Gawo #290, June 08, 2022

Yesu anakwezera chotchinga mmene amatuma ophunzira ake.

Mu phunziro lapitali tinaona choyamba cha Mmene mtumiki Otumikira Amachitira, Thamangirani  Ku Cholinga Chachikulu,chomwe chimakhudzana ndi masomphenya athu kapena chifukwa chomwe tikutsogolera.Powonjezera ,atsogoleri achitabwino amakweza chotchinga kwa omwe akutsatira pozindikila ngodya zomwe zimatsogolera ntchito yawo.Amaitana wina aliyense kuti azichita munjila zolingana ndi  ngodyazo.Yesu anachita chimodzimodzi ndi ophunzira ake pomwe anawatuma.

3 Mukani;taonani,ine ndatuma inu ngati ana a nkhosa pakati pa mimbulu. 4 Musanyamule thumba la kamba ,kapena nsapato;ni musalankhule munthu panjira. 5Ndipo munyumba iri yonse mukalowamo muthange mwanena ,mtendere ukhale mnyumba iyi. 6 Ndipo mukakhala mwana wamtendere mmenemo,mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe,adzabwera kwa inu. 7 Ndipo mnyumba momwemo khalani ,ndikudya ndikumwa za kwawo; pakuti wantchito ayenera  mphotho  yache ;musachokachoka mnyumba .8 Ndipo mmudzi uliwonse mukalowamo ,ndipo alandira inu,idyani zomwezo akupatsani; 9 ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nawo ,Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma kumudzi uliwonse mukalowamo, 10 ndipo salandira inu ,mmene mwatuluka ku makhwalala ache nenani, 11 likhale fumbi lochokera kumudzi kwanu, lomamatika kumapazi athu tilisansira pa inu,koma zindikirani ichi,kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.12 Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo Ku Sodoma kudzapitilira kuposa mudzi umenewo.( Luka 10:3-12)

Pamenepa Yesu akuonetsela mchitidwe wachiwiri ,Kweza Chotchinga,podziwa ngodya zofunika zomwe Yesu amafuna kuikiza mwa ophunzira ake, Atsogoleri mu Utumiki phunzirani kuchokera Ku chitsanzo cha Yesu momwe ngodya zimaumbira utsogoleri wawo.

Ngodya zimaumba  njira za ntchito yathu.

Yesu anapereka ndondomeko  za malangizo a mmene ophunzira amayenera kuyendera,"musatenge ziwama kapena nsapato;ndipo musapatse moni aliyense munjira ....musayendeyende kuchoka mnyumba ina kupita nyumba ina. "Anawaitana kutenga zinthu mophweka,kuti chidwi chawo chikhale pa ntchito yawo basi,ndipo kuti akhale akhale pa cholinga chawo.Pomwe amapereka malangizowa ,amagawana nawo ngodya zofunika kwa Iye.Akanati agwiritse ntchito njila yina kuti ophunzira ake atsatile akanati," Timafuna moyo osalimbana ndizambili,wachindunji,ndi wakhazikika pa cholinga."

Masomphenya kapena cholinga chachikulu chimaonetsera chifukwa chomwe timatsogolera pomwe ngodya zimaonetsera momwe timatsogolera.Atsogoeri otumikira z amadziwa ndi kufotokoza  ngodya  zofunika kwa magulu awo.Amayikamo gulu ngati mbali ya ndondomekoyi ,koma sapereka ntchito kufotokozera kuti ngodya zofunika kwambiri ndiziti.

Ngodya zimaumba uthenga wa ntchito yathu

Yesu anafotokoza bwino za uthenga omwe ankafuna ophunzira ake atenge ku midzi yomwe amapita.Anawaitana iwo kuti akalalike uthenga,"ufumu wa Mulungu wafika pafupi nanu ."uwu unali uthenga womwe ukanathandiza kukwaniritsa cholinga chachikulu.Yesu ankafuna otsatira ake agawe uthenga omwe umagwirizana ndi  ndondomeko za  ngodya zawo.Ndandanda uwu  unalora ophunzira kukalalika molingana ndi mmene anauzidwira.

Atsogoleri mu  utumiki amagwira ntchito molimbika kuwonetsetsa kuti  uthenga  mu ngodya zawo waperekedwa momveka bwino  ndi mwapafupi pafupi kwa bungwe lonse.Amapanga kauniuni   pafupipafupi kuwonetsetsa kuti uthenga, ndondomekoza ngodya zawo ndi cholinga chachikulu sizikuthawana kwenikweni.

Ngodya zimaumba zitsanzo kwa ntchito yathu.

Yesu akupereka zitsanzo za anthu a mitundu iwiri omwe akalandire ophunzira ake--- wina anawalandira ,ndipo wina adawakana.Ndichifukwa chani Yesu anapereka zitsanzo izi?Ankafuna kulimbikitsa ngodya zake munkhani zomwe anafotokoza ndi zitsanzo adaperekazo.Ankafuna ophunzira ake amvetsetse momwe ngodya zawo zingakakhalire mowonamtima  ndi zomwe angakachitire  kuti akakhale okhulupirika ku ngodya zawo.

Atsogoleri muutumiki mosamalitsa amasankha zitsanzo zawo.Amagawana nkhani ndi kuzindikira makhalidwe pa gulu  lawo omwe sasiyana ndi ngodya zawo.Pomwe apeza kusiyana,amakonza ndi kupereka uphungu kuti abweretse kugwirizana ndi ndondomeko za ngodya zawo. Amakweza pamwamba cholinga pofotokoza momvekabwino ndi kugwiritsa ntchito ngodya zawo.

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • Werengani nkhani yonse ya Yesu Atumiza ophunzira ake 72 pa Luka 10:1-24. Onani mmene ankachitira ngati mtsogoleri ndi momwe zimaonetsera  ngodya zomwe Yesu amafuna ophunzira ake atsatire.
  • Kodi bungwe lanu liri ndi ngodya zofotokozedwa bwino?ngati sichoncho ,tengani kanthawi kulingalira za mmene angakhalire ndi kupanga dongosolo lobweretsa atsogoleri apamwamba mu dongosolori.Ngati muli ndi ngodya zofotokozegwa kale mwandondomeko,kodi ndi zomveka bwino kwa aliyense mu bungwemo?kodi china chomwe chingachitike  ndichani powonetsetsa kuti aliyense  akumvetsetsa ndikutsatira  ngodyazi?
  • Kodi mufotokoza nkhani zomwe zimathandiza anthu kumvetsetsa  ngodya zomwe mulinazo?
  • Kodi mumapanga kauniuni pa otsatira anu ngati akutsatira ngodya zomwe mumapereka ?munjira zanji zomwe mungachitire izi motsindika kambiri?
  • Pakakhala kusiyana pakati pa ndandanda wa ngodya zanu ndi mmene otsatira anu akukhalira ,kodi mumalankhula motani  kuti mubweretse kulingana?Ngati pali ena mugulu lanu omwe akupanga zosiyana ndi ngodya zanu,kodi zimasokoneza motani kuthekera kwanu kukwaniritsa cholinga chanu chachikulu?

Mu mutu otsatirawu ,tiwunika mmene Yesu anakwezela  malire pomwe ankatuma ophunzira Ake.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online