Gawo #280, December 8, 2021

KUSANKHA KWA ATSOGOLERI

Atsogoleri amasankha mtsogoleri wina kuti alowe nawo mgulu lawo ndikuti awathandize kuchita masomphenya.Koma njira zogwilitsidwa  ntchito posankha zimasiyana malinga ndi mmene ziliri.

Buku la Machitidwe  muli njira zinayi zosiyana zomwe mpingo wakale umasankhila atsogoleri .Imodzi mwa izo  ndi pomwe chosowa chinazuka pa zoyenera atsogoleri.

1."Munthawi imeneyo pomwe chiwerengero cha ophunzira chimakwela  a Helene achiyuda pakati pawo anadandaula motsutsana ndi ayuda a chi Heberi chifukwa amayi awo amasiye samathandizidwa pa kugawa chakudya cha tsiku ndi tsiku.2 Ndipo khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndikiti,"Sikwabwino kwa ife kuleka utumiki wa mau a Mulungu ndi kumagawa chakudya.3.Abale ndi alongo sankhani abambo asanu ndi awiri kuchokera mmagulu mwanumo odzala ndi Mzimu ndi nzeru.Tipereka udindo umenewu kwa Iwo.4 kuti tiyike chidwi chathu ku pemphero ndi utumiki wa mau"Lingaliro iri lina kondweletsa gulu lonse .Anasankha Sitifano,munthu odzala ndi chikhulupiliro ndi Mzimu Oyera,komanso Filippo,ndi Polokolo,ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parimera,ndi Nikolao, ndiye opinduka wa ku Antiokeya.(Machitidwe 6:1_5).

Atumiki otsogolera dziwani kuti kupatsa ena mphamvu kupanga chisankho zikhoza nthawi zina kukhala njira  yabwino pakusankha atsogoleri.

NJIRA YOSANKHA YAKAWIRIKAWIRI YOYENDERA KUDZIWIKA.

Mmene zinaliri,madikoni asanu ndi awiri anasankhidwa Koma atumwi sanapange nawo masankho:anaitana gulu kuti lisankhe anthu omwe akhale atsogoleri. Uku kunali kusankha moyendera kudziwika,zingofananirako ndi njira yosankhira ya demokalase yomwe anthu amavota mwa ufulu.Iyi ikanakhala ya chiopsyezo  kwa atumwi .Zikanatani ngati anthuwo akanasankha munthu olakwika?

Njirayi imagwiritsidwa ntchito mu mipingo yambiri pomwe anthu amavota,ndipo opambana amalengezedwa. Izi sizingachitike kwambiri mu bizinesi,koma  mtsogoleri otumikira yemwe ndi mwini wake kapena mtsogoleri angathe kuitana ena kutenga mbali mu ndondomeko zovotela popereka maganizo awo,ndemanga kapena kuwunika zambuyo .Ngakhale kuti chisankho chenicheni Sichipangidwa ndi voti ,mtsogoleri otumikira ndi ofuna kupereka mpata kwa ena  mundondomeko .Njira imeneyi imafunikira kuzichepetsa ndi chikhulupiliro chozama mwa anthu ndipo atsogoleri otumikira  a Mulungu ndi ofuna kupereka mphamvu yawo kwa ena.

MPHAMVU YOSANKHA POYENDERA KUDZIWIKA.

Njira imeneyi iri ndi maubwino ochuluka.Imodzi ya ubwinowu ndiwoti anthu amasankhawo amalimbikitsika potenga nawo mbali."Uku kumakhala kusankha kosangalatsa gulu lonse."Pomwe anthu atenga nawo mbali popanga chisankho, sikwenikweni kudandaula za zotsatira zake.

Sichimenechi chokha,koma atsogoleri osankhidwa pogwilitsa ntchito njirayi amanva kutsatilidwa kwa Iwo amene aziwatsogolerea kuyambira pachiyambi.Amayamba kutsogolera ndi kutsimikizika  kuti omwe akuwatsogolerawo akufuna kuti awatsogolere pa udindowo.

Ubwino wina wa njira imeneyi ndiyoti  anthu opanga chisankho amakhala pafupi kwa atsogoleri okhala ndi kuthekera kuposa atsogoleri omwe ali pamwamba penipeni  mu ndondomeko ya zisankho.Atsogoleri otumikira azindikire kuti si Iwo okha omwe akhoza kusankha atsogoleri  ndikuti enanso atha mwanzeru kuwalora kutero.

ZOVUTA ZOMWE ZILIPO POSANKHA POGWILITSA NTCHITO KUDZIWIKA .

atsogoleri otumikira zindikirani kuti pali ziwopsyezo zochitika munjira yosankha mwa ufulu wa anthu.Choopsya chimodzi ndichoti kusankha poyendera kudziwika kutha kusiya Mulungu pambali!kusankha kutha kukhala mpikisano wa kutchuka.

Kuopsya kwina ndikoti cholinga chosangalatsa  anthu chitha kukhala chofunika kuposa maitanidwe oti utsogolere anthu.Ichi ndi chiopsyezo makamaka kwa  omwe  paumunthu wawo amakonda kusangalatsa anthu.

Koma atsogoleri otumikira  atha  mwanzeru  kufikira ndi kutsogolera mu masankho ngakhale pomwe enawo akupanga chisankho. Atumwi anaika zikhomo apa asanapange masankho ;ankafuna atsogoleri omwe anali"odzala ndi Mzimu ndi nzeru".Atsogoleri akhoza kuitanitsa mapemhero osala kudya asanapangitse masankho kapena mkati mopanga zisankho.Akhozanso kupereka malangizo a mtumdu wa  Atsogoleri omwe akufunika.

Atsogoleri otumikira amawona njira yosankha pogwiritsa ntchito kudziwika ngati imodzi mwa njira yomwe Mulungu angatsogolere pa mamangidwe a gulu lawo.Komanso amazindikira kuti pali nthawi zina Mulungu atha kuwatsogolera kutsatira njira ina,mu nkhani ina yotsatirayi.

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • Kodi kaganizidwe ndi machitidwe a omwe anandizungulira anaumba maonedwe anga oti kusankha pogwiritsa ntchito kutchuka ndi njira yabwino yosankhira atsogoleri?
  • Kodi ndipati pomwe nditha kugwiritsa ntchito njira yosankha mtsogoleri poyendera kutchuka?Ngati ndikugwiritsa ntchito njirayi,Kodi ndaonetsetsa kupewa kugwa mmavututo pogwiritsa ntchito njirayi? Ngati sindikasankha kugwiritsa ntchito njirayi,munjira ziti zomwe Mulungu angathe kundiyitanira kuti ndigwiritse ntchito njira imeneyi  mu nthawi imeneyi?
  • Ndi mu nthawi ziti zomwe kusankha poyendera kudziwika ingakhale njira yabwino kwa ine posankha atsogoleri?Munthawi ziti zomwe kusankha poyendera kudziwika ingakhale njira yabwino kwa ine posankha atsogoleri? Munthawi ziti zomwe kusankha poyendera kudziwika singakhale njira yabwino kwa ine?
  • Munkhani ina yotsatirayi ,tiona za kusankha atsogoleri mongosankhula.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2021

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online