jpeg

Gawo 273, November 25, 2020

Phokoso la utsogoleri wa chete- mmoyo

Kodi utsogoleri umamveka ngati chani? Nthawi zambiri timaganiza za mtsogoleri ngati waumunthu wamphamvu, komanso wokakamiza, omwe mofuwula amalengeza masomphenya awo omwe Mulungu waapatsa ndi dongosolo lawo lodabwitsa losintha dziko. Amalankhula mofuwula ndi kuchititsa pokhazikitsa ndi kulengeza.
Amakula mukuchititsa pochita maphunziro olankhula pa gulu.
Kulankhula bwino ndi chachidziwikire kuti ndi gawo lofunikira kwambiri la utsogoleri koma baibulo lili ndi zambiri zomwe limanena za mphamvu ya chete!
Mu gawo ili tizindikira kuti utsogoleri wa kachetechete umalankhula mofuwula mu magawo ambiri osiyanasiyana. Atsogoleri otumikira amaphunzira kulemekeza phokoso la chinunu powonjezera kuchititsa kwawo! Paulo akupereka ndondomeko ya moyo wathu wonse:  Pakutinso munawachitira ichi abale onse a mMakedoniya lonse. Koma tikudandaulirani, abale muchulukireko koposa ndi kuti muchiyese kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuwuzani; kuti mukayende oona mtima pa iwo akunja, ndikukhala osasowa kanthu (1 Thessalonians 4: 10-12).
Paulo akulimbikitsa awerengi ake ‘kukhumba kukhala moyo wa chete.’ Kukhumba ndi chete sizimapezeka muchiganizo chimodzi nthawi zambiri! Atsogoleri ambiri amakhumba zinthu zambiri. Amafuna chipambano. Amapanga dongosolo lochitira ntchito. Amalota zopanga ndalama, kupanga mpingo waukulu kapena kukhudza dziko. Amakonda zolinga! Koma Paulo akuphatikiza cholinga chosazolowereka ,  ‘chikhale chokhumba chanu kukhala moyo wa chete.’ Vesi iyi ikutipatsa ma phindu atatu omwe amachitika pomwe atsogoleri otumikira aphunzira kutsogolera mwa chete.

Utsogoleri wa chete umalimbikitsa tcheru

Paulo akuti phindu loyamba la moyo wa chete kapena odekha ndi kuphunzira ‘kusamalira za iwe mwini.’ Atsogoleri nthawi zambiri amachoka mmalo awo a ulamuliro kuti apereke maganizo awo pa zinthu zomwe sizikuwakhudza. Chimodzi cha zoopsa za kulankhula mawu ambiri ndi choti pomwe atsogoleri amaliza kulankhula zabwino, amanena zinthu zoipa kapena miseche! Pomwe amaliza kulankhula choonadi, amayamba kugawana ‘theka la choonadi’ ndipo kenako mabodza.
Kukhala moyo wa chete kumapangitsa mtsogoleri wotumikira kukhala tcheru pa magawo okhawo omwe Mulungu wamuitanirako. Kudzera mu chitsanzo chawo atsogoleri otumikira amachititsa ena kuti adzisamaliranso zawo.

Utsogoleri wa chete umapangitsa ntchito kuchitika.

Paulo akutibetchera ife kukhala chete ndi ‘kugwira ntchito ndi manja athu.’ Atsogoleri ena amataya nthawi yambiri kuwafunsa ena kuti awathandize popeza iwo alibe nthawi yogwira ntchito! Moyo wa chete umalunjika pokhala chitsanzo kwa ena, powonetsa mmalo molankhula. Chotsatira ndi choti ‘sindidzadalira wina.’ Atsogoleri otumikira mwa chete amapanga ntchito kutheka. Amatsogolera pogwira ntchito poitana ena kuti athandizane nawo.

Utsogoleri wa chete umaumba ulemu.

Paulo akutiuza ife kukhala wa chete ndi cholinga choti; ‘kuti mukayende oona mtima pa iwo akunja,’ Atsogoleri ambiri amakonzekera bwino pomwe akuwonekera ku gulu, koma Paulo akutikumbutsa ife kukhala moyo wokhulupirika  wa chete wa tsiku ndi tsiku. Kutsogolera kwa chete uku ‘kudzapangitsa kuti tipatsidwe ulemu ndi akunja.’ Atsogoleri omwe amapanga phokoso lochuluka angathe kusangalatsa anthu omwe ali  ‘mkati’ koma amavutika kuchulukitsa kuchititsa kwawo kunja kwa gulu limenelo. Atsogoleri otumikira amaphunzira kuti kutsogolera kwa chete kumakhudza ngakhale omwe ali ‘kunja’ amaumba kuchititsa powirikiza kuchita zoyenera.
Langizo la Paulo likukumbutsa atsogoleri otumikira kuti kukhala moyo wa chete sikumachepetsa kuchititsa koma kumachulukitsa. Atsogoleri otumikira amachititsa pomwe akukhala miyoyo ya chete. Amapita pamwamba pokhala chete!

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • Ndi magawo ati omwe ndimayesedwa kulankhula omwe simadera a udindo wanga? Zotsatira zake ndi zotani mu utsogoleri wanga?
  • Kodi pali magawo omwe ndikuwauza ena kuchita zinthu zomwe ine sindikufuna kuchita? Ndi chani chomwe chiyenera kusintha kuti ndikatsogolere mwa chitsanzo?
  • Kodi pali kusiyana pakati pa ‘moyo wanga wa tsiku ndi tsiku’ ndi momwe ndimaonekera pa gulu? Ngati ndi choncho, ndi chani chomwe chiyenera kusintha ndipo chichitika liti?
  • Kodi pali ziopsezo pomwe tikukhala moyo wa chete kwambiri? Kodi ndingaziteteze bwanji ku ziopsezo ngati izi?
  • Kodi ndingaike bwanji pa mulingo ofanana maitanidwe okhala ‘moyo wa chete’ ndi maitanidwe okhala kazembe wa Khristu? Kodi kuopsa kochita koposa muyeso mwina pokhala chete kapena pochita phokoso ndi kotani?
    Mu gawo lotsatira , tidzawona Phokoso la utsogoleri wa chete….mu kulingalira

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatira chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembatsa mwaulere komanso kuwona magawo akale. Mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.  Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi Abusa Joseph Saizi, josephsaizi2017@gmail.com
 

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2020

Modify your subscription    |    View online