Mu phunziro lapitali tinaphunzila kwa Mose mmene atsogoleri otumikira amasinthana udindo mwabwino.Tsopano tiyeni tione mbali ina ya ndondomeko,chiyambi cha ntchito yatsopano ya Yoswa,olowa mmalo mwake.
Atsogoleri onse azakumana ndi nthawi pomwe alowa mu malo atsopano a udindo wa utsogoleri kapena kusintha kulowa Ku bungwe latsopano kapena gulu latsopano.
Kodi zimakhala bwanji kuti chiyambi chikhale
Chabwino?Mu phunziro lino tiona za
Zilembo za ABC pa chiyambi chabwino cha Yoswa:Zindikilani zenizeni,Khulupilirani mu malonjezo a Mulungu komanso lumikizanani ndi anthu.
Atsogoleri nthawi zambiri amayamba udindo wawo ndi zoyembekezeka zomwe sizenizeni.Akhoza kuyembekezera kuti udindo atengawo ndi mbambande palibenso kapena atha kukhala ndi chikaiko za lithe let's kwawo pa ntchitoyo.Mu zonsezi atsogoleri otumikira amafunika kuti azindikire zenizeni monga Yoswa anachitira.
1 Mose atamwalira mtumiki was Ambuye,Ambuye ananena kwa Yoswa mwana wa Nuni,ophunzira wa Mose;2 "Mose mtumiki wanga wafa.Tsopano,iwe ndi anthu onse awa,konzekani kuwoloka ntsinje wa Yerodani Ku malo amane ndikuwapereka posachedwapa_kwa a Israeli. 3 ndizakupatsa malo aliwonse lizaponde phazi lako,monga ndinalonjezera Mose.(Yoswa 1:1_3).
Zindikilani nthawi yakale
Yoswa atangofika pa udindo wake watsopano.chinthu choyambilira chomwe Mulungu akumulankhula mu udindo wake watsopano ndi kuzindikira zakale.,"Mose mtumiki wanga wafa." Lingalirani pamenepa kwakanthawi.Ndimau asanu omveka bwino Mulungu akuzindira mtsogoleri wamphamvu yemwe analipo Yoswa asanalowepo.Mose anayenda pa nyanja yofiira ndi kukumana ndi Mulungu pa phiri la Sinai!Zinali zovuta kwa Yoswa kuyenda mofanana ndi Mose.Mulungu sanafune Yoswa kapena atsogoleri otumikira kusalabadira za muthawi yakale pomwe akuyamba ntchito yawo yatsopano.
Atsogoleri otumikira amazindikira kale lawolawo.Amabweretsa mbiri yawo yakale mu udindo wawo watsopano. Amazindikira zomwe anaphunzira nthawi yakale kuchokera mu zolakwitsa zawo kapena zipambano zawo.
Atsogoleri otumikira amazindikiranso kale lomwe ndi la bungwe lomwe akulowamo.Amakhala ofuna kubwetetsa mphatso zawo ndi maitanidwe awo mu udindo wawo watsopano ndi kubwetetsa popitilizira.Amafunafuna kuphunzira za momwe wachokayo amagwilira ntchito ndiponso ndichifukwa chani amatsogolera moteromo.Amalankhula mwaulemu molemekeza omwe analipo iwo asanabwelepo posatengera kupambana kapena kulephera.Atsogoleri otumikira amazindikira ndi kuphunzira kuchoka mu kale koma samakhazikika mu kalemo.
Zindikilani nthawi yatsopano Mulungu amayenda mwachangu kuchokera mu nthawi yakale kubwera mu nthawi yatsopano."Ndipo tsopano,iwe...."Mose wapita ndipo sabweleranso.Yoswa ndi mtsogoleri watsopano wa anthu.Mulungu akufuna kuti iye azindikire chenicheni ichi.Yoswa amafunika aphunzire kuziona yekha mu njira yatsopano ya udindo watsopano. Sanalinso othandizira mtsogoleri; wasintha tsopano!Atsogoleri otumikira vomelani kusintha mmalingaliro mwanu zomwe zikufunika kuchitika mu udindo watsopano koma osati ndi kuzikweza kapena kuzidalira mwa iwo okha.Amazindikira ndikuzichepetsa ndi kuyamika pa udindo wawo watsopano pantchito.
Zindikilani ntchito
Chotsatira Mulungu akukumbutsa Yoswa za ntchito yomwe ili kutsogolo kwake,"Ndipo tsopano...."konzeka kuwoloka ntsinje wa Yelodani kulowa mu mzinda...."Mulungu anali ndi ntchito yoti Yoswa agwire ndipo inali yaikulu,kutsogolera anthu a dziko kulowa mmalire a dziko lina.Mulungu Ali ndi ntchito kwa atsogoleri onse otumikira omwe apatsidwa ntchito zatsopano kapena kupitiliza zakale.Atsogoleri otumikira ali mbali yoti agwire chifukwa pali ntchito yoti agwire kuti akwaniritse zolinga zamulungu pa malo ena ndi nthawi yake. Atsogoleri otumikira amazindikira kuti Mulungu wapatsa iwo malo otumikira ndicholinga chopitiliza ntchito yake.Amazindikira kuti utsogoleri ni nkhani ya iwo koma cholinga Chachikulu cha Mulungu. Amayambabwino pozindikira zenizeni za kale,zatsopano ndi ntchito yomwe apatsidwa. |