Atsogoleri omwe amaphunzira kulandira chisomo cha Mulungu ndi kulowetsa chisomochi mmoyo wawo wa tsiku ndi tsiku ali okonzeka tsono kugawana chisomochi ndi ena. Pomwe akuchita choncho amakumbukira mawu a Paulo: ‘Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupilira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade. Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene iye adakonzeratu kuti tizichite (Aefeso 2: 8-10). Atsogoleri otumikira amakondwera mchisomo cha Mulungu cha kwa iwo. Amadabwa pa ukoma wake powaitana iwo kuti atsogolere ena. Ndipo amaphunzira kutanamphitsa chisomo cha Mulungu kwa omwe akuwatsogolera. Kodi atsogoleri otumikira amagawana bwanji chisomo ndi omwe akuwatsatira?
Atsogoleri otumikira amawonetsera masomphenya kwa owatsatira ndi chisomo
Pomwe atsogoleri otumikira ayang’ana pa owatsatira, samangowona chabe a ntchito omwe adzawathandiza kukwaniritsa masomphenya awo, amaona atsogoleri a mtsogolo mwa chisomo cha Mulungu! Amaona kuthekera. Amaona tsogolo. Samangowona zolephera. Amaona zomwe zingachitike ndi mphamvu ya chisomo. Amaona azimai ndi azibambo pomwe chisomo cha Mulungu chingagwirepo ntchito kuti akachite chomwe ‘adawakonzekeretseratu’ kuti akachite. Atsogoleri otumikira amaona ena kudzera mmaso a chisomo cha Mulungu.
Atsogoleri otumikira amayembekezera owatsatira kufuna chisomo
Atsogoleri otumikira aphunzira kuti akufunikira chisomo cha Mulungu mmiyoyo yawo, choncho sadabwitsika pomwe owatsatira akufuna chisomo! Amadziona okha ngati momwe Paulo adafotokozera mu chaputala chotsatira cha Aefeso: Umene adandikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene adandipatsa ine, monga mwa machitidwe a mphamvu yake. Kwa ine wochepa ndi wochepetsetsa wa onse woyera mtima adandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu (Aefeso 3: 7-8) Popeza atsogoleri otumikira aphunzira kupeza umunthu wawo mu chisomo cha Mulungu osati mu ntchito zawo, amayembekezera kuti owatsatira adzafunanso chisomo.
Atsogoleri otumikira amatanamphitsa chisomo kwa omwe amatsatira
Atsogoleri omwe sadakumanepo ndi chisomo cha Mulungu amavutika kuchita zabwino ndi mphamvu zawo. Amaziyeza okha kupyolera mkuchita kwawo. Ndipo amachita chimodzimodzi ndi owatsatira. Amaloza zala zotsutsa, chiweruzo ndi manyazi. Amawerenga buku lolemba momwe zinthu ziyenera kukhalira mokuwa ndi kulemba mzere kunsi kwa malamulo omwe aphwanyidwa! Samavomereza kulephera wawo. Atsogoleri otumikira amadziwa kuti akufunikira chisomo ndipo amatanamphitsa ichi kwa iwo omwe akuwatsatira. Atsogoleri otumikira samenya owatsatira awo ndi mndandanda wa ‘zoti muchite ndi zoti musachite’! samagwiritsa ntchito manyazi polamulira khalidwe la ena. Amaitana ena kuti awone chisomo chopambana cha Mulungu. Chisomo chimalola mtsogoleri otumikira kukhululuka zolakwika za otsatira. Chisomo chimalola mtsogoleri otumikira kunena, ‘ndikudziwa walephera, inenso ndinatero. Chisomo cha Mulungu chikuthandiza kuchita bwino.’ Chisomo chamalola mtsogoleri otumikira kupereka mwayi wachiwiri. Ichi sichitanthauza kuti palibe nthawi yomwe mtsogoleri ayenera kukonza, kudzudzula kapena kumasula wotsatira. Koma zikutanthawuza kuti liwu la pamwamba kwambiri lidzakhala lowonetsera chisomo. Popeza akudziwa kuti akufunukira chisomo, atsogoleri otumikira amaperekanso chisomo kwa ena. Atsogoleri otumikira amatsogolera ndi chisomo pogawana chisomo cha Mulungu. Kugawana chisomo kumawumba kopambana momwe timatsogolelera. Atsogoleri otumikira amaona utsogoleri monga iye wochimwa opulumutsidwa mwa chisomo, wotsogolera wochimwa wina yemwe akufunikira chisomo chomwecho. Atsogoleri otumikira amalandira chisomo cha Mulungu, amaphunzira kukhala mmenemo, ndipo kenako amagawana ndi omwe akuwatsogolera. Amakhala ngati Yesu, atsogoleri ‘odzala ndi chisomo.’
|