Gawo #293, July 19 , 2022

Yesu:Tsiliza Ntchito

Mu maphunziro anayi apita tawona momwe Yesu anawonetsela machitidwe a  Mtsogoleri  Muutumiki. Anafotokoza masomphenya; Anathamangira kwa Cholinga Chachikulu. Anakhazikitsa Ngodya kuti ophunzira ake  akweze Chotchinga. Anawonetsera mmene angamangile pa mphamvu momwe amawatuma awiri awiri. Mu izi,ndi njira zina zambiri, Yesu akuwonetsera njira yosiyana ya kutsogolera zomwe tiziwone mu machitidwe otsiliza, Malizitsa Ntchito.

1 Zitatha izi,Ambuye anasankha ena 72  ndikuwatumiza awiri awiri patsogolo pake Ku mudzi  uliwonse ndi malo omwe amafuna apite. 16 "Yemwe amvera inu amvera ine ;yemwe akana inu akana one;koma iye amene akana ine akana yemwe anandituma ine."17 Ophunzira 72 wo anabwelera ndichimwemwe  ndipo anati," Ambuye,ngakhale zimatigonjera mu dzina lanu." 18 Anayankha ,"Ndinawona Satana akugwa ngati mphenzi kuchokera kumwamba. 19  Ndakupatsani ulamuliro oponda pa njoka ndi zinkhanira ndikugonjetsa mphamvu zonse za m'daniyo;palibe chizakupwetekani.20 Komabe,musakondwere kuti mizimu imakugonjerani ,koma mukondwere kuti maina anu alembedwa mwamba."21 Pa nthawi imeneyi,Yesu odzala ndi chimwemwe cha mzimu,anati,"Ndikuyamikani, Atate,Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi,chifukwa mwabisa zinthu izi kwa anzeru ndi ophunzira ,ndi kuziwulura kwa ana amakanda.Inde,Atate,pakuti izi ndizomwe munasangalala kuzichita.(Luka10:1,16-21).

Tingaphunzirepo chani kuchokera Ku chitsanzo cha Yesu za momwe Yesu anamalizitsira ntchito?

Atsogoleri muutumiki amakuza anthu awo.

Yesu akadatha kupanga yekha ntchito yomwe anapatsa ophunzira ake.koma amafuna kuti Iwo akule  ndikukhala ndi mphamvu pawokha ngati atsogoleri.Anakhala akuwona iye akulalika,kuphunzitsa ,ndikuchiza.Tsopano,Iye amafuna kuti aphunzire kupanga pa Iwo okha.Anawatumikira powathandiza kuti akule.

Atsogoleri ena amawona gulu lawo  munjira yoti angowathandiza kukwaniritsa masomphenya.Atsogoleri muutumiki amaika maso awo masomphenya, koma pansipamtima wawo amapeza njira zokuzira wina aliyense wagulu lawo.Amaika chidwi chawo pa ogwira ntchito monganso amachitira  pa ntchito.

Atsogoleri muutumiki amapereka ulamuliro ndi udindo

Yesu anapereka ulamuliro ndi udindo kwa ophunzira ake. Anati,"Ndakupatsani ulamuliro.... "Yesu akadatha kusunga mphamvu zake zonse ndikuzigwiritsira ntchito Yekha.koma anachita mwadala kupereka idindo ndi ulamuliro wake kwa Otsatira ake.

Atsogoleri muutumiki salakalaka kusunga ulamuliro ndi udindo, amakhala ndi chilakolako pansi pa mtima wawo  kuti apereke kugulu lomwe akukuza.Amazindikira kuti izi sizimangothandizira gulu lawo kukula ndi kutukuka  komanso amakonzekeretsa magulu awo  za mtsogolo.

Atsogoleri muutumiki amakonzekera kupambana kwamtsogolo

Yesu samangotumiza kokha gulu lake pa ntchito yanthawi yomweyo.Amapanga mwadala  ndi mwandondomeko ,kuwakonzekeretsa kuzatsogolera iye atapita. Anali ndi cholinga chomwe chimafunika kutula ntchito  kwa ena  omwe amatsatira. Ndipo anali "odzala ndi chimwemwe" mmene amawona zikutheka!

Atsogoleri ambiri amalimbika kugwira ntchito kuti zolinga zawo zikwaniritsidwe koma osaganizira kwenikweni zomwe zizachitike pamene Iwo apita.Atsogoleri muutumiki amayamba ndikuchoka kwawo pamtima pawo  ndipo amamanga magulu omwe azapitilize kuti cholinga chawo chachikulu chizapite patali mtsogolo.

Yesu akuwonetsa atsogoleri kulikonse mmwene  machitidwe a utsogoleri angasinthire.Ndipo akuwonetsera kuti Utsogoleri Muutumiki umatheka ndithu- - Gulu Lake likupitirizabe  cholinga chake zaka 2000 zakwana pano!

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

Zoti tilingalirepo ndikukambirana

  • Werengani ndime yonse pomwe Yesu akutuma ophunzira ake 72 pa Luka 10:1-24. Lingalirani pa zomwe amachita ngati mtsogoleri nde momwe zikuwonetsera kumalizitsa kwa ntchito yake.
  • Kodi ndikuchitapo chani kuti anthu anga ndiwakuze? Kodi ndingachitenso chani kuti ndikuze kuthekera kwa utsogoleri  mwa Iwo?
  • Munjira iti yomwe ndingapereke ulamuliro ndi  udindo kwa wina wa mugulu langa?Kodi ndingachite liti zimenezi?Kodi ndiwauze motani kuti amvetsetse? Kodi ndingathawandizire motani?
  • Kodi ndikukonzekeretsa motani gulu langa  kuti lizachitebwino ine ndikapita?Kodi dongosolo la ozalowammalo liri bwino kwa ine ndi ena? Kapena ndikufunika ndikonzebe mwabwino? Kodi ndikufunika ndichitechani kuti zizandibweletsele chimwemwe chomwe Yesu analinacho pomwe amawona ophunzira ake akupambana?

Mpaka nthawi ina,ine wanu paulendo,

Jon Byler

 

Muphunziro lotsatirali ,tiyamba phunziro latsopano. Maganizo anu nthawi zonse ndiolandiridwa pa mitu yomwe yakukondwetetsani!

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online