Muphunziro lapitali tinaona chachiwiri cha chitsanzo cha mtsogoleri otumikira,ndinso,tinaona mmene Yesu anafotokozera momveka bwino ngodya za utumiki kwa ophunzira ake, mmene chipambano chawo chikachokere.
8" mukalowa mmudzi ndipo mwalandiridwa ,idyani chakudya chomwe mwapatsidwa.9 chizani odwala omwe alipo ndikuwauza kuti,"ufumu wa Mulungu wayandikira.10 koma mukalowa mmudzi ndipo simunalandiridwe,pitani mmisewu mwake ndikuti,11 Ngakhale fumbi la mmudzi mwanu tikulitsatsa kumapazi athu ngati chenjezo kwa inu.Koma mudziwe ichi :ufumu wa Mulungu wayandikira16 iye amene amvera inu amveranso ine ;koma iye okana ine akananso yemwe anandituma ."17Ophunzira 72 wo anabwelera ndi chimwemwe ndikuti," Ambuye ,ngakhale ziwanda zimagonjera kwa ife mu dzina lanu."18 Anayankha Iwo nati, ndinaona satana akugwa ngati mphenzi kuchokera kumwamba.19 ndakupatsani ulamuliro oponda pa zinkhanira ndi njoka ndikugonjetsa mphamvu zonse za m'daniyo;ndipo palibe chomwe chizakuonongani ,20 Komabe musakondwere kuti ziwanda zimakugonjerani koma kondwerani kuti maina anu alembedwa kumwamba."( Luka 10:16-24)
Yesu anafotokoza momveka bwino kuti chipambano cha ophunzira ake chikachokera pati.Anawaphunzitsa kuti akakhale opambana ndikuchotsa zotchinga zomwe zikanalepheretsa kupambana kwawo.Analambula njira kwa otsatira ake ndikuwawonetsera atsogoleri mu utumiki kuchita chimodzimodzi.
**Atsogoleri mu utumiki amafotokoza mwabwino chipambano pakulumikizana
Yesu anatuma gulu lake ndikulifotokozera momveka bwino njira yomwe chipambano chawo chikabwelere.Cholingachawo chinali kukalarikira uthenga omwe anawapatsa.Ndikuti chipambano chawo chikalumikizika Ku cholinga chachikulu kapena Ku masomphenya omwe anagawana nawo, Antchito awumbika kuchoka Ku "munda wakholola" Tsopano akulumikiza chipambano chawo Ku kukwaniritsa cholinga chachikulu.Akuwafotokozera bwino kuti ena akalandira uthenga wawo ndipo ena akawukana.Chipambano chawo sichidachokere kuzimenezi .Pomwe anabwelako Ku ntchito zawo ,Iwo anazipatsa chipambano kuchokera pa zozizwa adachita,Yesu akuwakumbutsa kuti kupambana kwawo kukulumikizika poti maina awo alembedwa kumwamba.
Atsogoleri muutumiki amapeza njira yofotokoza momvekabwino njira yomwe chipambano cha gulu lawo chikachokere.kaya kuchoka ku zomwe agulitsa,miyoyo yomwe yasinthika,makasitomala ,kapena opezeka pa msonkhano atsopano.Mulimonse mmene mulingo wa chipambano ungakachokere ,atsogoleri muutumiki amafotokoza bwino kuti chipambano ndichani ndipo sichani! Ndipo nthawi zonse amalumikiza chipambano Ku cholinga chachikulu.
*Atsogoleri mu utumiki amawunikira chipambano pophunzitsa*
Yesu sadangotambasula bwino mmene chipambano chikachokere, anaperekanso chiphunzitso chowoneka kwa gulu lake zomwe zidawathandiza kuti akachitebwino.
Anawapatsa malangizo a uthenga omwe amati akalalike ndi kuwapatsa malangizo apadeladela .Cholinga chake chidali choti akapambane ndipo anawawunikila.
Atsogoleri muutumiki perekani maphunziro ndi kuwunikira zomwe zikufunika kuti gulu lawo lifikire chipambano. Amatumikira ena pophunzitsa zomwe zimakonzekeretsa gulu lawo kufikira pa chipambano.
**Atsogoleri muutumiki amaika ndandanda chipambano pochotsa chiphinjo.*
Yesu anadziwa kuti padzakhala mabvuto pa njira yawo ya chipambano. Kotero ,anachotsa chiphinjo cha kukanidwa powawuza ophunzira kuti aziyembekezere!Anawa chophinja cha kuzikuza pomwe anabwelera odzala ndichimwemwe pa zomwe anachita .Anawakumbutsa kuti chipambano chawo sichidachokere pa zomwe zidachitika koma pa ubale wawo ndi Iye.
Atsogoleri muutumiki amawona vuto pagulu lawo ndikulichotsa.Amapeza njira zothandiza kuthana ndi zophinja zosayembekezeka pakutero gulu lawo litha litha kupambana.
Atsogoleri muutumiki amazindikira kwawo kumabwera pomwe omwe akuwatsogolera apambana.Ndipo amaika chidwi chawo pofotokozabwino mmene chipambano chawo chikachokere ndipo amawaphunzitsa ndi kuwawunikira Ku chipambano.Amalambula njira! |