Gawo #294, August 16, 2022

ATSOGOLERI MU UTUMIKI TENGANI MBALI

Atsogoleri nthawi zambiri amakakamizidwa kufufuza mbali zosiyanasiyana  pa mbali zochuluka  za nthawi yathu ino.

Tikukhala mu dziko lomwe limatenga mbali mu zandale, zachikhalidwe, za umoyo, zachuma, ndi zina zotero. Mbali zomwe atsogoleri amasankha  kutsatila zimakhudza utsogoleri wawo ndi Iwo amene amatsatila. Pamene mtsogoleri wasankha mbali yolakwika,akhoza mwachangu kuikidwa pambali! Kodi mtsogoleri mu utumiki amasankha motani mbali yoti atsatire? Yoswa anakumana ndi munthu yemwe amapeleka thandizo kwa atsogoleri muutumiki posankha mbali.

13Pamene Yoswa anayandikira Yeriko,anayang'ana mmwamba ndipo anaona munthu mwamuna ataima kutsogolo kwake ndi lupanga mmanja mwake.Yoswa anamutsatira namufunsa ,"kodi uli mbali yathu kapena ya adani athu?" 14 "Ndilibe mbali,"Anayankha,"Koma ngati Olamulira gulu la nkhondo la Ambuye ndadza tsopano."Kenako Yoswa anagwetsa nkhope yake pansi kupereka ulemu, ndikumufunsa, "Uthenga otani umene Ambuye wanga  ali nawo kwa mtumiki wake?"15  Olamula gulu la  nkhondo la Ambuye anayankha nati,"Vula nsapato zako ,pakuti malo omwe waimawo ndi oyera." Ndipo Yoswa anapanga momwemo.(Yoswa 5:13-15).

Yoswa amatsogolera Anthu a Mulungu mu nkhondo yawo yoyamba. Iyi idali nthawi yovuta kwambiri. Kupambana mu nthawi imeneyi ikadakweza kwambiri mbiri yake pomwe kulephera kukadakhala chokhumudwitsa .Amafunika kuwonetsetsa kuti mbali yake ipambane! Pomwe anakumana ndi mwamuna uja ali ndi lupanga, amene ayenela kuti ndi Mngelo, Yoswa adafunsa funso mwabwinobwino,"kodi uli wa mbali yathu kapena wa mbali ya adani athu? "Kodi zomwe anaumana nazo mnthawiyi zitiphunzitsa ife chani ngati atsogoleri mu utumiki?

Atsogoleri mu utumiki amazindikira mbali yawo.

Yoswa anawona mmene zinaliri kuchokera Ku mbali yake.Ankafuna adziwe ngati munthu ameneyu anali wa kwaiye kapena otsutsana naye. "Ndiwe wa mbali yathu kapena ya adani athu? "Koma pokumana naye, anazindikira kuti pali mbali ina yomwe sanaiwone. Atsogoleri mu utumiki amazindikira kukhala Ku mbali ya Iwo okha  yoganizira potenga mbali. Amazindikira kuona dziko ndi funso uli, "Kodi muli a mbali ya masomphenya anga kapena  opikisana nane?" Koma kuchokera kwa Yoswa, Atsogoleri mu utumiki akuphunzira kufunika kosiya ndi  kuzindikira kuti palinso mbali zina!

Atsogoleri mu utumiki amavomereza mbali ya Mulungu.

Yoswa ayenera kuti anazizwa ndi kuyankha kwa mwamuna uja,"Ndilibe mbali"anayankha," Koma ngati olamula wankulu wa nkhondo ya Ambuye  ndabwera tsopano."Kuyankha uku kudasinthiratu zokambirana ndipo zidapangitsa kusintha mafunsidwe.Si lidalinso mmene lidaliri,funso la Yoswa lidasintha  kuchoka pa" Ndani ali wa mbali yanga?" kupita Ku "Kodi ndili Ku mbali yoyenera?" Mulungu akuitana atsogoleri mu utumiki kusintha mfundo zawo,osati  zokhoza kapena zolakwa, Koma kuti akulamula ndani? Zolinga za Ambuye  ndi zoposa zolinga zathu.Mbali ya Mulungu sikhala Ku mbali iliyonse ya mtsutsano wathu. Atsogoleri mu utumiki sasokoneza chowonadi Koma amazindikira kuti maonedwe awo ndi apafupi ndipo sangafane ndi a Mulungu monga momwe amaganizira poyamba!Atsogoleri mu utumiki sathetsa masomphenya awo, amangotengera masomphenya awo Ku cholinga chachikulu. Amazindikira kuti mbali yawo si yokakamiza anthu kukhala Ku mbali yawo, Koma kutengera aliyense Ku mbali ya Mulungu. Atsogoleri mu utumiki amazindikira kuti sangapambane nkhondo yoti anthu akhale Ku mbali yawo  mpaka atazitengera okha ku mbali ya Mulungu.

Atsogoleri mu utumiki amazichepetsa

Yoswa adagwetsa nkhope yake  pKupita mbali yatsopano ansi! Akadabwelera kwa anthu omwe aja ndi kupitiliza kuwatsogolera Ku nkhondo ya Ku Yeriko.Koma kowonedwe kake ka zinthu kasintha.Wazindikira kuti akutsogolera pa mbali ya Mulungu, osati kupempha Mulungu kukhala mbali yake. Akadatha kulamulabe, koma ngati  wokhala pansi pa ulamuliro. Sakadaitana anthu kukhala Ku"mbali yake", mmalo mwake akadaitana onse kukhala kumbali yake Ku mbali ya Mulungu. Atsogoleri mu utumiki amazichepetsa mu utsogoleri wawo kuti azindikire kuti Mulungu sali kumbali yawo; koma ali mbali ya Mulungu. Mozichepetsa amafunsa Mulungu kuti awatsogolere pa nkhani za kugawanika zomwe akukumana nazo ndi kuphunzila kuti kutenga mbali  si kochuluka kwa 'ife'ndi'awo'ngati chidwi chawo ndi cha pa Mulungu!

Zoti tilingalirepo ndi kukambirana:

  • Kodi ndi nyengo iti yomwe ndikukumana nayo nthawi ino yomwe ndi yogawanika kapena yomwe anthu akupatukana potsutsa? Muone nkhani imeneyi bwino pomwe mukuyankha mafunso otsatirawa.
  • Mu njira zanji zimene ndikuwona mwachibadwidwe kusiyana "mbali" kuchokera Ku mbali yanga kokha? Kodi ndachitapo chani msabata yangothayi zomwe zikufotokozera ichi? Kodi ndingapeze bwanji maonedwe olinganiza a" Mbali ina"ya zinthu.?
  • Mu nyengo imeneyi, kodi ndingaziwe bwanji kuti Mulungu ali kumbali yanga?kodi izi zibweretsa kusintha kotani kwa utsogoleri wanga?kodi nanga nditafunsa Mulungu ngati anali kumbali yanga pa nkhani imeneyi ndipo Wandiyankha,"Ndilibe mbali ,"anayankha, "Koma ngati Olamula  wa gulu la nkhondo la Ambuye ndabwera tsopano."? Kodi izi zingaumbe bwanji mmene ndingayankhile? kodi ndingachite mantha kuti chowonadi Chingapondelezedwe kapena ndingadalire Mulungu kuti amadziwa chowonadi chonse koposa ine
  • Kodi zikutanthaundauzanji  pa utsogoleri wanga " kugwa nkhope pansi"pa nkhani imeneyi? Pomwe ndabwelera ,kodi utsogoleri wanga ukasitha motani?

Mpaka nthawi Ina ,ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online