Atsogoleri otumikira amalandira chisomo monga momwe tidawonera mu gawo la mmbuyomo. Amavomereza kuti akusowekera chisomo ndi kuyamba ulendo wawo ndi Yesu. Ulendo umenewo umafunikira kuphunzira kukhala mwa chikhulupiliro. Monga momwe Paulo akutikumbutsa ife: ‘Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupilira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade. Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene iye adakonzeratu kuti tizichite (Aefeso 2: 8-10). Pomwe atsogoleri alandira chisomo cha Mulungu, amayamba ulendo ophunzira kukhala mwa chikhulupiliro. Amavomereza kuti ntchito sizingawapulumutse iwo, koma adalengedwa ‘kuti achite ntchito zabwino.’ Atsogoleri amakula kuti amvetsetse kuitanidwa kwa padeladela komwe Mulungu waapatsa kutsogolera omwe amawatsata ndipo amatangwanika ndi ntchito zomwe alinazo. Koma ayenera kuphunzira kukhala ulendowu mwa chikhulupiliro. Kodi atsogoleri otumikira amalora bwanji chisomo kuwawumba asadayambe kufuna kutsogolera ena?
Atsogoleri otumikira amalora chisomo kuwumba umunthu wawo.
Atsogoleri otumikira amapeza umunthu wawo mu zomwe Mulungu waapangira, osati zomwe iwo apangira Mulungu! Amaphunzira kukhala ndi chenicheni choti ‘ndi mwachisomo kuti mwapulumutsidwa.’ Amatsogolera ndi kutumikira chifukwa cha chisomo, osati kuti apeze chisomo! Ichi ndi chomwe chimapanga kusiyana konse momwe mtsogoleri amaonekera. Siudindo, dzina kapena zinthu zomwe tili nazo zomwe zimawumba umunthu wathu koma makamaka ndi chisomo cha Mulungu pa miyoyo yathu. Atsogoleri otumikira amapeza umunthu wawo mu chisomo cha Mulungu.
Atsogoleri otumikira amalora chisomo kuwumba utumiki wawo.
Atsogoleri omwe amakhala mwa chisomo amavomereza kuti ‘adalengedwa kukagwira ntchito zabwino.’ Atsogoleri amagwira ntchito molimbika. Koma atsogoleri otumikira amalora chisomo kuwumba utumiki wawo. Atsogoleri otumikira amaphunzira kuti utumiki wawo kwa Yesu ndi kutengapo mbali ku chisomo chake osati kukhala ndi malingaliro otsutsika, mantha kapena pongofuna kugwira ntchito! Amakhala ndi kutumikira mwa chisomo. Pomwe Paulo akupereka malangizo kwa mtsogoleri wachichepere, Tito, akuti, Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi (Tito 2:11-12) Zinthu zomwe atsogoleri otumikira amati ‘eya’ ndi zinthu zomwe amati ‘ayi’ zimawumbidwa mwa chisomo cha Mulungu. Samatumikira kamba kokhala ndi malingaliro otsutsika kapena kungoti poti ndi ntchito, amatumikira nkuvomereza ku chisomo cha Mulungu. Atsogoleri otumikira amaona ntchito zawo ngati kusefukira kwa chisomo cha Mulungu mmiyoyo yawo, osati chomwe chimakopa chisomo cha Mulungu. Atsogoleri otumikira amatumikira ambuye ndi mtima wonse, osati kamba kotsutsika kapena ntchito, koma chifukwa amamukonda iye ndi zomwe wachita mmiyoyo yawo.
Atsogoleri otumikira amalora chisomo kuwumba maitanidwe awo.
Paulo akukumbutsa atsogoleri kuti maitanidwe awo ndi kuchita ‘chomwe Mulungu adatikonzekeretseratu kuti tichite.’ Maitanidwe a mtsogoleri wotumikira kumatsanulika kuchokera mchisomo cha Mulungu, osati mzokhumba zawo zosintha dziko lapansi. Masomphenya a mtsogoleri wotumikira ndiko kuvomereza maitanidwe a Mulungu, osati kulira kwa munthu yemwe akufuna kulamulira. Kukhala mwa chisomo kumawumba moposa momwe timatsogolelera. Choyamba atsogoleri otumikira amaphunzira kukhala mchisomo cha Mulungu kuti akapeze kuchititsa pa ena. Amakonza nkhani za umunthu ndi maitanidwe pomwe akulingalira pa chisomo cha Mulungu. Kuyenerezedwa kwawo sikumatsamira pa zomwe akwaniritsa, koma pa chisomo cha Mulungu. Ichi chimawapanga iwo kulowa mu ntchito ya utsogoleri wawo motsimikizika koma modzichepetsa kwakukulu ndi kuzindikira chisomo cha Mulungu mmiyoyo yawo. Atsogoleri otumikira amatsogolera ndi chisomo poyamba pophunzira kukhala mchisomo cha Mulungu.
|