|
Atsogoleri Odzidalira Amapeleka Ntchito Kwaena
Gawo #367, May 20, 2026
Kupereka ntchito kuti ena agwile ndikovuta!sizophweka kupeleka mphamvu ndikupeleka mpata kuti ena agwile zomwe iwe umagwilanso. Komatu kupeleka ntchito ndi mbali yofunika ya mtsogoleri wamphamvu. Eliya akuonetsa momwe atsogoleri odzidalira amakwanitsila kupeleka mphamvu kwa otsatila awo.
Atawoloka, Eliya anati kwa Elisa, “Ndifotokozere, ndikuchitire chiyani ndisanachotsedwe pamaso pako?”
Elisa anayankha kuti, “Ndikupemphani kuti mundipatse magawo awiri a mphamvu za mzimu wanu wa uneneri.”
Eliya anati, “Wapempha chinthu chapatali, komabe ukandiona pamene ndikuchotsedwa pamaso pako, mphamvu wapemphayi idzakhala yako, koma ukapanda kundiona sizidzachitika. ”
2 Mafumu 2: 9-10
Eliya anali atamuphunzitsa Elisa kwa zaka 5 ndipo panthawi yakusinthanaku onsewa adadziwa kuti Eliya apita posachedwa. Kukambilana kwawo komaliza kukuonetsa kuti Eliya ankakwanitsa kupeleka ntchito chifukwa anali mtsogoleri odzidalira.
Atsogoleri odzidalira amapeleka ntchito kwa ena chifukwa amaika chidwi pa ena.
Funso la Eliya kwa Elisa ndilozama kwambiri, "Kodi ndikuchitile chani ndisanatengedwe kwa iwe? Eliya anali mneneli wamkulu ndipo anali ndi sukulu ya aneneli yomwe inkazindikila za ulamuliro ndi utsogoleri wake. Anamuitana Elisa ndicholinga choti azimuthandizila ntchito yake ndi kumutumikila. (Onani 1 mafumu 19: 19-21) Anali chi chifukwa chokwanilabwino choika chidwi paiyemwini pa nthawi yakunyamuka kwake, koma mmalomwake chidwi chake chinali pa Elisa! Anali odzidalira bwino pozindikila kuti dziko silimangothela pa iye yekha basi, panali ena omwe anamuitanila kuti awatumikire. Atsogoleri osazidalira amasowa chitsimikizo Cha chomwe ali ndi ulamuliro wawo. Amaona ena ngati njira yopezekelatu yomwe ikwanilitse zolinga zawo. Atsogoleri amenewa amafunsa, " Kodi mungandichitile chani? Atsogoleri muutumiki amafunsa, " Kodi ndingakuchitileni chani? " Atsogoleri muutumiki amaika chidwi chawo pa ena.
Atsogoleri odzidalira amapelekela ntchito kwa ena chifukwa amakhala ndichidwi pa kuchitabwino kwa ena.
Chopempha cha Elisa chinali " magawo awiri amphamvu za mzimu wanu. " Sanafune kuti angotengela moyo ndi cholinga kuchokera Eliya, koma kutenga mochuluka kawiri! Eliya anavomeleza kuti ichi "chinali chinthu chovuta" ndipo sichimayenela kukhala chisankho chochokela kwa iye momwe Mulungu akanamugwilitsila ntchito Elisa. Koma sanaophyezedwe ndi lingaliro la otsatila wake kuchita zomwe iye sanachite! Anali odzidalira mumaitanidwe ake ndi mbali yake ndipo anadziwa kuti palibe chomwe Elisa akanakwanilitsa chomwe chikanamutsitsa. Anakwanitsa kukhala wachindunji ndi kukondwela ndichipambano cha ena. Atsogoleri osadzidalira amakhala ndi chidwi pa kuchitabwino kwa iwo eni, osati kwa ena. Amaona otsatila omwe ali ndimphatso ngati chiopyezo ku udindo wawo ndi mphamvu zawo. Koma atsogoleri muutumiki amakhala odzidalira ndipo amasangalala ndi zomwe ena akwanilitsa. Amasiya kuzikweza kwawo ndi kuziyeneleza kwawo. Khumbo lawo ndi lowona ena akupambana ndipo amaika chidwi pa kuchitabwino kwa ena mmalo mwa iwo eni.
Atsogoleri odzidalira amapelekela ntchito kwa ena chifukwa amakhala ndi chidwi pa ozalowa pamalo awo.
Eliya anadziwa kuti watsala pang'ono kupita. Koma mmalo moti awone kuchoka kwake ngati chochitika choti anthu azalile maliro, anaona kuti ndimwai oti amukuze mumphamvu Elisa. Analibe nkhawa pozindikila kuti ntchito izapitilira kuchitabwino iye atachoka. Atsogoleri osadzidalira samaziona atasiya kutsogolera, asakuchita zomwe amatha bwino ndi kukonda kuchita. Saganizila zokonzekeletsa ena kupitiliza zinthu iwo atasiya. Amatenga nthawi yawo poika chidwi pa zokwanilitsa momwe angathele kuti awonetsele kufunika kwawo. Koma atsogoleri odzidalira amayamba ntchito ndi mapeto azinthu mmalingaliro awo, tsiku lomwe iwo sazakhalanso pamenepo. Ntchito yawo ndi yokonzekeletsa ena kupitiliza ntchito ndipo amatumikira pokhala ndi chindunji pa ozatenga malo. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti mulingo weniweni wa utsogoleri wawo umatsamila pa zozachitika mbuyo mwakuchoka kwawo.
Zoti tilingalire ndi kukambilana
- Kodi ndimadela ati omwe ndimavutika kupereka mphamvu kwa ena? Kodi zimenezi zikulankhula chani za mmene mtima wanga uliri ndi kudzidalira kwanga kapena kusowa kodzidalira?
- Kodi ndimawapempha mochuluka bwanji iwo amene amanditumikira" Ndingakutumikileni bwanji? "Kodi izi zimasintha bwanji machitidwe ku utsogoleri? Kodi ndindani wamugulu langa yemwe nditha kumufunsa funso ili mumasiku ochepa akubwelawa?
- Kodi ndingakondwelere bwanji zipambano za ena amugulu langa? Kodi ndindani yemwe wachita chinachake posachedwapa yemwe ndingamuyamikile pagulu?
- Kodi ndimunjila ziti zimene ndakonzekeletsa ena ku nthawi yomwe sindizakhalanso pa udindo wanga omwe ndilinawo pano? Kodi ndinjila zina ziti zomwe ndingatsate kuti ndikonzekele bwino ozatenga malo anga?
Mpaka nthawi ina, ine wanu wapaulendo,
Jon Byler
Muphunziro lotsatilari, tiona momwe atsogoleri odzidalira amathetsela kusiyana. |