Gawo #292, July 6, 2022

Manga pa mphamvu

Mu phunziro lapitali tinawona momwe Yesu anapelekera chitsanzo chachitatu mu Chitsanzo Cha Mtsogoleri Otumikira,mmene anawalambulira njira.Anathandizira  kupambana pofotokoza kuti chipambano ndi chani  ndikuchotsa zophinja mwa Iwo.Yesu analinso  kadaulo  pomanga gulu.Pomwe amatuma ophunzira ake,mwadaladala anakweza mphamvu za wina aliyense wa

  iwo ndipo akupereka chitsanzo   cha mmene anachitira, Manga pa Mphamvu.

 1 Zitatha izi Ambuye adasankha wena 72 ndi

ndikuwatumiza awiri awiri  patsogolo pa iye  Ku mudzi uliwonse  ndi kumalo  komwe iye amafuna kupita.2 Adawauza , " kholora ndi lalikulu,koma antchito ndi ochepa.Pemphani Ambuye wa Kholola , kotero,kuti atumize anchito ku munda wake wakholora.3 Pitani! Ndikukutumani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu.

4 Musatenge chikwama kapena nsapato;ndipo musapereke moni kwa wina aliyense panjira.

17  Ophunzira 72 wo anabwera ndi  chimwemwe  ndikuti ,"Ambuye, ngakhale ziwanda zimatigonjera mu dzina lanu."18 Iye anayankha ," Ndinawona satana akugwa ngati mphenzi  kuchoka kumwamba.19  Ndakupatsani ulamuliro   oponda pa njoka ndi

 zinkhanira  ndi kugonjetsa  mphamvu za m'daniyo ;palibe chomwe chizakupwetekani.20 Komabe, musakondwere chifukwa ziwanda zimakugonjerani,koma kondwerani kuti Maina anu alembedwa mmwamba."(Luka 10:1-4,17-20).

Pongowona chabe mmene nkhaniyi iliri ,zikuwonetsa kuti Yesu  amangokwaniritsatu  ntchito kudzera mwa ena. Koma tiyeni tiwonetsetse  bwino pa momwe amamangira gulu Lake  pogwiritsa ntchito mphamvu za wina aliyense payekha.

*Atsogoleri Muutumiki amazindikura kufunika kogwirantchito  ngati gulu.*

Yesu anawatumiza ophunzira ake awiri awiri, osati yekha yekha.Yesu akadatha kuwatuma aliyense payekha payekha  72 kudela lake lake koma anasankha kumanga pa mphamvu  popanga magulu 36.Anazindikira kuti kubweretsa anthu awiri pamodzi kuti akwaniritse cholinga sikunali kutaya nthawi ndi mphamvu koma kuchulukitsa kwa mphamvu .Mphatso zosiyana ndi kuthekera kwa aliyense kukanakathandizidwa ndi nzake. Wina wa iwo  akanatha mwachangu kupsya mtima  pokambirana ndi wachilendo  pomwe  wina amatha mwabwino kufotokozera za cholinga chawo.wina atha kukhala wamphamvu popanga maubale ndi wanthu  pomwe wina atha kukhala ndi luso lakafikiridwe pa munthu. Yesu mwadala anasankha magulu amene akadafikitsa  pamwamba mphamvu za omwe Adawaitana.

Atsogoleri muutumiki  zindikirani mphamvu za wina aliyense zomwe zimagwirantchito bwino pogwirana manja ndi ena.Atsogoleri muutimiki amazindikira kuti  pa iwo okha sangakhale ndi mphamvu zonse ,koma atha kumanga gulu lomwe ndilokwanabwino ndi mphamvu zosiyana siyana.Amazindikira kuti kugwirantchito  ngati gulu kumapangitsa maloto kutheka.

*Atsogoleri muutumiki amagwirizanitsa mphamvu ndi ntchito ya gulu.

