|
Atsogoleri odzidalira ndi Atsogoleri Muutumiki
Gawo #365, April 22, 2026
Kodi ndinu odzidalira bwanji mu udindo Wanu wa utsogoleri? Nanga kudzidalira panokha ngati mtsogoleri kumatumikira bwanji ena? Mu mutu umenewu tiona mozama kusiyana pakati pa mtsogoleri odzidalira ndi osadzidalira ndinso kuzindikira chifukwa chomwe atsogoleri odzidalira ali atsogoleri muutumiki. Anthu ambiri omwe ali mu maudindo a utsogoleri sakhala odzidalira koma Yesu anasonyeza chitsanzo munjira yosiyana kwambiri.
Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo; anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake. Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake. Yohane 13: 3-5
Zambiri zinalembedwa za zomwe Yesu anachita pano, kutsuka mapazi a ophunzila Ake ndimadzi ndi kupukuta, ntchito ya otumikira. Koma mavesi omwe akupitilira zomwe akuchita zikuonetsela Mchitidwe wake wa utumiki kuyenda kuchokela muzinthu zitatu zomwe amadziwa zomwe zinampatsa kudzidalira ngati mtsogoleri.
Atsogoleri odzidalira amadziwa ulamuliro wao.
Yesu amadziwa kuti zinthu zonse zili "pansi pa ulamuliro wake. . . "Ankadziwa za mphamvu ndi ulamuliro omwe ananyamula ndi ophunzila Ake. Chifukwa anali odzidalira mu ulamuliro Wake, amatha kudzichepetsa kutsuka mapazi a ophunzila Ake. Machitidwe Ake muutumiki sanazimitse ulamuliro wake munjira iliyonse. Analibe chomwe akanaonetsa kapena kubisa.
Atsogoleri ena amakhala ndimantha kutumikila ena chifukwa amaopa kuti awoneka amphamvu zochepa. Amakhulupilira kuti atsogoleri amphamvu amakhala ndi owatumikira. Kotero, pomwe akupeza ena oti awatumikire, ndipomwe amakhulupilira kuti ndi atsogoleri amphamvu. Uku ndikuonela pansi komanso kusokoneza momwe utsogoleri uliri! Atsogoleri muutumiki amakhala otsimikizika ndipo amazindikira, monga Yesu kuti ali pa malo a ulamuliro ndicholinga chopanga ena kukhala ofunika ndi kuwatumikira. Atsogoleri muutumiki amagwilitsa ntchito ulamuliro wawo chifukwa cha ena, osati iwo eni. Izi zimachitika pamene ali odzidalira mu ulamuliro omwe alinawo.
Atsogoleri Odzidalira amadziwa kuti iwo ndindani
Yesu amadziwa kuti ubale wake ndi Atate Wake anali maziko a ulamuliro wake ndipo kuti "anachokera kwa Mulungu. . . "Anali odzidalira pa chomwe Iye anali. Udindo wake mu utsogoleri sunasinthe chomwe anali munjila ina iliyonse. Amatha kutsuka mapazi koma osasintha chomwe Anali.
Atsogoleri osazidalira pazochitika zawo kapena mau amafunsa ena, "Kodi simudziwa kuti ine ndindani? Ine ndi wapampando, wamkulu wa kampani, kapena m'busa!" Amafuna kuoneka ndi kuzindikilika kuti ndi anthu ofunika ndipo amaona kuti udindo wao wa utsogoleri ngati chopangitsa iwo kukhala apamwamba. Amapeza kudziwika kwawo kuchokela ku udindo wawo ndipo sangatumikire ena chifukwa zitha kuoneka ngati zochepetsa chomwe ali. Koma atsogoleri osazidalira sakhala achidwi pa chomwe ali ;amakhala ndichidwi pa chomwe ena ali- ndi kufunafuna kumanga ndi kulimbitsa omwe amawatsogolera. Safuna kuti awonetsele chomwe ali;ndi otsimikizika mu chomwe ali. Kotero kuti alibe vuto kutumikila ena.
Atsogoleri odzidalira amadziwa tsogolo lawo
Yesu ankadziwa kuti "azabwelera kwa Mulungu." Anamvetsetsa kuti cholinga chake chenicheni sichinali chomangililika ku udindo wake wa utsogoleri. Kotero, kutumikila ena sikungasinthe tsogolo Lake.
Atsogoleri ena amakhala ndimantha kutumikila ena chifukwa amaopa kuti ngati atapeleke mphamvu ndi kukuza ena, asowa choti azichita!Amakhala ndi mantha kuti atumukire chifukwa sali otsimikizika za tsogolo la iwo eni.
Koma atsogoleri muutumiki amakhala otsimikizika za tsogolo lawo. Amazindikira kuti utsogoleri wawo siwaiwo okha kapena zomwe angapeze kuchokera mu utsogoleri. Ali muutsogoleri ndicholinga chotumikila ena ndipo amatumikira chifukwa ndichinthu choyenera, osati chifukwa chazomwe angapeze kuchokera mu zochita zawo.
Ngati mtsogoleri odzidalira, Yesu anatumikira. Atsogoleri odzidalira ndi atsogoleri muutumiki.
Zoti tilingalire ndi kukambilana
- Kodi ndine odzidalira bwanji ngati mtsogoleri? Kodi chizindikiro chomwe ndimachiona muutsogoleri wanga ndichiti?
- Kodi ndimagwiritsa ntchito udindo wanga wautsogoleri kuti ndionetsele mphamvu zanga ndi ulamuliro wanga? Munjira ziti?
- Kodi pali njira zimene chimene ndili chagwilizana ndi udindo wanga wautsogoleri? Kodi chingachitike ndichani momwe ndimaonela zinthu lero nditasiya udindo wanga kapena malo anga?
- Kodi ndimakhalapo ndimantha oti kutumikila ndikupatsa mphamvu ena zitha kundipangitsa kuti ndikhale osowa chochita chaphindu? Kodi zimenezi zikukhudza bwanji utsogoleri wanga?
Mumaphunziro otsatilawa tidzaona zomwe atsogoleri odzidalira amachita, tiyamba kuona pa momwe atsogoleri odzidalira amalimbikitsira. |