Gawo #282, February 2, 2022

KUSANKHA ATSOGOLERI: KUKUZA ANTHU

Taona kale  zitsanzo zingapo kuchokera my buku lopatulika kuti atsogoleri anasankhidwa mu buku LA Machitidwe.Atsogoleri ena anasankhidwa potumidwa ndi Mulungu.Ena anasankhidwa ndi anthu pomwe ena anangisankhidwa ndi odzala mpingo.Nthawi zina, panali kasakaniza ka njira zosankhira.Tsopano tiona njira yomaliza ya kasankhidwe ka atsogoleri,koonetseledwa bwino kuchokera mu moyo wa Paulo."Anatumiza awiri a omuthandizira,Timoteyo ndi Erasito,ku Makadonia ,pomwe amakhala Ku dela la Asuli kwa kanthawi."(Machitidwe 19:22).

Chimachitika ndi chani munyengo imeneyi?Paulo amadzutsa ndinso amakuza atsogoleri Timoteyo ndi Erasito.Kenaka anawatumiza kukatsogolera ku Makadoniya.Atsogoleri otumikira atha kuphunzira kwa Paulo posankha atsogoleri pokuza anthu.

NJIRA YAKUSANKHA  POKUZA ANTHA.Kodi Paulo amasankha bwanji atsogoleri pokuza anthu?Mu  umunthu wa Paulo munalinso chapamtima cha kudzala mipingo koma kuti zitheke  modabwitsa ndi momwe ndondomeko zake zinalili za kuchulukitsa ndi  kukuza anthu. Kulikonse komwe anali kupita amapita ndi kagulu ka wanthu omwe amawakuza mu utumiki. Amasankha atsogoleri kuchoka mwa amene amawakuza yekha. Njira ya makuzidwe ndi kutumiza anthu ku utumiki ngati atsogoleri ndi chimodzi mwa zifukwa zomwe zinapangitsa Mtumwi Paulo kuthandiza kwambili mpingo mpaka lero.

Zikuonetsa kuti Paulo samakuza anthu kuti akagwile nchito imodzi yapaderadera,koma iye ankangokuza  basi ,kenaka ndikuwasankha kuti akagwire ntchito malingana ndi maitanidwe awo.(onani Machitidwe 18:19  pali chitsanzo china). Ena atha kunena kuti samapatsidwa ntchito zapadela kapena maudindo apadela a atsogoleri.Koma Paulo anawatumiza ndi ulamuliro otsogolera ndi kuchita mmalo mwake.

Atsogoleri otumikira onani njira yokuza anthu ngati mbali  imodzi ya maitanidwe a Mulungu.Amazindikira kuti kuti dziko lathu likufunika atsogoleri ndipo amafunafuna kuwakuza ngakhale pali kapena ngakhale palibe udindo.Kukuza ena ndi chapamtima cha mtsogoleri otumikira

MPHAMVU YOSANKHA POKUZA ANTHU.Njira imeneyi  yosankha atsogoleri iri ndi maubwino ochuluka.Iyi ndi  itha kukhala  yopambana kwambiri koposa zina posankha atsogoleri. Njira zina zomwe taonapo zimafunika mtsogoleri akhale pomwepo kenaka asankhidwe.

Paulo sanadikire kuti atsogoleri azikuze okha

,koma inaikiza mu moyo mwawo!pomwe amakuza atsogoleri, anali ndi gulu lomwe amasankhamo atsogoleri ofunika pa malo omwe akufunika munthu.Njira iyi yosankha atsogoleri imapeleka nthawi yokwanira kuti mtsogoleri okhala ndi kuthekera adziwike bwino ndi mtsogoleri yemwe alipo.Sipamafunikira  kuyesedwa  kulikonse ,akhala akugwira ntchito limodzi ,pamodzi kwa nthawi yaitali!Pali ubale okhazikika  bwino pakati pa  Paulo ndi omwe amawakuza.

Atsogoleri otumikira zindikirani mphamvu yosankha atsogoleri kuchoka mwa omwe akuza okha.Amaona njira  imene ingachulukitsile atsogoleri pa zolinga za Mulungu, ndipo amatsatira chitsanzo cha Paulo poikiza  ndi kukuza omwe amuzungulira.

ZOVUTA ZOMWE ZIMAKHALAPO POKUZA ANTHU. Pakhoza kukhalanso zobetchera ndi njira imeneyi.Atsogoleri ena amatha kukuza wanthu ndi zolinga zoti akwanilitse nfundo zawo kapena akwaniritse masomphenya awo .Ichi ndi cholinga cholakwika ndipo chiikhoza kupangitsa maubale osakhalabwino.Kuopsya kwina ndikoti mtsogoleri sangaone mupyolera munthu yemwe akumudziwa posankha mtsogoleri.Akhoza kusiya omwe ali ndi kuthekera kwakukulu.Atsogoleri otumikira mwanzelu amapewa zobetchera  zosankha pokuza anthu  pomwe akutsatira chitsanzo cha Paulo.

Atsogoleri otumikira amaona kuti njira yosankha anthu omwe awakuza okha ngati njira imodzi yomwe Mulungu akhoza kutsogolera pomanga gulu lawo.komabe amapitiliza kufunafuna chitsogozo cha Mulungu  panjira yosankhira atsogoleri. Amafunafuna kutsatira chitsogoza cha Mulungu mu nyengo iliyonse ndipo amakhala osamalitsa  kuzindikira kuti pali nthawi zosiyana,zomwe Mulungu akhoza kutsogolera njira yomwe sanakonde  kugwiliitsa ntchito.Amazindikira kuti pali njira zingapo zomwe ndizopezeka mu Buku Lopatulika posankha atsogoleri.

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • kodi zochitika zanga zambuyo mbuyo ndi kaganizidwe kanga pa omwe andizungulira kwaumba kaonedwe kosankha pokuza wanthu ndekha kapena ayi nanga kandionetsa kuti ndi njira yabwino yosankhira atsogoleri?
  • kodi nditha kugwiritsa bwanji njira yosankha pokuza wathu ndekha  posankha mtsogoleri?ngati ndakonda kugwiritsa ntchito njirayi , kodi ndapewa zovita zomwe zilipo pogwiritsa ntchito njirayi?Ngati sindikonda kugwiritsa ntchito njirayi, ndi munjira ziti zomwe Mulungu akundiitanira kuona njirayi kuti ndiyofunika kugwiritsa ntchito munyengo zanga?
  • Munyengo ziti zomwe kusankha atsogoleri omwe wakuza wekha  ikhoza kukhala yabwino  posankha  atsogoleri?Munyengo ziti zomwe kusankha atsogoleri omwe wakuza wekha singakhale yabwino kwa ine?(kuti timalizitse njira zomwe  Paulo amagwiritsa ntchito pokuza ena ,pakhala phunziro lamtsogolo pa  mutu omwewu.)

Mu nkhani yotsatirayi,tiona kumasulira kwa ABC!

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online