Gawo #299, October 26, 2022

Boazi: Kutumikira Posunga Mau Ake

Pokhala munthu "oyima bwino" Boazi anatumikira ena mu njira zingapo zomwe taona kale. Amakhala mwabwino ndi wanthu,amakhala ndi ofooka mwaulemu,ndipo ankapeleka molowa manja. Ankatumikiranso ena posunga mau ake.kangapo mu nkhani ya Rute, Boazi anachita zomwe adanena kuti achita ndipo zikupereka chitsanzo kwa atsogoleri mu utumiki mu gawo ili la ungwiro.

Rute 2

8 Choncho Bowazi anati kwa Rute, “Tamvera mwana wanga, usapite kukakunkha mʼmunda wina, ndipo usachoke mʼmunda uno. Koma uzitsata adzakazi angawa.

9 Uziyangʼana munda akukolola anyamatawo akamakolola mʼmundamu, ndipo iwe uzitsata pambuyo pawo. Ndawawuza anyamatawo kuti asakuvutitse. Ndipo ukamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawa atunga.”

15 Atanyamuka kuti azikakunkha, Bowazi analangiza anyamata ake kuti, “Ngakhale mayiyu azikunkha pakati pa mitolo musamuletse ndi kumuchititsa manyazi.

16 Koma muzimusololerako ngala zina za mʼmitolo ndi kumusiyira kuti azikunkha ndipo musamukalipire.”

Rute 3

11 Ndipo tsopano mwana wanga usaope. Ine ndidzakuchitira chilichonse udzapemphe popeza anzanga onse amʼmudzi muno akudziwa kuti ndiwe mkazi wa khalidwe labwino.

12 Ngakhale kuti ndinedi wachibale woyenera kukusamala, koma alipo wachibale weniweni kuposa ine.

13 Gona konkuno usiku uno mpaka mmawa. Tsono ngati iyeyu adzakulowa chokolo, chabwino alowe. Koma ngati safuna kutero, ine ndikulumbira pamaso pa Yehova Wamoyo kuti ndidzakulowa chokolo. Ugone kuno mpaka mmawa.”

Kodi tingaphunzire chani kwa Boazi za mmene tingatumikilire posunga mau athu?

Atsogoleri mu utumiki amakumbukira mau awo.

Boazi analonjeza Rute kuti antchito ake amuna samuta chipongwe. Awa sanali mau oyelekeza chabe anali ndi cholinga chokwanilitsa. Anakumbukira zomwe anamulonjeza ndipo anachitapo kanthu mwachangu. Atsogoleri ambiri amalankhula zambiri ndikupanga malonjezo ndicholinga  chokondweletsa Iwo amene akuwatsogolera. Koma alibe cholinga chochitapo kanthu pa malonjezo awo ndipo mwachangu amaiwala zomwe adanena. Owatsatira mosachedwa amawaphunzira ndipo sawalabadira Ku mau awo opanda kanthuwo. Koma atsogoleri muutumiki amaganiza kaye asadalankhule chifukwa amafuna kuzakumbukira zomwe alonjezazo. Amachitapo kanthu mwachangu monga Boazi anachitira, kapena amakumbukira mwaiwo okha kuti azakwaniritse mau omwe alonjezawo.

Atsogoleri amakhala ndi chikumbumtima ndi kuyesetsa kukumbulira mau aliwonse omwe analonjeza.

Atsogoleri mu utumiki amalemekeza mau awo.

Boazi amakumbukira mau ake ndipo anawatsatira ndi kuchita.Adapita kwa ogwira nthito ake ndi kubweleza malangizo ake kwa Iwo kuti akwaniritse lonjezo anachita kwa Rute.Pomwe kenako anamulonjeza kuti achitopo kanthu pa pempho lake la ukwati,"Ndithudi pa Mulungu Wamoyo  ndichita."Boazi analanthula mau  Otsindika awa chifukwa anali mtsogoleri yemwe amalemekeza chomwe wazipereka kuchita.Atsogoleri ambiri amalankhula zambiri osati Kuchita.Koma Atsogoleri mu utumiki samati "Ndizachita " mwachibwana.Amalemekeza mau awo ndi kuchita moyenelera.

Atsogoleri mu utumiki amamanga mbiri ndi mau awo.

Boazi anakhala moyo wake polemekeza mau ake ndipo kutsimikizika kwake kunapanga mbiri yomwe mtsogoleri aliyense akuyenera kusilira.Rute atafotokozela Naomi zomwe Boazi adanena ,Naomi anayankha,"Dikira, mwana wanga ,kufikira utazindikira chomwe chitachitike .chifukwa munthuyu sapumula kufikira zonse zitakonzeka lero"(Rute 3:18).Mbiri ya Boazi sidamangidwe pa tsiku limodzi,zidali zotsatira za kutsimikiza polemekeza mau ake .Atsogoleri ambiri amalemekeza mau awo tsiku limodzi koma osati tsiku linalo.Koma atsogoleri mu utumiki amagwira ntchito molimbika tsiku ndi tsiku kuti atsatire malonjezo awo. Amapepesa akalephera ndikulimbikirabe  kuti akhale munthu osunga mau awo.Ndipo ndi nthawi,amamanga mbiri yomwe atsogoleri awo onse akhoza kudalira. 

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Werenganinso ma chaputala 4 a Rute kuyan'gana zisonyezo  zina za mmene Boazi anasungira mau ake. Mukuonapo ziti? Mu njira iti yomwe mungaphunzirepo kuchokera pa chitsanzo chake?
  • Kodi ndinaiwalapo chomwe ndinalonjeza kuchita? Kodi ndingachite chani kuthana ndi cholakwikachi?
  • Kodi pakadali pano ndalonjeza zambiri kuposa zokwaniritsa ?Kodi chotsatira ndi chani cha utsogoleri wanga? Kodi ndipange motani kuti ndizikwaniritsa mau anga?
  • Kodi ndikudziwika ngati munthu osunga liu anga? Ngati sichoncho, ndichifukwa chani ndipo ndisinthe chiyani?Ngati ndichoncho Kodi ndigwiritse motani kudalira komwe ena alinako mwa ine kuti ndiwatumikire bwino?

 

Mpaka nthawi ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

 

Mu nkhami yotsatirayi ,tiona mozama mmene Boazi anatumikilira  posunga mau make.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online