May 10, 2021

Okondedwa mwa Mbuye,

Landirani moni mu dzina la mphavu la Mbuye wathu Yesu Khristu amene ali wolamulira dziko lonse lapansi ngakhale tili mu nyengo yovuta.

Mwachisoni ndikukudziwitsani za imfa ya abusa a Joseph Saizi omwe sopano ali ndi Ambuye. Abusawa anatisiya pa 17 April, 2021 atadwala kwa nthawi yochepa. Abusa a Saizi anapereka nthawi yawo ndi mphavu zawo potanthauzira mawu a Mulungu m’chichewa kuyambira m’chaka cha 2016. Ndili ndi chikhulupiliro kuti mwakhala mukudalitsika nazo ngati owerenga. Ntchitoyi ayigwira opanda kulandira malipiro, kusonyeza mtima otumikira ndi cholinga choti inu owerenga mukadalitsike nazo. Ndikuyamika chifukwa cha moyo wawo komanso utumiki wawo. Tiyeni tikukumbukire mkazi wawo Grace ndi ana osiyidwawo.

Pachifukwa ichi, mwakhala musakulandira makalata kuchokera kwa ine kwakathawi sopano. Pachifukwa ichi pakhala povuta kutumiza mauthenga pokhapokha ngati wina atapezeka ozipereka kupitiliza utumikiwu. Kumasulira mauthengawa kumasowekera kuti munthu angakhale ndi compuyuta, kuthekera komanso kuzipereka pa masabata awiri aliyonse.

Ngati mkati mwanu mukumva kuti mukhoza kugwira ntchitoyi yankhulani ndi m’bale William Mbungo pa email iyi mbungo@crispmail.com kapena poyimba lamya pa numbala iyi  +265999603188.

Ambuye akudaliseni.

Jon Byler

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2021

Modify your subscription    |    View online