Gawo #296, September 13, 2022

BOAZI:Kutumikira Pokhala Bwino ndi Anthu

Tawona kale kuti Boazi anali munthu oyima bwino.Chomwe anali mkati mwake ndichomwe chidapanga zonse zomwe titha kuziwona kunja.Mu zinthu zotsalira za phunziroli tiwona mozamabwino  pa mfundo zisanu za matumikilidwe zomwe zikuwonetsera mtima wake ndi khalidwe lake.Poyamba,tiwonetsetsa pa momwe Boazi amakhalira bwino ndi ena.

Nthawi zambiri timamuwunika mtsogoleri pa zomwe anakwaniritsa .Anachita chani?Anafikira zolinga ziti?Anapanga chani?Awa ndi mafunso ofunikira,koma Boazi akuyitanira atsogoleri mu utumiki kugwiritsa njira zosiyana za mulingo.Tiyeni tiwonetsetse pa momwe Boazi amakhalira ndi magulu angapo a wanthu ndi zomwe atsogoleri akhoza kuphunzira pa chitsanzo chake.

Atsogoleri mu utumiki amakhala bwino ndi antchito awo

4 Mu nthawi yomweyo Boazi anafika kuchokera Ku Bethlehem ndi kuwapatsa moni antchito okolora ,"Ambuye akhale nanu!"anayankha (Rute 2:4).Awa ndi mau oyamba omwe tikumva kwa Boazi, mau a malonje.Mau ake oyamba ndi a mdalitso  ndi otitsimikizila ,kuwonetsa ulemu ndi ubale ndi Iwo.Anali bwana ,mwini wake ,olemba ntchito,Oyambitsa kampani.Koma Boazi sanakayendele ntchito yomwe yagwirika asanalumikizane ndi mitima yawo.Ndipo mayankhidwe awo anawonetsa kuti ulemu unali weniweni.Ogwira ntchito ambiri amayan'gana kumbali abwana awo akafika,kuwopa kukalipidwa kapena kuchotsedwa.Boazi akuphunzitsa atsogoleri mu utumiki kuti kukhala bwino ndi antchito ndi ndi njila yopambana ku maubale.Kukhala bwino ndi anthu kukhozanso kupangitsa kuti phindu  lituluke bwino!Koma atsogoleri mu utumiki amakhala bwino ndi antchito awo ,osati chifukwa choti apeze zotsatila zabwino,Koma chifukwa ndi chinthu choyenera kutero!

Atsogoleri mu utumiki amakhala bwino ndi alendo.

5. Boazi anafunsa kapitawo wa zokolora ,"Kodi mzimai wachichepeleyo ndi wa kwandani?6 Kapitawo anayankha"Ndi Mmoabu,yemwe anabwela kuchoka Ku dziko la Moabu ndi Naomi.8 Ndipo Boazi anati kwa Route,"Mwana wanga , tamvetsela,usapite kukakunkha Ku munda wina komanso usachoke mmunda uno,ukhale muno ndi azimayi antchito anga.9. Uziyang'ana munda akukolora anyamatamo,ndipo uzitsatira pambuyo pa azimayi .Ndawafotokozera azibambowo kuti asaike dzanja lawo pa iwe. Ndipo ukamva ludzu,uzikamwa madzi omwe azibambo atunga."(Rute 2:5-6,8,9).Pamenepa mu nkhaniyi ,Rute ndi mulendo kwa Boazi,munthu amene sadakumanepo naye. Atsogoleri ena amamuswaya mlendo.Ena amawonetsetsa kuti mlendo wachotsedwa pa chithu chawo.Koma Boazi anatenga nthawi kufuna kudziwa kuti ndindani ndipo pompo pompo kupeza njira yomuthandizira!sakufuna kumubweletsa mu gulu lake kuti akwanitse zolinga zake;anapeza njira yomuthandizira kukwanilitsa zolinga zake.Atsogoleri Mu utumiki  onani alendo ngati maumwayi atsopano otumikilira!

Atsogoleri Mu utumiki amakhala bwino ndi banja lawo

Pafupi ndi pothera nkhani ya Rute tikupezapo mnunsu wa momwe Boazi amakhalira ndi apabanja ake.1 Munthawiyi Boazi anakwera kupita Ku bwalo losonkhanira ndi kukhala pansi .Tsono anangoona wachibale oyenera kulowa chokolo uja akufika.Boazi anati ,"Bwela pano, mzanga,ndipo khala pansi,"ndipo anapita nakhala pansi(Rute 4:1).

Munjra zambiri ,wachibale uyu anali opikisana naye.Ngati oyenera kulowa chokolo poyambilira anaitanitsa malo a Naomi ndi mzimayi wamasiye Rute yemwe Boazi akufuna kuti akwatire.Koma Boazi akumutcha "mnzanga..." Anali ndi zokambilana zovutilapo zomwe zathera poti Boazi kukhala odalitsika kukwatira Rute.Boazi watumikira bwino apabanja ake popewa kugawanika kwa maubale.Anayanjanitsa chidwi chake ndi Iwo a apabanja pake ndipo aliyense kuchoka pamalopo mwabwinobwino.Atsogoleri Mu utumiki amakhala bwino ndi apabanja awo kulemekeza maubale kuposa zokhumba zawo.

Zoti tilingalirepo ndi kukambirana

  • Werengani ma chaputala 4 a Rute poyang'ana  zina za momwe Boazi amakhalira ndi anthu. Mukuona chani?Munjira iti yomwe mungaphunzilirepo pa chitsanzo chake?
  • Chimachitika ndi chani pa malo anga a utsogoleri ndikafika?kodi anthu amalandila kupezeka kwanga kapena amapenya kumbali?kodi ndingaike bwanji chidwi changa pa omwe ndikuwatsogolera osati ngati zipangizo zokwaniritsira masomphenya anga?
  • Kodi ndikuyenera kuwona motani anthu achilendo?kodi ndimawaona ngati chionongeko ?ngati othandiza oyenelera kwa ine? Kapena,ndimawaona ngati maumwayi atsopano otumikira?ndi mulendo otani amene ndakumana naye musabata yathayi ndipo ndi chani  chomwe Mulungu akundiitanira kuti ndimutipumikire?
  • Werenganinso nkhani ya Boazi ,munthu mmodzi,momwe akhalira ndi apabanja ake pa Rute 4:1-12.Ndi chani china chomwe mungaphunzirepo pa chitsanzo chake?ndi chifukwa chiyani zikadakhala zovuta kwa Boazi yemwe anali ndi chidwi chokwatira kuchitira ulemu opikisana naye ?kodi ndani mubanja langa yemwe ndimawaona zovuta kumutumikira?kodi ndipange chani mu sabatayi kuwalemekeza?

 

Mpaka nthawi ina ,ine wanu pa ulendo ,

 

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online