Gawo #283, February 16, 2022

KUSINTHA KWA ABC: LEMEKEZANI ZENIZENI

Mtsogoleri wina aliyense pangafupike kapena pangatalike amafika ku nthawi yosintha atsogoleri.Kusintha kumeneku kutha kuchitika mofuna ,mmene zinthu zilili, motsogozedwa ndi Mulungu,kapena pakutha chabe kwa nthawi.Ndiye,atsogoleri onse atha kukhala kuti achokera mu kusintha ,akukonza  zosintha,kapena akuika maziko a kusintha kwa mtsogolo!

Mmene ndikulemba ,nanenso ndikukumana ndi kusintha kofunikira mu utsogoleri wanga omwe.Ndiye kapena ndikulemba ichi Kuti  chindipindulire ine mwini,koma ndikukuitanirani kuti muzindikira pamodzi ndi ine mmene atsogoleri otumikira  angasinthire .Tiona za kusintha komaliza pa  moyo wa Mose pomwe akutsatira njira ya kusintha ya ABC.:Zindikirani  zenizeni,Dalitsani  Opitiliza,ndipo Samalirani  Ubale.

"Ndipo Mose anakwera phiri la Nebo kuchoka Ku Mapili a Moabu kukwera pa ku Pisa,kudutsa Ku  Yeriko.Kumeneko Mulungu  anamuonetsa malo onse _kuchoka Ku Giiadi kupita Ku Dan,.....4.Ndipo Mulungu anati kwa iye," Awa ndimalo ndinalonjeza  pa pangano kwa kwa Abraham, Isaki ndi Yakobo pomwe ndinati,'ndizapeleka kwa mtundu wako.'Ndafuna kuti uwaone ndi maso ako,koma  suwoloka kupitako,"5 Ndipo  Mose mtumiki wa Ambuye anafera kumeneko ku Moabu,monga momwe Mulungu ananenera.6Anamuika ku Moabu, muchigwa choyang'anana ndi Beti Peori,koma mpaka lero palibe yemwe amadziwa komwe mnda ake ali.7.Mose anali wa zaka  120 momwe amafa,koma maso ake sanafoke kapena thupi lake kutha mphanvu.  A Israel analira maliro a Mose muchigwa cha Moabu kwa masiku makumi atatu,kufikira nthawi yolira ndikubuma inatha.(Deuteronomy 34:1,4_8).

Nthawi ina Mose anali mtsogoleri wamkulu wa dziko lonse.Nthawi yotsatira anasintha kukalandira mphotho yake yamuyaya.Chinthu choyambilira chomwe atsogoleri otumikira aphunzirepo kuchoka pa kusintha kwake ndi  kuzindikira  zinthu  zitatu zomwe ndizenizeni.

  Zindikirani zenizeni zomwe zachitika.Mose anatsogolera dziko mu nthawi zina zovuta kwambiri.Ndikukhulupilira kuti anakwera pang'onopang'ono phiri  pomwe amaganizira kugawika kwa nyanja ya Yofiira,malamulo khumi,madzi ochoka muthanthwe,ndi zina zomwe anakumana nazo mu zaka makumi anayi autsogoleri wake.Zambiri adachita.

Atsogoleri otumikira  amazindikira ndi kuyamikira kwa Mulungu zonse zinakwaniritsidwa.Ndipo pamene atsogolera bwino,zambiri zachitika,samazitukumula okha koma amakondwelera zenizeni zomwe Mulungu wachita!

Kuzindikira zenizeni za zomwe sizinakwaniritsidwe.Mulungu anamupatsa Mose kafungo chabe ka malo omwe analonjeza anthu ake.Ndikutha kumva ululu wa Mose pomwe ananva mau a Mulungu, "sukalowa mu dzikolo" Kwa zaka zambiri Mose anasunga masomphenya amoyo koma tsopano amachoka ,ndipo zambiri sadachite.

Pomwe atsogoleri otumikira akumana ndi kusintha, amazindikira kuti pali zinthu zomwe sizinachitike .Ngakhale  chifukwa cha kulakwitsa kwawo.(monga zinaliri ndi Mose) kapena kungoti nthawi yakusintha inakwana,amavomereza zenizeni zoti zambiri zinali zisanachitike.Amamvetsetsa kuti masomphenya a Mulungu nthawi zonse amakhala aakulu koposa utsogoeri wawo ndipo zina sizizakwaniritsidwa kusintha kusanachitike.

Zindikirani zenizeni za zomwe zizachitike.Monga Mose anaunika malo a Israel,amaona zomwe zizachitike akapita.Mtsogoleri wina azachita zomwe sadachite!

Chioonadi chopweteka ichi sichimakhala chophweka kuti mtsogoleri  achivomeleze.Atsogoleri ena savomeleza choonadi choti akukalamba!kapena kuti achita zonse zomwe akadatha ku  bungwe.Kapena kuti ena akufunika kuti alowemo ndi mphatso zatsopano kuti apumile moyo watsopano mu masomphenya. Koma atsogoleri otumikira phunzirani kwa Mose kuzindikira choonadi ichi ngati nthawi yafika yakusuntha.

Atsogoleri otumikira mukusintha amakondwera pa zomwe zachitika. pomwenso akuzindikira kuti Mulungu azagwiritsa ntchito mtsogoleri wina kukwaniritsa zomwe sizinachitike.Amazindikira zenizeni izi pamene akutsatira chitsogozo cha Mulungu mu kusinthaku.Amalira kwa Mulungu kuti ayang'anire mitima yawo ku kuzikweza ,nsanje,kapena kuona kulephera.Amakhala ofuna kupitiriza kutumikira pamalo omwe Mulungu watsogolera.

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • Mukusintha komwe ndaona ,kodi ndaona motani atsogoleri akuchita  bwino pa kuzindikira zenizeni?
  • Mu kusintha kwambuyomu mu utsogoeri wanga ,kodi ndazindikira mwabwino motani  zomwe zachitika, zomwe zatsala kuti zichitike ndi zomwe zizachitike mtsogolo?
  • mu mbaliyanga panopa,kodi ndichite chani lero kuti ndikonzekele bwino kusintha  kwa utsogoeri?

    Mu phunziro lotsatira ,tiona za kusintha kwa "B"mkati mwa  ABC:
    Zindikirani Zenizeni.
    Dalitsani Olowammalo.
    Samalirarani maubale.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online