Tawona kale kuti Boazi anali "munthu wamaimidwe abwino". Khalidwe lake linaumba machitidwe ake a utsogoleri munjira yomwe amakhalira bwino ndi anthu ndi mmene amachitira ndi ofooka. Kupereka kwake moolowa manja kunaonetseranso khalidwe lake. Kawiri munkhaniyi Boazi anapereka moolowa manja kwa Rute.
Rute 2
14 Nthawi ya chakudya cha masana Bowazi anati kwa iye, “Bwera kuno, utenge buledi ndi kusunsa nthongo mu vinyo.” Choncho anakhala pansi pafupi ndi okololawo, ndipo Bowazi anamupatsa chakudya ndi nyama yowotcha. Anadya chilichonse amafuna ndipo chakudya china chinatsalako.
Rute 3
15 Bowazi anati kwa Rute, “Bwera mnacho kuno chofunda wavalacho ndipo uchiyale pansi.” Ndipo atayala, Bowazi anathira makilogalamu makumi awiri a barele ndi kumusenzetsa Rute. Rute anapita nakalowa mu mzinda.
Boazi anagawana chakudya chake ndi Rute mmunda kenaka anampatsanso chopereka moolowa manja cha chimanga.,chambiri chomwe iye akanakwanitsa kunyamula! Ndipo Rute sanali yekhayo yemwe anapindula kuchoka Ku mtima wake opereka moolowa manja. Panalinso ena omwe anadya limodzi mokondwa ndi Boazi ndi azimayi enanso omwe amagwira ntchito mmundamo. Boazi amatha Kupereka moolowa manja chifukwa mtima wake unali pa kutumikira. Kupereka kwake ndi chitsanzo kwa atsogoleri onse otumikira.
*Atsogoleri mu utumiki amapereka moolowa mania pomwe akuika chidwi chawo pa ena osati pa Iwo okha.*
Pomwe Boazi anakhala pansi kuti adye chakudya chake, akanangothokoza Mulungu chifukwa chompatsa chakudyacho. Koma anayang'ana yang'ana ndikuona kuti Rute analibe choti adye.Kotero ,anagawana naye, kupereka chake chabwino, osati zotsalira. Chidwi chake sichinali pa zozowa zake, koma pa zosowa za ena.Atsogoleri ambiri amazikundikira okha pamene akutsogolera.Amaganizira za zolinga zawo zoti afikire, za ndondomeko zawo ndipo amaona ena ngati njira yowathandizila kukwaniritsa mathero awo. Koma atsogoleri mu mutumiki amaona udindo wawo ngati mwayi otumikira omwe akuwatsogolera.Amaika chidwi chawo pa ena Iwo asanaziikemo.Chidwi chawo ndi cha kunja osati cha mkati mwawo.
*Atsogoleri mu utumiki amapereka mokondwela pomwe akuika chidwi chawo pa kupereka osati pa kulandila.*
Boazi anatsegula munda ndipo chilungamo chake amayembekezela zokolola.Koma chidwi chake chinali pa kupereka mmalo mopeza.Anawona chimanga ngati chinthu chomwe sichikanakwanilitsa zosowa zake zokha koma chomulora kupereka kwa ena ngati Rute.Iye anadziwa kuti opereka amalandilanso,koma cholinga chake chinali pongopereka ndi mtima okondwera.Atsogoleri ambiri ali pa maudindo a atsogoleri pa cholinga chopeza kuchokera muutsogoleri.Izi ndi monga mphatso za ndalama,zolipira milandu,kukhala ndi ulamuliro kapena kukonda mphanvu za ulamuliro.Koma atsogoleri mu utumiki amatsogolera kuti akapereke.Samaika mulingo wa kupambana kwawo pa zomwe amapeza koma pa zomwe amapereka.Chidwi chawo chili pa kupereka osati pa kupeza.
*Atsogoleri mu utumiki amapereka moolowa manja pomwe akuika chidwi chawo pa kuchuluka osati pa kusowa kwa zinthu.*
Boazi sanayang'ane pa zokolora zake ndi kuganiza kuti kupereka kumubweretsela kuluza pa zokolora zake.Sanaganizire kuti kugawa chakudwa chake kumupangitsa kukhala ndi njala.Anali ndi lingaliro la kuchuluka .Anazindikira kuti chinalipo cha onse ndipo kuti kupereka kumabweretsa dalitso mmalo mwa kusowa.Sadadziwe munthawiyi kuti azapeza mkazi ndi malo mu mbiri ya Israel ya kupereka kwake.Koma Boazi anali ataphunzila kale kuti atsogoleri omwe amapereka ndi omwenso amapeza phindu.Atsogoleri ambiri amaona chithu chovuta kupereka chifukwa amaona kuti zinthuzo ndi zopezeka patalipatali.Amaganiza kuti ngati apereka ,sangapeze zokwanila iwowo.Atsogoleri amenewa amapereka pokhapokha ngati awona kuti ali ndi zochuluka.Atsogoleri oganiza moterewa sapezanso zambiri kuti apereke!Koma atsogoleri mu utumiki amaona dziko la zochu
luka.Amapeza madalitso mu kupereka ndi kupeza chimwemwe cha kulandiranso. Kupereka kwawo kumatakasa ena kuti aperekenso, ndipo dziko limayamba kuyenda munjira zokongola. Chidwi chawo chili pa zochuluka, osati pa kupelewera. |