Taona momwe Mose anavomelezera zenizeni mu kusinthana kwa udindo kwake ndi momwe anamudalitsila Yoshua ,olowammalo mwake.Munkhani yomalizayi ,tiona momwe anachengetelera maubale.Nkhani ikutiuza za mmene imfa yake inakhudzila anthu."A Israeli anamulira Mose mu zigwa za Moabu masiku khumi ndi awiri kufikira nthawi yolira maliro itatha.(Deuteronomo 34:8)
Imfa ya Mose inakhudza dziko la Israel.Mose anawatulutsa mdziko lguputo ndi kwa zaka makumi anayi mu chipululu.Anali mtsogoleri yekhayo yemwe amamudziwa koma tsopano wapita!Kubuma kwawo kunaonetsela kuzama kwa maubale omwe Mose anali nawo ndi wanthu.
Mu masiku makumi atatu akulira ayenera kukumbukira nkhani zambiri za mu utsogoleri wake. Anakumbukira momwe anamufikira Farao ,kugawa Nyanya Yofiila ,anawabweletsela malamulo khumi,anaphimba nkhope yake yowala pochokera pamaso pa Mulungu,kumanga chihema,ndi kudzodza Aroni.Anakamba nkhani za nthawi yomwe anatulutsa madzi kuchoka muthanthwe,mmene anaona Dathani ndi Abiramu anamezedwela ndi nthaka,mmene anapachikira njoka ya mkuwa kuwapulumutsa ku mliri ndi kusankha akulu makumi asanu ndi awiri(70).
Kusintha kwa utsogoleri kwa Mose kukutikumbutsa ife tonse kuti utsogoleri umayendela maubale.Utsogoleri wake siudali oyendela kuti ndianthu angati anawatsogolera kapena ndizaka zingati anawatsogolera. Mphanvu ya utsogoleri wake sunayendele mtunda omwe anawatulutsira Ku Iguputo kufikira ku malire a Dziko la Malonjezano.Utsogoleri wake unayezedwa ndi maubale.Mu kusintha utsogoleri, atsogoleri otumikira phunzirani kusamalira maubale onse omwe alipo.
Samalirani a omwe mwawatsogolera.Mose amakonda anthu omwe anawatsogolera. Buku lonse la Deuteronomo ndi mau ake otsanzika kwa anthu omwe amafunitsitsa kuti akapeleke malo ake kumwamba(onani Exodo 32:31,32).Pomwe amafika kumapeto kwa ulendo wa utsogoleri wake,anatenga mutu umodzi (Deuteronomo 33) kudalitsa mtundu uliwonse .Kusintha utsogoleri kwa Mose kukuonetsela kulira mumtima kwa kutayika kwa maubale komwe kumayenelera.
Atsogoleri otumikira phunzirani kuti mbali imodzi ya kusamalira maubale ndi kuwalora apite.Kusintha mu utsogoleri kumasowekera kusintha kwa maubale ndi kuwamasula omwe wakhala ukuwakonda.Mtsogoleri otumikira akhoza kukhala ndi kuthekera kosungabe maubwenzi ndi anthu atatha kuyendabe ,koma amavomereza kuti sali m'busa wawonso,bwana wawo,kapena owatsogoleranso.
Atsogoleri otumikira amasamalira maubalewa koma sayembekezera kupitilira munjira yomwe analiri poyamba.
Samalirani maubale ndi omwe akakhale atsogoleri.Taona kale momwe Mose anadalitsira Yoshua,olowammalo mwake momwe anaikira manja ake pa iye pamaso pa anthu omwe.Poyambilira ,Yoshua anali pambali pake pomwe ankayimba nyimbo yake yotsiriza kwa dziko(Deuteronomo 32:44).
Mose analemekeza ubale uwu ndikuuuwonetsera kwa atsogoleri onse otumikira momwe angasamalire ubale ndi yemwe akulowa mmalo mwathu.Patha kukhala kukhulanabe kapena kusokonekera mu ubale ndi yemwe akukutsatira.Koma atsogoleri otumikira amalemekeza olowa mmalo mwawo pokana kumvera ku mafunso kapena madandaulo a omwe anawatsogolera kale.Mwachisomo amasankha wena mu kutsogoleredwa ndi mtsogoleri watsopano.
Samalirani Maubale akutsogolo.Kusintha utsogoleri kwa Mose kunali kotsiriza kuchoka mu dziko lino.Analowa mu mulingo watsopano wa maubale amuyaya.Koma kwa ambiri aife ,kusintha kwathu kuzatitengera kuchoka ku utsogoleri wa gulu lina kapena malo kutipititsa kwina.Nthawi yakulira tsiku lina idzatha monga momwe zinaliri kwa Mose.
Pomwe atsogoleri otumikira akulira kutayika kwa maubale mu kusintha kwa utsogoleri,amayembekeza ndi chimwemwe
Maubale amtsogolo .mtima wao ofuna kutumikira uzawatsogolera ku maubale atsopano.Ndipo momwe akutsanulira chikondi chawo mu maubale atsopanowo, nkupita kwanthawi maubalewa azakhara opambana ndi odzadza ndi omwe awasiya mbuyo.
Atsogoleri otumikira chokani mmaudindo mwabwino.Ngakhale akudutsa mu kusintha kapena akukonzekera ,amaphunzira kwa Mose kuvumeleza zenizeni ,kudalitsa olowammalo mwawo ndi kusamalira maubale. |