|
Atsogoleri Odzidalira Amavomeleza Kusiyana
Gawo #368, July 1, 2026
Atsogoleri muutumiki amatumikira iwo amene amawatsogolera povomeleza kusiyana. Mmalo moti achite mantha ndi kusiyana, amaona kusiyanako ngati mphamvu. Gulu la utsogoleri la ku Antioch linali lodzadza ndi atsogoleri odziwikabwino odzidalila asanu.
Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.” Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza. Machitidwe A Atumwi 13: 1-3
Gulu limeneli linaonetsela momwe atsogoleri muutumiki anavomelezela kusiyana.
Atsogoleri odzidalira amavomelezela kusiyana chikhalidwe chifukwa zimapeleka kaonedwe kazinthu.
Gulu limeneli linabwela pamodzi kuchokera ku zikhalidwe zosiyanasiyana zodziwika. Barnaba anachokela ku chilumba cha Cyprus ndipo anali Muyuda koma ankalankhula chi Giriki. Simoni (dzina la chi Yuda) ndi Lusiyasi (dzina la chi Latini) anali a ku Afrika komanso ayenela anali okuda. Manaen anali wa chi Palestina ndi kuchokera kwa chi Giriki omwe anakula mkatikati mwa dziko lazandale mu Yudeya. Saulo, yemwe adzakhale Paulo, anali Muyuda ophunzila bwino ochokela ku Tarsusi. Gululi linali ndithu losakanikila- mtundu ndi losakanikila- zikhalidwe. Kusiyana kwawo kochokela zinawapatsa kusiyanasiyana kwa kaonedwe kazinthu komwe ankafuna kuti atsogolere mpingo omwe umakula ku Antiokeya omwe unali ndi anthu osakanikila Ayuda ndi Amitundu. Kusiyanasiyana kwawo kwa kochokela ndi kusiyanasiyana kwa kaonedwe kazinthu kunawapanga kukhala gulu lamphamvu. Pomwe panali kufunika koti wina akalankhule mu sinagoge wa Chiyuda, Paulo anali okonzeka. Barnaba amatha kulankhula chi Giriki. Manaem amatha kulankhula kwa andale amitundu ndipo Simoni ndi Lusiyasi amatha kulumikizana ndi olowamdziko amaiko ena. Kusiyana kumeneku kukadatha kupangitsa mikangano yachidziwikile, koma atsogoleri amenewa anali odzidalira bwino kuthana ndikusiyana kwa kaonedwe kazinthu komwe aliyense anabweletsa ku gulu lawo.
Atsogoleri osazidalira amaona kusiyana kwa kochokela ngati chiopyezo ndi chionongeko. Amayang'ana anthu omwe amaganiza ngati iwowo ndi kuona dziko chimodzimodzi. Koma atsogoleri odzidalira muutumiki amatumikira povomeleza zikhalidwe zosiyanasiyana.
Atsogoleri odzidalira amavomeleza kusiyana kwa mphatso chifukwa zimatulutsa chilimbikitso.
Panali mphatso zosiyanasiyana zomwe atsogoleri odzidalira amenewa analinazo, ena anali aneneli, ena anali aphunzitsi. Barnaba anali olimbikitsa, opeleka ndiponso mamuna wa chikhulupiliro. Anazindikira kufunika kobweletsa Saulo ku Antiokeya kuti azathandizile mpingo ongobadwa kumene( Onani machitidwe 11;19-26). Saulo anali wamasomphenya andondomeko. Pamodzi ndi ena, anali gulu lamphamvu chifukwa cha mphatso zawo zosiyanasiyana.
Atsogoleri osazidalira samakonzekelatu chivomelezo ndi chitsimikizo cha mphatso za ena. Amamva chiopyezo pomwe ena akuchita bwino zinthu. Koma atsogoleri muutumiki odzidalira amaona kusiyanasiyana kwa mphatso ngati chilimbikitso. Amazindikira ndi kuvomeleza kufunika komwe mphatso zina zimabweletsa. Amatumikila povomeleza mphatso zosiyanasiyana.
Atsogoleri odzidalira amavomeleza kusiyana maitanidwe chifukwa amatakasa luso
Pomwe gulu linali kulambila ndi kusalakudya zinaonetsedwa poyela kuti awiri anaitanidwa kuti apite. Pomwe anamumasula Barnaba ndi Saulo, anakhazikitsa kukula kwa mpingo kwatsopano ndi luso zomwe zikadapita ku dziko lodziwika!
Atsogoleri osazidalira sangaone wina mopitilira ntchito yomwe akugwila kapena kuona zazikulu zoposa iwowo ndi maitanidwe awo. Koma atsogoleri muutumiki amazindikila kuti maitanidwe osiyanasiyana amapangitsa kufalikila kwa luso. Amatumikira povomeleza maitanidwe osiyanasiyana.
Zoti tilingalire ndi kukambilana:
- Kodi kusiyanasiyana kwa mugulu langa ndi kotani kumbali ya kochokela? Mphatso? Maitanidwe? Kodi zimenezi zimakhuza bwanji kuchitabwino kwanga?
- Kodi ndimunjila ziti zomwe ndingalimbikitsile kaonedwe kazinthu kusiyanasiyana mugulu langa?
- Kodi ndinayeselapo kubweletsa pafupi anthu amphatso zomwe zili zofanana kapena zosiyana ndi zanga? Kodi zimenezi zinakhuza bwanji kuthekela kwa utsogoleri wanga?
- Kodi ndazindikila motani ndi kuvomeleza mphatso zosiyanasiyana zamugulu langa? Kodi ndingalankhule ndindani lero kuti ndionetse kuyamika kwanga chifukwa cha mphatso zomwe amabweletsa zomwe zili zosiyana kwambiri ndi yanga?
- Kodi kaonedwe kanga kazinthu kakhala kotani kwa iwo omwe maitanidwe awo ndi osiyana ndithu ndi anga? Kodi ndimantha kudalitsa ndi kumasula mphatso zimenezi munjila zomwe zimatulutsa upangili watsopano? Kodi ndindani wamugulu langa yemwe atha kukhala ndi kufunsa kuti atachita chinachake chatsopano ndi chosiyana? Kodi ndingawalimbikitse bwanji kutsatila kuitanidwako?
Muphunziro lotsatilari, tiona momwe atsogoleri odzidalira amavomelezela zolakwitsa. |