Kupeza munthu oyenera pa malo oyenera ndi imodzi mwa ntchito yovuta mu utsogoleri.Tikanaona kasankhidwe ka atsogoleri komwe olemba anzawo ntchito amatsata,amayang'ana zambiri ya munthu yambuyo.Atsogoleri otumikira amagwiritsa ntchito anthu olemba anzawo ntchito, komanso akafuna kuti masankho awo atsatila chitsogozo chamulungu.Ambiri amalozera kwa mpingo oyamba pokometsela njira yomwe akondayo posankha atsogoleri njira ya mu "buku loyera"ndinso yabwino kwambiri.Koma kodi buku la machitidwe likutiphunzitsa atsogoleri otumikira za njira yoyenera posankha atsogoleri?pali njira zingapo zinayi zosiyana zomwe mpingo oyamba unasankha.Taonakale "kulamulidwa ndi Mulungu" ndi "kusankha poyendera kutchuka" ngati njira zosiyana zomwe mpingo wakale umasankhira atsogoleri.Koma palinso njira ina. "Analalika uthenga wabwino mu mzinda wina ndipo anapeza gulu lambiri la ophunzira kenaka anabwelera ku Layisitila,/Koniya ndi Antiyokeya, Kuwapatsa mphamvu ophunzira ndi kuwalimbikitsa kukhalabe owona muchikhulupiliro.'tikuyenera kudutsa mu zovuta zambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu,'anatero. Paulo ndi Banaba anawasankhira akulu a mpingo pa mpingo uliwonse ndipo,ndi pemphero ndi kusalakudya,anaikiza iwo kwa Ambuye,Yemwe amayenera kuika chidaliro chawo." (Machitidwe14:21-23) Pamenepa, atsogoleri a mpingo, Paulo ndi Banaba, anasankha akulu a mpingo pa mpingo uliwonse. Tiyeni tionepo pa kasankhidwe aka ka atsogoleri.
NJIRA YOSANKHA ATSOGOLERI NDI OMWE ALI MU UTSOGOLERI. Njira yomwe Paulo ndi Banaba anagwiritsa ntchitoyi ikuoneka ngati yosavuta,"anangosankha atsogoleri "mu mipingoyi.Zikuonetsa kuti sanafunsire uphungu kwa mamembala a mipingoyo komanso sanapangitse masankho.Komabe, anaikapo pemphero ndi kusalakudya ngati mbali ya kasankhidwe kawo.Atsogoleri otumikira phunzirani pa chitsanzo chawo kuti posankha atsogoleri mu njira iyi ndi zothandiza kufuna chitsogozo cha Mulungu.Atsogoleri otumikira sagwilitsa ntchito njirayi kuika anzawo kapena achibale mu utsogoleri.Amagwiritsa ntchito njirayi ngati machitidwe otumikira kwa omwe akhale pansi pa utsogoleri ongosankhidwa umenewu.pomwe atsogoleri otumikira agwiritsa ntchito njirayi mosabisa amasamalitsa kuona kuti zotsatira za zisankho za omwe akhale owatsatira.
UBWINO POSANKHA ATSOGOLERI POGWIROTSA NTCHITO NJIRA YONGOSANKHA. Pali ubwino osankha atsogoleri mongoloza.Ndi njira yosavuta ndipo ikhoza kupangidwa mwachangu ngati pakufunikira kutero Mwachangu.Munjira Zina, mtsogoleri yemwe akusankha akhonza kukhala ndi kumutsatira bwino za mphatso za munthuyo, maitanidwe ndi kuthekera koposa omwe skumutsatira.Mu mipingo iyi , Paulo ndi Banaba mwina anaona mulingo wa kukhwima mwa okhulupilira atsopano kuti sikunali kolimba kwenikweni kuthe akanatha kusankha atsogoleri. Choncho njirayi ikhonza kukhala ndi ubwino kwa gulu la chichepele.Atsogoleri omwe anasankhidwa munjira imeneyi anali ndi kuvomerezedwa kowonekeratu kwa Paulo ndi Banaba, omwe anadzala mipingoyo ndipo anaoneka kuti ndi owaimilira awo.Atsogoleri otumikira phunzirani pa chitsanzo ichi kuti kumaonetsetsa mphatso ndi maitanidwe a munthu musanapange kanthu.Kenaka molimbamtima amasankha atsogoleri mokomera onse.
ZOVUTA ZOPEZEKA POSANKHA ATSOGOLERI MONGOLOZA. Pomwe zikuoneka kuti palibe vuto ndi kusankha komwe Paulo ndi Banaba anapanga, njira iyi ikuyenera kutsatidwa mosamalitsa.Mphamvu yosankha popanda ganizo kuchoka kwa ena kutha kukhala kopangitsa mtsogoleri kuzimva ndi kuthera ku zokhumudwitsa zoyipa.Kusiya anthu pambali posankha kukhoza kupindula nthawi zina koma nthawi zina zimatha kupangitsa kuwukira kwa mtsogoleri wosankhidwayo.kumvera kwa mtsogoleri wosankhidwayo kukhonza kukhala kochuluka kwa munthu yemwe anawasankhayo mmalo mozipereka kutikira anthu omwe ali pansi pawo.Atsogoleri otumikira, mwanzeru amapewa kugwa mumbuna kwa kusankha atsogoleri.Ngati Paulo ndi Banaba, amafunsira chitsogozo chochokera kwa Mulungu ndi kusankha gulu mmalo mwa anthu. Samalolera kuti iyi ikhale njira yomweyo yomwe atsogoleri amagwiritsa ntchito mpaka kale. Atsogoleri otumikira amaona njira yosankha pongoloza ngati imodzi mwoa njira yomwe Mulungu akhonza kutsogolera kumanga gulu lawo.Komanso amazindikira kuti pali nthawi zomwe azatsogolera kuti agwilitse ntchito njira ina.Mu zokambirana zotsatirazi , tiwona za njira yotsiriza yosankhira atsogoleri.
|