Gawo #284, March 3, 2022

KUSINTHA KWA ABC: DALITSANI OLOWAMMALO MWANU

Munkhani yapitayi,tinaona momwe Mose  analandilira zenizeni za kusinthana kwake.Tsopano,tiyeni tiyike chidwi chathu kwa Yoshua,omwe analowa mmalomwake.

"9Tsono Yoshua mwana wa Nani anali odzala ndi mzimu wanzeru  chifukwa Mose anaika manja ake pa iye.Ndiye a Israeli anamumvela ndikuchita  zomwe Mulungu analamula Mose.10 Kuyambira pamenepo,palibe mneneri anadzuka my Israeli ngati Mose,yemwe Ambuye amayankhula naye maso ndi maso,11 yemwe anachita zozizwa  ndi zodabwitsa zomwe Ambuye anamutuma kuchita mdziko la Iguputo_kwa Farao ndi kwa ogwira ntchito ake ndi kwa dziko lake lonse.12 pakuti palibe yemwe  anaonetsa ntchito zamphamvu kapenanso kuchita ntchito zozizwitsazomwe Mose anachita pamaso pa  a Israeli one" (Deuteronomo 34:9_12).

Mose anadalitsa Yoshua munjira zingapo ndipo akuonetsa atsogoleri  onse  otumikira momwe angadalitsile olowammalo mwawo pomwe pachitika kusitha kwa utsogoleri.

AKONZEKELETSENI BWINO. Yoshua "anali odzala ndi mzimu wanzeru." Izi zinabwela patatha zaka zoikiza ndikukonzekeletsedwa ndi Mose  mnthawi yamoyo wake.Mose amagawana ntchito ndi Yoshua. Amapeleka maumwayi kwa Yoshua kuti akumane ndi Mulungu kupezeka  nawo pakati pa  atsogoleri ena a dziko.Yoshua anali ndi kuthekera kopeza ukadaulo mu nkhondo,kulakwitsa,ndizina zambiri.Pomwe nthawi yosintha utsogoleri inafika ,Mose anali atakonzekeretsa Yoshua kale mwabwino.

Atsogoleri otumikira sadikilira nthawi yosintha mtsogoleri kuti muikize mwa atsogoleri ena,ndi chapamtima pawo kuona ena akuchitabwino atalowa mmalo mwawo.Amadalitsa olowammalo mwawo powakonzekeletsa bwino.Munthawi zomwe mtsogoleri alibe mwayi osankha olowammalo mwawo, amayesetsa  kuchita mbali yawo kutula udindo munjira yomwe imalora olowammalo mwawoyo kuchitabwino.Ndipo amachita zonse zomwe angathe pokonzekeletsa anthu kulandira mtsogoleri watsopano.

ATUMIZENI BWINO.Mose "anaika manja pa iye".Ichi ndichizindikiro choti chochitikachi chinali mbali yofunikira mu kusitha kwa udindo kwa Mose.Poika manja ake pa Yoshua, Mose anavomeleza poyela kuti iye sanalinso mtsogoleri. Manja ake anadalitsa Yoshua kulowa mmalo ake pomwe amaikiza utsogoleri  ndiulamuliro wake  mwaiye.Chotsalira chinali chokongola," a Israeli amunvera iye  ndikuchita zomwe Mulungu analamula Mose."

Pomwe atsogoleri otumikira asinthana bwino,ntchito ya Mulungu imapitilira popanda mpungwepungwe.Atsogoleri otumikira samangosiya mwakachetechete ntchito zawo.Amadalitsa poyela omwe akulowa mmalo mwawo ndikulakalaka kuikiza mwa iye kudalira  ndi zamphanvu zomwe agwira limodzi kuti atukuke.Poyela ngakhale kumbali amachita zonse zomwe angathe kuti awonetsetse chipambano cha olowammalo mwawo.

ASIYENI BWINO.Mphatso yomaliza yomwe Mose anapereka kwa Yoshua ndi kusowapo pamalopo! Sanakhale pomwepo kuonelera ndi kumamuchonga Yoshua kapena kuti aziona zolakwitsa za Yoshua. Anachokapo!Atsogoleri otumikira amachoka mmaudindo  mwabwino pongochokapo pomwe nthawi yawo yatha .Atsogoleri otumikira safuna kuti afe kaye kuti achoke bwino!Koma amalolera  zomwe anali kufa ndikuonetsetsa kuti apereka njira kwa mtsogoleri watsopano.Amaonetsetsa kuti  asagwirenso ntchito yomwe amagwira ali mu utsogoleri.Pomwe pali pothekera ndi poyenelera,amapereka mpata potalikira  ndi kusakhalapo  kuti mtsogoleri watsopano atenge mbali ndi ntchito zake popanda kusokonezedwa .

Mwachiziwikire,pakhoza kukhalapo nthawi zomwe kusitha udindo kumafunika mtsogoleri ochokayo  akhalebe akuwunikira  kapena kumuuza zochita mtsogoleri watsopanoyo.Izi zikhoza kuchitika.Koma pamakhala nthawi ina  yomwe kukhalitsa kwambiri kumaononga  kwambiri kupambana kuchitira  ubwino.Atsogoleri Otumikira amakhala ofuna kuchoka ndipo ena alowepo.

Atsogoleri Otumikira amalakalaka kuchita bwino kwa gulu lomwe  amalitsogolera.Kotero,amakonzekeletsa ozalowammalo  patali nthawi yosinthana isanafike.Amawadalitsa  powakonzekeretsa  bwino  ndi kuwatumiza poyela mkuona kwa onse.Akatero amachokapo kuyendela yawo!

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • Mu kusintha kwa maudindo komwe ndaonapo,ndaona bwanji atsogoleri akuchitabwino pa kudalitsa  omwe akulowa mmalo mwawo? Ndaonabwanji kusowa kwa dalitso kwa olowammalo? Zotsatira zokhalitsa zinali zotani?
  • Mu kusintha maudindo mbuyomu mu utsogoleri mwanga  kodi  ndachitabwino bwanji podalitsa olowammalo mwanga?
  • Mu udindo wanga panopa,kodi ndifunika ndichitechani kuti ndikonzekeletse bwino munthu wina ozalowa mmalo mwanga?

    Munkhani yotsatirayi ,tizaona lembo la "C" la mu ABC' kusintha bwino kwa maudindo:
    Vomelezani zenizeni
    Dalitsani Olowammalo mwanu.
    Samalirani maubale.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online