Pomwe Yesu amatuma ophunzira ake awiri awiri, anali ndi kumetsetsabwino kuti anali ndi ntchito pa cholinga Chake.Amayenera kukaphunzitsa ndi kuchiza .Amakonza njira ya Yesu.Anawalangiza kuti asakawonongeke ndi zinthu zabwino monga malonje kwa wanthu mkati mwanjira !Anazindikira kuti kuwakuma ngati magulu ndi mphamvu zosiyana zikakwaniritsa cholinga chawo chachikulu kwambirikwake. Wina angathe kuwonongeka popereka moni kwa munthu panjira koma nzawo alinaye limodzi atha kubwenzeletsa chidwi chawo pa cholinga chawo.

Atsogoleri muutumiki amaphunzira kudziwa mphamvu za gulu lawo. Kenaka,mwadaladala ndi motsatanjira amagwira ntchito yogwirizanitsa  gulu lawo ndi mphamvu za wina aliyense payekha payekha kuti cholinga chikwaniritsidwe.

*Atsogoleri muutumiki amalimbikitsa  kukula kopitilira  ndi  kutukuka kwa gulu lawo*

Pomwe ophunzira ake adabwera atachitabwino pa cholinga  anadzala ndi chimwemwe.Yesu anali othokoza

chifukwa cha kukwanilitsaku,koma mwachangu akuyamba kuwathandiza    kuti akhale ndi kuona kwabwino.Akuchotsa maso awo  Ku kuchitabwino kwapano  kuwatengera Ku cholinga chapamwamba.Yesu akuikiza mwa iwo kukula kopitilira.Chidwi Chake chili pa kukonzekeretsa gulu kuti lizatenge ntchito akazachoka.Anawapatsa chochita chimodzi chowakonzekeretsa iwo Ku ntchito zikuluzikulu.Monga Yesu,atsogoleri

 muutumiki amaganizira za tsogolo ndikupitiriza  kuikiza mu kukula ndi kutukuka  kwa gulu lawo.Atsogoleri muutumiki sachitamantha  ndi kupita mtsogolo kwa ena,amalimbikiza ichi!Amazindikira kuti palibe chipambano popanda alowammalo. Amathandiza magulu awo kumanga pa mphamvu za munthu aliyense kuti  kuchitabwino kwa mtsogolo kuzakhale kwakukulu koposa zipambano za tsopano.

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • werengani ndime yonse pomwe Yesu amatuma ophunzira ake 72 pa Luka 10:1-24.Lingalirani pa zomwe iye amachita ngati mtsogoleri ndi mmene zinawonetsera kumanga pa mphamvu.
  • Kodi ndi zitsanzo zowonjezera ziti zochokera mmoyo wa Yesu zomwe mungaganizire zomwe zikuwonetsera kuthekera Kwake komanga pa mphamvu?
  • mu utsogoleri wanga ,kodi cholinga ndichopereka ntchito kwa aliyense payekha payekha kapena pa gulu.? Ndikapanga magulu ,kodi ndimawunika mphamvu zomwe zikufunika pa ntchitoyo  nditatero ndikuwatuma anthu potengera zomwe ndapeza?
  • Kodi ndimazindikira  mphamvu zanga ndi zifooko zanga ndipo mwadala ndimabweretsa ondizungulira kuti andithandizile mmadera a kufooka kwanga?ngati sichoncho,ndichifukwa chani nanga ndichite chani musabata ino kuti ndisinthe?Ngati ndichoncho,kodi zakhudza motani utsogoleri wanga nanga zakhudza bwanji omwe ndimawatsogolera?
  • Kodi ndikukuza gulu langa kuti lingokwaniritsa cholinga kapena ndikulikonzekeretsa kutengamalo pomwe utsogoleri wanga watsilizika.Kodi chitsanzo cha Yesu chikupambana kuganiza kwanga za chipambano chamtsogolo.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2021

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online