|
Atsogoleri Odzidalira Amavomelezela Zolakwitsa
Gawo #369, August 12, 2026
Atsogoleri amalakwitsa komanso omwe amawatsogolera amalakwitsa!Koma pali njila zambiri zomwe atsogoleri amatsatila akalakwitsa. Kuyankha kwawo kumaonetsa mulingo wawo wa kudzidalira ngati mtsogoleri. Nkhani ya Yosefe ndi yachitsanzo munjila zambiri. Pomwe abale ake a Yosefe anamugulitsa ku ukapolo, sikunali kulakwitsa kokha, komanso kuipa kwakukulu komwe anamuchitila Yosefe. Kubwezela kwake kwa iwo pomwe anaziulula yekha kwa iwo ndikofunikila.
Ndipo tsopano, musawawidwe mtima kapena kudzipsera mtima chifukwa choti munandigulitsa ine kuno, popeza Mulungu ananditsogoza ine kuti adzapulumutse miyoyo yanu. Kwa zaka ziwiri tsopano, kwakhala kuli njala mʼdziko muno, ndipo kwa zaka zisanu zikubwerazi, anthu sadzalima kapena kukolola. Koma Mulungu ananditsogoza kuti adzakusungeni ndi moyo ndi kuti mudzakhale ndi zidzukulu pa dziko lapansi. (Gen. 45:5-7).
Kayankhidwe ka Yosefe kwa abale ake kukusonyeza chisomo ndi chikhululukiro ndi kudzidalira kozama komwe analinako ngati mtsogoleri. Akuonetsela njira yomwe atsogoleri odzidalira amaonela zolakwitsa za ena.
Atsogoleri osazidalira amavomelezela zolakwitsa chifukwa amamvetsetsa udindo wawo kwa omwe amawatumikira
Yosefe anazindikira dzanja la Mulungu mu moyo wake ngakhale nkudzela kwa zolakwitsa za azichimwene ake. Akuona kuti "popeza Mulungu ananditsogoza ine kuti ndizapulumutse miyoyo yanu. "Anali odzidalira pomvetsetsa kuti cholinga cha Mulungu pa moyo wake ndipo amamvetsetsa kuti zolakwitsa za ena sizikanasintha chomwe iye anali kapena chimene Mulungu ankafuna kuchita ndi moyo wake. Udindo wake unapatsidwa ndi Mulungu ndipo siunali oti upindulire iye, koma kutumikira ena.
Atsogoleri osazidalira amaona zolakwitsa za ena ngati zokhudza mwachindunji udindo wawo ndi kulemekezeka kwawo. Pomwe zolakwitsa zachitika, amabweza poyang'ana zomwe akuganizila kuti ziwafikila. Koma atsogoleri odzidalira amachita zinthu motsamila pa chidaliro chomwe ali nacho kuti Mulungu athana nazo ndipo amazindikira kuti zolakwitsa za ena sizingakulitse kapena kuchepetsa maitanidwe awo a kutsogolera.
Atsogoleri odzidalira amavomelezela zolakwitsa chifukwa amalabadira za momwe iwo amene amawatsogolera amamvela.
Yosefe anadziwa kuti abale ake azunzika ndi kutsutsika komanso kudziphyela ntima iwo eni. Kotero akuwauza, "ndipo tsopano, musawawidwe mtima ndi kudziphyela mtima chifukwa munandigulitsa ine kuno. "Anali ozindikila bwino pa kuganiza momwe iwo amamvela, osati momwe iye amamvela. Yosefe mmalingaliro make munali tayale. Anali atathana ndi kuwawidwamtima kwake kwamkati ndipo tsopano anali ndi kuthekela kusamalira za ena.
Atsogoleri osazidalira amangoganizila za kuwawidwa kwawo kokha. Pomwe zolakwika zachitika, amatha kubwezela mwa mkwiyo, moonetsela kuipidwa, kapena moonetsa kunyoza. Amaonetsa momwe zolakwitsa za wina zimakhuzila chithunzi chawo. Koma atsogoleri odzidalira amaika chidwi chawo pa momwe yemwe walakwitsayo ndi kusamala za momwe iwo akumvela.
Atsogoleri osazidalira amavomelezela zolakwitsa chifukwa amafuna zabwino kuchokera kwa omwe amawatumikira
"Koma Mulungu ananditsogoza kuti azakusungeni ndimoyo ndikuti mudzakhale ndi zidzukulu padziko lapansi" Yosefe anakwanitsa kuika chidwi pa abale ake ndi momwe kulakwitsa kwawo kunawathandizila kupeza zosowa zawo, osati zosowa zake. Anaimabe pacholinga chotumikila ena ndi kukwanilitsa zosowa zawo, osati zake.
Atsogoleri osazidalira amaunguza zolakwitsa poyang'ana momwe zingakhuzile udindo wawo kapena malo awo. Koma atsogoleri odzidalira amakhala ndi chindunji pa zomwe zili zamtengo wapatali kwa omwe amawatumikira ndi kuvomeleza zolakwitsa ngati mwayi otumikila. Ngati munthu yemwe analakwitsa akufuna chilimbikitso, amalimbikitsa. Ngati akufunika kuunikilidwa, amaunikira. Ngati munthuyo akufunika kuti akumane ndi zotsatira zobwela chifukwa cha kulakwitsa kwake, amapanganso zimenezo, koma osati chifukwa cha mkwiyo kapena cholinga chobwezela koma pa chifukwa cha mtima wautumiki. Atsogoleri azidalira amafuna zamtengo wapatali kwa ena.
Zoti tilingalire ndi kukambilana
- Kodi ndinazipangitsa kulakwitsa motani? Kodi ndinakula ndi kufika pa muyezo oti ndimavomeleza zolakwitsa zanga ngati mbali ya ulendo wanga kapena ndimayembekeza ungwiro kuchokela kwa mwiniwakene? Kodi zimenezi zimakhudza bwanji machitidwe anga pomwe ena alakwitsa?
- Pomwe wina amene ndimamutsogolera walakwitsa, Kodi ndimaunguza chimenechi potsamila pa momwe zingakhuzile ine, kapena momwe zingakhuzile munthu yemwe analakwitsayo? Kodi zolakwitsa za ena zili ndichani pa momwe ndimazionela ndekha ndi udindo wanga?
- Pomwe wina wa pansi pa ulamuliro wanga walakwitsa, kodi kulephela kwanga kundipanga kukhala ndi chidwi pa kupsamtima kwanga kapena kwa munthu yemwe analakwitsayo? Kodi zimenezi zimakhudza bwanji utsogoleri wanga?
- Kodi pomwe amene ndimamutsogolera walakwitsa ndimaika chidwi kwambiri Poona zomwe ndimafuna kapena pa zomwe amafuna? Kodi zimenezi zimakhudza bwanji utsogoleri wanga?
Muphunziro lotsatilari, tiona momwe atsogoleri odzidalira amakuzila ena. |