Gawo #295, August 31, 2022

Boazi:Kutumikira Pakuima Bwino.

Nkani ya Boazi tikuyiwona munkhani ya Ruth,mpongozi wakudziko  la chilendo wa Naomi. (Ngati nkhaniyi simukuyidziwa,tengani mphindi 10 kuwerenga buku la Rute).Boazi akutchulidwa mu nkhani yopezeka mutu was chiwiri,Naomi ndi Rute,onsewo amasiye ,atabwelera Ku Israeli kuchokera Ku dziko LA Moabu.Moyo wa Boazi okuyankhula mofatsabwino ndi mwamphamvu kwa onse atsogoleri mu Utumiki ndipo tionapo madela angapo omwe moyo wake ukutipatsa chitsanzo kwa ife.Choyamba chikubwela pamene akutifotokozera ife za iye koyamba. 

 

1Ndipo Naomi adali ndi m'bale wake kumbali ya malemu mamuna wake,Oyimabwino ochokera Ku banja la Alimeleki ,amene dzina lake lidali Boazi.(Rute 2:1). 

 

Boazi akumulongosola apa ngati "munthu oyimabwino" .Lingalirani pamenepo kwa kanthawi.Oyimabwino si liwu lomwe timagwiritsa ntchito kawirikawiri pofotokoza winawake.Koma likusonyeza mphamvu khalidwe labwino,komanso kuimabwino ndi Mulungu.likuwonetsera kulemekezeka  ndi machitidwe .Boazi anatumikira pokhala mwanuna Oyimabwino ndipo akupereka chitsanzo kwa atsogoleri onse mu utumiki. 

 

Atsogoleri mu utumiki amayima pa kuwumba khalidwe. 

 

Boazi, anali munthu wakhalidwe.Anatsogolera ndi nzeru,anali mwamuna wamalankhulidwe abwino ndipo amalemekeza ena. Zonsezi zikuonetsela munthu wa kwalidwe lokhazikika. Tiwona zambiri za khalidwe lake likuwonetsedwa poyera pomwe tikupitilira kuwona pa moyo wake mu phunziroli. Khalidwe lake likufunikiranso kwambiri tikawona munthawi yomwe iye adakhala ndimoyo. Mwa Rute tikuwona zowonetsela chowonadi  kuti si onse mu delaro adali ndi khalidwe la ngati la Boazi. Adakhala munthawi  ya Oweruza pomwe "aliyense adachita momwe anaonera " (oweruza21:25). Ndi munthu oyimabwino chifukwa cha khalidwe lake. Boazi akuphunzitsa atsogoleri mu utumiki kuti kutsogolera kumayambira ndi mkati. Akuwonetsera kuti utsogoleri kwambiri ndi uwu kuti ndife kuposa zomwe timachita. 

 

*Atsogoleri amayima pokhala moyo okakamira 

 

Boazi ndi Otchuka! Tikukambabe nkhani yake lero ,patadutsa zaka mazanamazana moyo wake utatha. Koma Boazi sadaganizileko kuti azakhala ndi chotisiyira chotere!Ankangochita chomwe chidali chabwino tsiku ndi tsiku .Atsogoleri kawirikawiri yan'ganani njira zobweletsera kusintha kapena kusiyana. Boazi akuphunzitsa atsogoleri mu utumiki kukakamira kukhala motsatira makhalidwe a Umulungu ndi njira ya matumikiridwe. Atsogoleri mu utumiki chitani chomwe ndi cholondola,osati kukwaniritsa zinthu zazikulu koma pa chifukwa chongoti chinthucho ndi choyenera. Amayima tsiku ndi tsiku pa makhalidwe awo abwino ndi kutsogolera ena ndi moyo okakamira pa chomwe ali. 

 

Atsogoleri mu utumiki amayima pa kusintha ena. 

 

Boazi anatumikira ngati mwamuna wa "maimidwe abwino" Ndipo chotsatira chake moyo wake unachitira ubwino ena.Onani zomwe anthu adanena pa kubadwa kwa mwana wake,' Obedi. 

 

14 Amayi adati kwa Naomi: "Ambuye atamandike ,amane tsiku la lero sadakusiye opanda okuyang'anira-owombola.Azakhale otchuka mu Israeli monse! (Rute 4:4) 

 

Moyo ndi khalidwe la Boazi lidathandiza Rute ndi apongozi ake Naomi.Komanso lidatulutsa mibadwo mibado ya atsogoleri otchuka mu Israeli, oyamba mfumu Davide kenaka kuposela apo Yesu!Khalidwe lake lizapitilira Ku mibadwo mibadwo. Boazi akuphunzitsa atsogoleri mu utumiki kuti tikaima bwino,timatumikira bwino.Timabweretsa kusintha pomwe tayima !

Zoti tilingalirepo ndi kukambirana:

  • Santhulani makhalidwe anayi a Rute ndi "kuyima" mmaganizo ake.Kodi mukuwonapo zitsanzo zina za Boazi zomwe zikuwonetsera kuti adali mwamuna oyimabwino? 
  • Kodi wena angati ndine" munthu woimabwino"? Kodi pali mipata mu khalidwe langa zomwe zikukhudzana ndi kuthekera kwanga kotsogolera?Kodi nditsatire ziti kuti zinthu izi zithe?Ndi madera ati omwe ndikufuna Mulungu asinthe moyo wanga? 
  • Kodi utsogoleri wanga ndimaika chidwi kwambiri pa mathero,kapena kukakamira kwa tsiku ndi tsiku.? 
  • Munjira ziti zomwe utsogoleri wanga ukuonetsera kukakamira kuchita chomwe chiri choyenera ? Ndichani chomwe Mulungu akufuna ndisinthe? 
  • Kodi akuyang'anira moyo wanga  ndi utsogoleri wanga pafupi ndani?Kodi mayimidwe anga abwino akuwakhudza motani? Kodi padzakhala kusintha kwanji pa zaka 100 kuchokera pano?Kodi zimenezi zindilimbikitsa motani kutumikira poyimabwino? 
 

Mpaka nthawi Ina ,ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Kutanthauzira kwa ma baibulo ena amati "munthu wamphamvu wachuma", " munthu odziwika wa khalidwe lolemekezeka","munthu wa chuma", ndinso "munthu oyenera" pofotokoza Boazi.

Munkhani yotsatirayi ,tiwona momwe Boazi adatumikilira  powaonetsera ubwino wena.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online