, anatenga mbali yomwe chidwi chinali pa ena, osati pa iye yekha. Atsogoleri otumikita lowanipo ndikutenga udindo omwe upindilire ena.
Moyo wa Boazi ndi chitsanzo kwa atsogoleri onse muutumiki. Anali munthu "omvetsetsa" yemwe machitidwe ake a utsogoleri ankasefukira kuchoka mumtima mwake kuti atumikire. Tsatani chitsanzo chake ndi omwe mukuwatumikira lero! |