Gawo #278, October 27, 2021

PHOKOSO LA ATSOGOLERI WACHETE...MU KUZITETEZA

Taona njira zomwe atsogoleri otumikira afunika kukhala chete. Koma nthawi yovuta kwambiri kukhala chete ndi pamene taputidwa kapena kunamiziridwa kuti tapanga chinthu cholakwika.Zimenezi zimachitika ,mwachilengedwe chathu kubweza kwake ndi kuziteteza tokha,kawirikawiri  ndi mau!kuziteteza wekha kawirikawiri ndi ufulu wa anthu dziko lonse.Koma pamene Yesu anamtengela Ku bwalo la mlandu,anaonetsa mu njira yosiyana kwambiri.

59.Wansembewamkulu ndi gulu lonse la akulu a chipembedzo anali kusakasaka umboni wabodza pa Yesu kuti apeze chifukwa chomuphera.60Koma sanapeze ngakhale chimodzi,ngakhale mboni zambiri zabodza zinalipo.Pomaliza awiri anabwera ndi kulengeza,"Munthuyu anati,ndikhoza kuononga kachisi wa Mulungu ndi kumanganso mmasiku atatu,"62 Ndipo wansembe wamkulu anaima nanenakwa Yesu,"Kodi suyankha?Kodi umboni ndiuti pa zomwe anthuwa akunena za iwe?63 Koma Yesu anakhalabe chete. Wansembe wamkulu anati kwa iye,"ndikugamula iwe polumbira  pamaso pa Mulungu ;tiwuze ngati ndiwe Mesiya mwana wa Mulungu. (Mateyu 26:59_63)Kuthekera kwa Yesu kukhala chete apapa ndi kowonekera ndipo kukutiphunzitsa zambiri za mphamvu ya chete mu kuziteteza wekha.

CHETE MUKUZITETEZA WEKHA KUMAONETSA KUZICHEPETSA.

Uchete wa Yesu unaonetsela kuzichepetsa kozama.Mulandu omwe ankamuimba anaupeleka molakwika pa zomwe iye ananena pa Yohane 2:19.

Ndithudi Yesu akanakanitsitsa pompopompo!Koma mozichepetsa anakhala chete,kukana kuziteteza yekha.

Anthu ozokweza amatsutsa mlandu wawo,amaziteteza ndi mau,sangavomele kunamizilidwa kopangitsa kuti awoneke oyipa ngakhale Iwo akhonza kapena ayi.Koma atsogoleri otumikira amaonetsela kuzichepetsa pokhalabe chete ngakhale akuwanamizila.

CHETE POZITETEZA ZIMAONETSELA KUZIDALIRA.

Yesu anaonetsela poyera kuzidalira ndi uchete Wake. Sanafune kukangana pokhala iye  Mesiya.Sanafune kuziteteza za chomwe iye anali.Anadziwa kuti iye ndindani . Uchete wake unakwezamau ndipo panalibe chizindikiro choti  atsimikizire.

Chete mu kuziteteza wekha umalankhula mokuwa kwambiri kuposa kulankhula ndi kutsutsa.zimaonetsa kutsimikiza kozam koti sindikuyenera chitsimikizo choti sindinalakwe;,ndikudziwa sindinalakwe.Nthawi zina mau amphamvu ndi Chete.Atsogoleri otumikira onetselani kutsimikiza  pokhala chete akukunamizirani.

CHETE POZITETEZA WEKHA ZIMAFUNIKIRA KUDALIRA MULUNGU.

Kukhala chete kwa Yesu ali pa mlandu zikuonetsa kuti kudalira kwake sikunali pa chigamulo cha munthu kuti ampeze olakwa kapena amumasula.Anadziwa kuti ndi Mulungu yekha akanawona tsogolo lake.Petulo, patangodutsa kanthawi Yesu ali chetebe,anaziteteza yekha mwaukadaulo(onani Mateyu 26:69-75).Koma patapita Zaka pokumbukira imfa ya Yesu anati "Amene pochitidwa chipongwe sanabweza chipongwe,pokumva zowawa,sanaopseza,koma anapereka mlandu wake kwa iye oweluza molungama." (1peter 2:23).Uchete wa Yesu unachita chinachake mwa Petulo amene pano akutibetchera kuti titsatire chitsanzo cha Yesu.

Atsogoleri amene  amazidalira okha afunika kulankhula ndi mau komanso mokakamiza  pa kuziteteza okha.Koma atsogoleri omwe amadalira kuweluza kwa Mulungu atha kudikira mwachete kudikira kuweluza kwake.Atsogoleri otumikira amaonetsera kudalira mwa Mulungu pamene akhala chete pa kuziteteza okha.

Pali nthawi kodi yomwe mtsogoleri ayenera kulankhula pamene akuimbidwa mlandu?Yesu, patakhotha uchete uwu,analamulidwa ndi wansembe wamkulu kulankhula. Pamenepo analankhula modekha choonadi cha chomwe anali.Pali nthawi zina pomwe pali poyenera kulankhula poteteza chowonadi pa Ife eni.Koma Atsogoleri otumikira amangogwiritsa ntchito ufuluwu pomwe aphunzira kuwawa koziletsa kokhala chete.

Atsogoleri a chete  amalankhula ndi mau poziteteza okha !Atsogoleri otumikira  amakwezedwa potseka pakamwa pawo

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

Zoti tilingalirepo ndi Kukambirana.

1. Kodi ndine odzichepetsa kwenikweni kukhala chete pomwe akundiweluza mlandu molakwika?kodi chili mwa ine ndichani chomwe chimadzuka kufuna kuziteteza ndekha?

2. Mu nyengo ziti zamoyo zomwe ndikakhala chete ndikungodalira  Mulungu kuti anene zotsatira?Zotsatira zinali zotani?Ine sindinapangepo izi ,koma pali nyengo yomwe ndikhoza kutsatira Yesu pokhala chete?

3. Ndi munthawi iti yomwe ili yoyenera kwa ine kuzionetsa kuziteteza polankhula powonetsera zichitochito zanga?Ndingaziwe bwanji nthawi yoti ndilankhule kapena ndikhale chete?Kodi ndiyenera nditani  ndisanatsegule pakamwa panga?

4. Pali kusiyana pakati pa kuziteteza ndekha ndi kuteteza ena omwe akuzengedwa mlandu wabodza?Kodi ndingasiyanitse bwanji?

 

Nthawi ina tizaona kusankha Atsogoleri mu njira ya Mulungu.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2021

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online