Gawo #287, April 13, 2022

ABC pa Chiyambi Chabwino: Khulupilirani mu Malonjezo A Mulungu

Monga tawonera mu phunziro lapitali,Yoswa anayamba bwino mu udindo wake watsopno pozindikira zenizeni zake mu nyengo yake.Atangoyambapo ananva  Mulungu akumupatsa malonjezo angapo.

5 Palibe yemwe azaima kutsutsana nawe masiku onse a moyo wako.Monga ndinali ndi Mose,ndizakhalanso ndi iwe;sindizakusiya kapena kukutaya.6 Khala wamphamvu ndi olomba mtima, chifukwa uzatsogolera anthu awa  kukatenga cholowa chomwe ndinalumbilira malolo awo kuwapatsa.7 Khala wamphamvu  ndi olimba mtima kwambiri.Samalira ndimvera malamulo onse omwe mtumiki wanga Mose anakupatsa;usaaapatukile Ku dzanja lamanja kapena Ku lamanzere,kuti ukakhale ochitabwino kulikonse uzapite.8 Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako;ulingalilemo usana ndi usiku,kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo,popeza ukatero uzakometsa njira yako nuzachita mwanzeru.9 Kodi sindinakulamulire?Khala wamphamvu ndi olimba mtima. Usachite mantha;usagwe mphwayi,pakuti Ambuye Mulungu wako azakhala nawe kulikonse uzapite."(Yoswa 1:5-9)

Pa chiyambi cha ulendo wa utsogoleri wake anamva ndi kukhulupilira malonjezowa omwe azakhale maziko Ku mchitidwe wake wa  utsogoleri. Mulungu anapereka malonjezo atatu omwe atsogoleri onse otumikira akufunika kutsamilapo,onsati kungoyambirapo ulendo Wawo,komanso  kupitiliza bwino.

Mulungu walonjeza kupezeka Kwake

"Ndizakhala nawe ; sindizakusiya kapena kukutaya." Mulungu analonjeza Yoswa kuti pa chilichonse chochitika kwa iye ngati mtsogoleri,Mulungu azakhala naye.Atsogoleri amapanga zisankho zovuta  ndipo amanyamula zothodwetsa pozindikila kuti zisankho zawo zimakhuza onse amene ali pansi pa utsogoleri wawo.Nthawi zina pamakhala zisankho zomwe zimafunika kuti apange zomwe sizingakhale zovomelezeka  ndi omwe akuwatsogolera.Kukula ndi  kulemela kwa maudindo amenewa kungapangitse mtsogoleri kunva undekha.Koma Mulungu analonjeza Yoswa kuti mu nyengo iliyonse, sazakhala yekha,adzakhala ndi kupezeka kwa Mulungu pamodzi naye.Atsogoleri mu utumiki amazindikira kuti amafunika kukhala ndi kotenga nzelu ndi kumvetsetsa makamaka pamene akulowa mu milingo yatsopano ya maudindo ndi kukumana ndi zobetchela zosayembekezeka.  Atsogoleri otumikira amadalira kupezeka kwa Mulungu kuwapatsa nzeru za zobetchela pa utsogoleri. Kupezeka kwake kumapatsa Atsogoleri otumikira ubwino wosasimbika!

Mulungu walonjeza mphanvu Yake.

Katatu mu mavesi awa Mulungu akuuza Yoswa kuti, "Khala wamphamvu ndi olimba mtima" Yoswa amafunikira mphamvu ndi kulumba za ntchitoyake yatsopano.Amafunika atsogolere anthu kulowa mu dziko latsopano  ndipo kumeneko kukakhala kukumana ndi nkhondo kutsogolokwawo.Utsogoleri umafunikira mphanvu.Yoswa amafunikira kuchita mbali yake,koma zinali zosakwanira.Pomwe akuyamba udindo wake, amafunikira kuzindikira kuti sakachitabwino  chifukwa cha kupambana kwake kapena  kuchitabwino kwa mbuyo.Amafunikira mphanvu zoonjezera  zomwe Mulungu analonjeza. Kotero, Mulungu

anamukumbutsa dziko lomwe anatsala pang'ono kulilanda linalonjezedwa ndi Mulungu ndipo Mulungu akapereka mphanvu yake kuthandizira Yoswa kuti akwanilitse ntchitoyo.Cholingacho ndi Chake Mulungu! Atsogoleri Mu utumiki  landirani maphunziro ndipo muphunzire kuchoka mu kuwerenga mabuku ndi njira zina zopambana.Amalimbika kuchita chilichonse chimene angathe .Komanso  moyamika amakhulupilira kuti Mulungu walonjeza kwa Iwo zofunikira kuti akachitire zomwe Mulungu anawaitanira kuti akachite.

Mulungu walonjeza Zolinga zake.

Mulungu amayembekezela Yoswa kutsogolera bwino,koma anatsimikiziranso Yoswa za zolinga zake.Poyamba akumupatsa Yoswa malangizo oti atsatire payekha,kuti asamalire kuchita kumvera malamulo a Mulungu akatero"azapambana nazachita bwino."Mulungu patsogolo pake akanaonjezelaponso zina  pa  malingaliro ake koma pomwe Yoswa wayambapo,otsatira ake anali maziko.Atsogoleri mu utumiki samangowona za malingaliro awo ;amafunafuna kutzatira zolinga za Mulungu. Amakhulupilira kuti zolinga za Mulungu ndizapamwamba ndi zofunika kwambiri kuposa zomwe angakhale nazo Iwo eni.

Yoswa anayamba bwino pokhulupilira malonjezo omwe Mulungu anamupatsa. Atsogoleri mu utumiki pangani chimodzimodzi.

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

(Ngati musali pa udindo watsopano munthawi ino,muone momwe mafunso awa akukhudzila pa malo pomwe mukutumikira pano.)

  • Mu nyengo ya utsogoleri wanga nthawi ino,kodi Mulungu ndikumamumva bwinobwino motani kupezeka kwake?Kodi pali kusiyana kwanji mu njira yomwe ndikutsogolera?Kodi pali zinthu zomwe ndikufunika ndichite pochulukitsa chidziwitso changa cha kupezeka Kwake mu ntchito zanga za tsiku ndi tsiku?
  • .Kodi ndi munjira iti yomwe ndikusowekera mphamvu msangamsanga mu utsogoleri wanga?Kodi ndikufuna kungodalira pa mphamvu zanga zokha  kapena ndimafuna kawirikawiri kudalira mphamvu ya Mulungu mu utsogoleri wanga?
  • Mulungu analamura Yoswa, "sunga buku ili lachilamulo lisachoke pakamwa pako;koma ulingaliremo usana ndi  usiku ,kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo." Ndi munjira iti yomwe ndimachita izi mu utsogoleri wangawu?Kodi pali kusintha komwe ndikuyenera kuchita potsatira chitsanzo cha Yoswa?
  • Kodi cholinga mu utsogoleri wangawu ndaika choyambilira zolinga zanga kapena

 

Ndinazindkira ndikuika  ndondomeko za Mulungu?Munjira iti yomwe Mulungu akundiitanira kumaphunziro ozindikira za zolinga zake za utsogoleri wanga?

Mu phunziro lotsatira,tionapo mmene atsogoleri mu utumiki amayambira bwino polumikizana ndi anthu.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online