Gawo #297, September 27, 2022

BOAZI:Kutumikira pa Kulemekeza Ofooka

Monga tinawonera mu phunziro lapitali Boazi anawonetsa mtima wake kwa antchito ake, achilendo ndi akubanja kwake pokhala nawo bwino.Koma mmene anachitira kwa Rute, khalidwe lake likuwonetseledwa kwambiri mmene anawonetsela ulemu kwa iye,munthu osawerengedwa mmudzi. Chiyeso chachikulu cha utsogoleri si mmene mtsogoleri amachitira kwa apamwamba pake kapena kwa omwe afanana mphamvu,koma momwe amachitira ndi omwe ali pansi pawo,makamaka omwe amatengedwa kuti ndi ofooka.Rute,kumuona mbali zonse, anali munthu ofooka ndi wa chiyembekezo chochepa mmoyo. Anali ochoka mdziko lina, anali wamasiye, anali osauka, komanso analibe mwana! Koma Boazi akumulemekeza ndi kowonetsa atsogoleri onse otumikira momwe angakhalire ndi ofooka ozuungulira mu utsogoleri wawo.

*Atsogoleri mu Utumiki amalemekeza ofooka powabwezeletsela ulemu wawo.*

Rute 2

15 Atanyamuka kuti azikakunkha, Bowazi analangiza anyamata ake kuti, “Ngakhale mayiyu azikunkha pakati pa mitolo musamuletse ndi kumuchititsa manyazi.

16 Koma muzimusololerako ngala zina za mʼmitolo ndi kumusiyira kuti azikunkha ndipo musamukalipire.”

17 Choncho Rute anakunkha mʼmundamo mpaka madzulo. Kenaka anapuntha barele anakunkhayo, ndipo anakwanira pafupifupi makilogalamu khumi.(Ruth 2:15-17).

Rute amafunika thandizo,anali osauka ndinso wa njala!Iye ndi Naomi analibe malo komanso njila yomwe akadakololera mbewu.Atsogoleri ambiri akadathamangira kukumana ndi chosowa ndi mphatso.Koma Boazi  sakupereka chakudya kwa Rute!Mmalo mwake, akupereka mpata wabwino kuti iye agwire ntchito kuti apeze chakudya. Akuwonetsetsa kuti iye athe kupanga mbali yake kuti apeze chakudya. Anatha kupita kunyumba madzulo monyada.Boazi anabwezeletsa ulemu wake. Atsogoleri mu Utumiki amakhala ofuna kuthandiza koma amachita izi mu njira zomwe zimalora olandilawo amabwezeletsa ulemu wawo.

Rute 2

15 Atanyamuka kuti azikakunkha, Bowazi analangiza anyamata ake kuti, “Ngakhale mayiyu azikunkha pakati pa mitolo musamuletse ndi kumuchititsa manyazi.

16 Koma muzimusololerako ngala zina za mʼmitolo ndi kumusiyira kuti azikunkha ndipo musamukalipire.”

17 Choncho Rute anakunkha mʼmundamo mpaka madzulo. Kenaka anapuntha barele anakunkhayo, ndipo anakwanira pafupifupi makilogalamu khumi.(Ruth 2:15-17).

Rute amafunika thandizo, anali osauka ndinso wa njala!Iye ndi Naomi analibe malo komanso njila yomwe akadakololera mbewu. Atsogoleri ambiri akadathamangira kukumana ndi chosowa ndi mphatso. Koma Boazi sakupereka chakudya kwa Rute! Mmalo mwake, akupereka mpata wabwino kuti iye agwire ntchito kuti apeze chakudya.Akuwonetsetsa kuti iye athe kupanga mbali yake kuti apeze chakudya. Anatha kupita kunyumba madzulo monyada.Boazi anabwezeletsa ulemu wake. Atsogoleri mu Utumiki amakhala ofuna kuthandiza koma amachita izi mu njira zomwe zimalora olandilawo amabwezeletsa ulemu wawo.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Werengani ma chaputala 4 a Rute,makamaka chaputala 2, mufufuze zowonetsela mmene Boazi analemekezera ofooka.Mukuwonapo chani? Ndi munjira iti yomwe mungaphunzilire pa chitsanzo chake?
  • Kodi machititidwe anga ndi otani pa omwe ali ofooka "kodi singiwapatsa ulemu kuposa apamwamba anga? Alipo kodi munthu wina kapena  gulu la anthu omwe ndimawaona mopepusa? Munjira yanji yomwe ichi chikuonetsela khalidwe la mtima wanga?
  • Kodi ofooka ndindani mubungwe langa kapena mu dela langa? Kodi ndichitenji kuti ndiziwaona ngati anthu? Ndingachite chani chowathandiza kubwezeletsa ulemu wawo? Kodi ndingawakweze motani? Kodi pali kusiyana kwanji pakati pa "zopereka mwaukere" ndi "zopereka  zotukula  munthu"?
  • Kodi ndimayesedwa motani kuthandiza anthu munjira yomwe imatsitsa kulemekezeka kwawo? Kodi ndisinthe chani kuti ndipereke thandizo lomwe limamanga anthu pamwamba?

 

Mpaka nthawi INA, ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online