Gawo #277, October 13, 2021

Phokoso la utsogoleri wachete......mu makopedwe onyengelera

Okondedwa Anzanga,ndikukhulupilira mulibwino!Kwa kanthawi,kuchokera pomwe m'bale wathu okondeka Joseph Saizi anamwalira,sitimatha kutumiza ziphunzitsozi za utsogoleri.Koma ndine okondwa kukudziwitsani kuti mkazi wake, Grace Saizi,wazipeleka kupitiliza kumasulira mu chichewa.Ndikuyamika chifukwa chofuna kugwira ntchitoyi kuti muthe kulandira ziphunzitsozi.Nambala yake ya email ndi gracekacheto@yahoo.com. Ya Whatsapp ndi +265884821937. Ngati muli ndi mafunso kapena mutafuna kulunikizana naye.Mulungu akudalitseni! Mwa iye, Jon Byler.

 

Atsogoleri amafikira ene powakopa monyengelera.Atha  kupangitsa ena kutsatira masomphenya awo,ndikukhala pambuyo pawo,ndi kukhala mbali ya gulu lawo.pafupifupi nthawi zones,timayesetsa kukopa ena ndi mawu,kawirikawiri ndi mau amphamvu kapena okwela omwe amathela ndi mfuuliro!koma nthawi zina chokopera wina chimabwela mwachete.

Petulo akuwuza akazi omwe ali ndi amuna osakhulupilira,(Akazi mu njira yomweyo mugonjere nokha kwa amuna nu kuti ngati wina wa Iwo sakhulupiliramau,akhoza kuwakopa popanda mau kudzela mu khalidwe la akaziwo,akawona chiyero ndi kulemekeza kwanu.(1Petulo 3:1_2))

Mmena zililimu,mamuna savomelezana ndi chikhulupiliro cha mkazi wake,chokhumba cha mkazi ndi chakuti akope mamuna Ku chowonadi .tikhoza kumupatsa uphungu oti apeze mfundo zothyakuka bwino kuti mamunayo azindikile kuti Mulungu alipo ndi  za kufunika kwa chipuumutso,ndi kumuwuza molimbamtima.Koma Petulo akupeleka uphungu oti akhalechete,mophatikiza ndi khalidwe la umulungu  zitengera kwa Mulungu mamunayo "opandamau".Atsogoleri otumikira phunzirani mphamvu ya makopedwe ndi Chete.

Makopedwe  a chete amaonetsela ulemu.

Petulo akulimbikitsa akazi kumvera " opanda mau".Kutsutsanamokweza mau zingaonetsele kupanda ulemu ndi kuthamangitsila mamunayo kutali.Koma mwakachetechete  mkazi asinthe moyo wake komanso asakakamize mamunayo kuvomelezana naye,zimaonetsera ulemu kwa iye ngati munthu.

Atsogoleri abwino amaonetsa ulemu kwa ena,makamaka Iwo amene sakugwirizana nawo.Amaonetsa ulemu kwa wina,nthawi zina pongopitiliza ubale popanda kukumbutsana za  kusagwirizana kwawo.Amadziwa kuti ulemu utsegula chitseko chakuwafikira.

Makopedwe a chete amaitanira kuzaonera pafupi.

"Azaona chiyero ndi kulemekeza kwa miyoyo yanu....." Uchete wa mkazi uzalora mamuna kuti awone!Uchete umaitanira mamunayo kuti acheuke ndikuwona zomwe mkazi wake akuchita,kuganiza kapena kuonetsera popanda mau.Mau amalimbikitsa anthu kuyang'ana pakamwa pathu kapena kuyang'ana kumbali,uchete umawalimbikitsa kutembenukira ndibkuonera pafupi.

Atsogoleri amakhalachitsanzo.Amalora miyoyo yawo kuti ilimbikitse owatsatira kubwela kuzaonera pafupi.

Makopedwe a mwakachetechete amasintha mitima.

Uchete wa mkazi kuphatikiza ndi kukhazikika mu khalidwe la bwino ,kukhoza "kutenga" mtima wa mwamuna.Mwamuna amayembekezera kufikiridwa ndi mfundo zotsutsa kwaiye kuti ngati akutsutsa abwezere mu njira yomweyo ndi kupambana nkhondoyo!Koma mmalomwake ,akupeza Uchete yekha,"chiyero ndi kulemekeza."Uchetewo sakuwuyembekezera ndipo ali ndi mphamvu zambiri,mapeto ake ,mphamvu ya Uchete imaphwanya kukana  kwake ndipo amavomerezana ndi mkazi wake.

Atsogoleri otumikira phunzirani,makamaka pamene pali kusagwirizana kuti kukhalachete  kuli ndi mphamvu yokopa.Atsogoleri otumikira azindikire kuti pomwe Mulungu akhoza kugwiritsa ntchito mau awo kubweletsa kusintha,iye akhonzanso kugwiritsa ntchito uchete wawo kusintha  mtima wa wina.Atsogoleri otumikira nthawi zina a mafikira  kudzera mu Uchete ndipo amaona Mulungu akusintha miyoyo.

Osalephera pali nyengo zambiri zimene atsogoleri amaitanidwa kupereka mfundo zawo ndi kukhala ndi mtsutso weniweni mwabwino pa chinachake.koma palinso nthawi zomwe atsogoleri angachite bwino potenga langizo la Petulo ndi kutsogolera kwa Chete.Atsogoleri otumikira amalira kwa Mulungu kuti awapatse nzeru zozindikira poti akope ndi mau,ndi pomwe Uchete  ndi kufikira koyenera.

Atsogoleri otumikira amalankhula mokweza mu Kukopa !Amakwela pamwamba potseka pakamwa!

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • kodi ndingaonetse bwanji ulemu kwa omwe akutsutsana nane?kodi ulemu wanga Unaonetseledwapo mwa chete?kodi pali nthawi zomwe uchete wanga sungalemekezedwe?
  • Kodi moyo wanga umalimbikitsa anthu kutsamilapo ndi kuonera pafupi, kapena kuchoka pa mfundo zanga?Kodi chotsatira ndi chani mu atsogoleri wanga?
  • Kodi ndili mu ubale ovuta pano omwe uli ndi kusamvana kwamphamvu?Ngati ndikutsogolera mwachete,kodi zilora Mulungu kusintha mtima wa munthu winayo?Kodi uchete ukhozanso kuchita mu mmoyo mwanga?
  • Mu njira yanji imene mfundo za mu ndimeyi kwa akazi omwe ali ndi amuna osakhulupilira akhonza kuchitira Ku maubale onse?Mu njira zanji zomwe mavesi awa sakuyenera kwa ena?Tingadziwe bwanji nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyenera kulankhula?
  • Pali njira ina yomwe kukhala chete kutha kukhala chida chomenyera mmalo chipangizo chakumufikira munthu? Kapena pali kusiyana  pakati pokana kulankhula ndi kusankha kukhala chete?

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2021

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online