Kusankha mtsogoleri ena ndi imodzi mwa ntchito yovuta mu utsogoleri.Atsogoleri ambiri apambanapo enanso analephera mu gawo iri.Mtengo wa kulephera ndi waukulu pomwe posankha sitinasankhe munthu oyenera. Kodi kufikira kwabwino pofuna kupeza ena omwe azamange gulu ndi kuthandiza kupitiliza masomphenya ndi kuti?
Nthawi zambiri zikhalidwe zathu kuphatikizika ndi zomwe tinadutsamo mmbuyo,zabwino ndi zoipa,zimaumba mafikilidwe athu a mneme timasankhira atsogoleri.Atsogoleri a zamalonda akhoza kutsamira ndi kudalira pa njira yotsimikizika yowunika anthu kuti apeze munthu oyenera. Atsogoleri a mpingo akhoza kutsamira pa njira ya uzimu yomwe imagwira bwino ntchito malinga ndi zomwe akufuna.kenaka amalozera ku mpingo oyamba ku Machitidwe komwe tikuphunzitsidwa kuti pali zinthu zinayi zosiyana momwe Atsogoleri anasankhidwira.
Atsogoleri otumikira phunzirani, onse akhoza kufunika pomwe ayikidwa pa malo oyenera ndi moyenera.
Njira imodzi yosankhira atsogoleri mmbuku la Machitidwe ndi pomwe Mulungu anaitana mtsogoleri wawo Yekha. Izi zinachitika ndi Paulo pa nthawi yokutembenuka kwake.(onani Machitidwe 9:15_16) ndiponso pomwe iye ndi Banabasi anatumidwa kukatumikira ku Antiyokeya.
2.Ndipo pomwe Anali kulambira ndi kusalakudya,Mzimu oyera anati,"mundipatulire ine Banaba ndi saulo ku ntchito yomwe ndawaitanira." Ndipo pomwe anasala kudya ndi kupemphera ,anaikamanja pa Iwo ndi kuwatumiza.(Mac 13:2_3).
NJIRA YOSANKHIRA ATSOGOLERI MOLAMULIDWA NDI MULUNGU.
Njira imeneyi palibe kulowelerapo kwa munthu mu kusankhidwa kwake. Mulungu analankhula momvekabwino kudzela mwa Mzimu ndi kuitana Banaba ndi saulo.Inde anali oyenelera mwapadeledela ndipo anali ataonetsa kale mu utsogoleri,koma panalibe dongosolo la kuyenerezedwa kwao komanso panalibe masankho omwe anachitika!
MPHAMVU YOSANKHA MOTUMIDWA NDI MULUNGU.
Kutumidwa ndi Mulungu kuli ndi ubwino:Mulungu walankhula!ndani otsutsa?Njira imeneyi ikhoza kugwiritsidwa ntchito kwambiri mu mpingo kuposa mu bizinesi,pomwe atumiki otumikira akufuna funa kutsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, pakhoza kukhala zomwe liwu la MULUNGU limaposa liwu la munthu mu Dela Lolemba Ntchito!
Atsogoleri otumikira zindikirani kuti Mulungu ndi Olamula oyenera ndipo pomwe chitsogozo chake chili cha chindunji,amangovomeleza pomwepo!
MBUNA ZOMWE ZILIPO POSANKHA MOTUMIDWA NDI MULUNGU.
Kusankha atsogoleri motumidwa kulinso ndi mavuto ake omwe amaoneka.
Vuto loyamba ndi kumva moyenera ndi momvekabwino liwu ka Mulungu. Zinthu zimaonongeka kwambiri pomwe mtsogoleri agwiritsa ntchito chiyankhulo choti Mulungu wandituma kuti akometse chisankho cha umunthu.Atsogoleri otumikira akhale osamalitsa ponena za okha."Mulungu wandiuza kuti munthu ameneyu akhale mtsogoleri"Ku Antiyokeya, panali mzimu wa chidziwitso ndi gulu.
Chiopsezo china posankha mu njira yotumidwa ndi Mulungu ndi pomwe mtsogoleri wasankha njirayi chifukwa sakufuna kupanga mu njira yovuta yomvetsera kuti munthu oyenera ndi Uti.Sakufuna kapena alibe zida zoyesela mphatso, luso ndi maitanidwe a mtsogoleri oyenera,ndiye amabweza masankho kwa Mulungu!.
Zopatsachidwi,mu Machitidwe 1, matiyasi anasankhidwa ndi mayere,njira ya umulungu.Koma poyamba, atumwi anaika dongosolo la ntchito zoti azagwire ndi kusankha anthu awiri omwe amayenera.kenaka analora Mulungu kuti apange chisankho chomaliza pa njira ya mayele.Atumiki phunzirani pa ichi kuti ngati ndondomeko zokhazikika sizinatsatidwe azakhala mu mavuto akulu ndi njira imeneyi!
Atsogoleri otumikira onani njira ina yosankha motumidwa ndi Mulungu ngati imodzi mwa njira zomwe Mulungu akhoza tutsogolera kumanga kwa gulu lawo.Komanso kuti pali nthawi zina zomwe Mulungu angawatsogolere kusankha njira ina. Mu nkhani ina ikubwerayi,tiona imodzi mwa njira zogwiritsidwa ntchito kawirikawiri |