Yesu anaphunzitsa ndikuwonetsela utsogoleri omwe unali osiyana mu nthawi yake ndipo omwe ukupitiliza kubetchela ndi kusintha miyanda miyanda ya atsogoleri kwa zaka zokwana 2000 zotsatila.Utsogoleri wa Yesu ndi chitsanzo chathu cha utsogoleri otumikira.Mu mutu uwu tiwona mmene Yesu anawonetsera zithu zisanu mwadala pomwe ankatuma ophunzira ake 72 mu Luka 10:1-24.Atsogoleri muutumiki phunzirani kwa iye ndipo tsatirani njira zisanuzi zomwe zimapanga maziko a Chitsanzo Cha Mtsogoleri Otumikira.Choyamba chomwe Yesu anawonetsera ndi Kuthamangira Ku Cholinga Chachikulu.
1 Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndikuwatumiza iwo awiri awiri Ku mzinda uliwonse umene iye amafuna kupitako.
2 Anati kwa iwo,"Zokolora ndi zambiri,koma antchito ndi opelewera.Pemphani Ambuye wa Zokolora ,kotero,kuti atumize antchito Ku munda wake wakholora.(Luka 10:1-24).
Yesu amafuna kutumiza ogwira ntchito 72 ndipo anali ndi cholinga chowonekeratu.Koma asanawatume ,anafotokozeratu monveka bwino masomphenya kapena
Chomwe tikutcha cholinga chachikulu.Atsogoleri Otumikira phunzirani mphamvu ya cholinga chachikulu kuchokera pa chitsanzo chake.
Cholinga chachikulu chimawonetsera chitsogozo.
Yesu anawauza ophunzira ake kuti apite mmadera ndi mmalo omwe iye amafuna awayendele.Mau ake anapereka chitsogozo kwa iwo.Sadangoziwa komwe amafuna kuti apite;komanso adadziwa komwe samayenera kupita!Cholinga chachikulu chimaonetsera chitsogozo. Atsogoleri ena amauza wanthu kuti apange ntchito koma samawalumikiza ku ntchito za Ku cholinga chachikulu.
Atsogoleri Otumikira fotokozerani cholinga chachikulu kuti chithandize otsatira Ku chindunji cha komwe akupita.Amaunika zochitika zonse powona mmene akutengera bungwe Ku cholinga chachikulu.
Cholinga chachikulu chimatsimikizira tanthauzo
Yesu anapempha ophunzira ake kuti atsogole Ku maderawa.Koma kupita kwawo kunali "kokonzekera kholora" lomwe limabwera.Yesu mosamala anawadziwitsa Iwo kuti zomwe amachita zinali zokonzekera
chinachake chachikulu ndichofunika kwambiri.Anapereka tanthauzo la ntchito yawo.Atsogoleri ambiri amangowona ngati otsatira amangofuna ka mnunsu kapena mutu wa chinthu kuti azigwira ntchito. Koma Yesu akukumbutsa atsogoleri onse mu utumiki anthu amafuna adziwe kuti ntchito yawo ili ndi tanthauzo komanso cholinga chopambana mwaiwo wokha.Atsogoleri muutumiki amathandiza wanthu kuti awone mmene machitidwe awo angatsogolere ku kukwaniritsa cholinga chachikulu.
Cholinga chachikulu chimathandizira kuzipereka
Yesu sadangotsegula maso awo ku cholinga chomvekabwino cha ntchito amawauza kuti ayigwireyo,komanso anawaitanira ku kuganiza kopapyola ntchitoyo kwa tsiku limenero.Anawaitanira ku kupemphelera antchito ambiri!Cholinga chachikulu chimatakasa kuzipereka kuchokera kwa ena.Pomwe akuvomereza masomphenya ngati awo,amayamba kutenga cholinga kukhala chawo ndikuitana ena kupanga nawo zomwe akuchita.Amathandiza nawo mtsogoleri ngati eni masomphenya. Pa ichi amakhala ozipereka kwatunthu ku cholinga chachikulu ndipo amakhala ofuna kuchita zonse zofunika kuti zichitike kuti zikwaniritse ntchito.
Atsogoleri muutumiki amatsogolera bwino pomwe akutsatira chitsanzo cha Yesu.amafotokoza momveka bwino cholinga chachikulu cha bungwe lawo ndi kusunga mwapamwamba masomphenyawa nthawi zonse kwa anthu omwe akuwatumikira.Amamangikira ntchito iliyonse ndi kuzipereka kwawo ku cholinga chachikulu ndipo pakupanga izi amapereka tanthauzo ndi cholinga kwa aliyense.Amagwira ntchito molimbika kuti awonetsetse munthu aliyense mu bungwemo,kuyambira wapamwamba mpaka wapansi ,amvetsetse kuti ali nawo mugulu lomwe likubweretsa kusintha.Limeneli ndiye gulu lomwe tonse tikufuna tikhalemo ndipo ndi moteromo momwe Yesu anatsogolera gulu lake! |