|
Khrisimasi Yopambana!
December 24, 2025
Okondeka Nzanga,
Chisomo ndi mtendele kwa iwe nyengo ino ya Khrisimasi. Ndikufuna kukufunila iwe - ndi omwe umawatumikila- chikondwelero chopambana cha Khrisimasi.
Pomwe ndikulingalira za kubwela kwa Yesu kuno kudziko lathu, ine ndilinso odzadzidwa ndi kuzizwa pa kukongola kwa kwa malingaliro a Mulungu. Kubadwa kwake kunaoneka ngati kwachibwanabwana ndi kwawamba, koma pomwe kunali kukwanilitsidwa kwa mauneneli omwe ananenedwa zaka mazanamazana zambuyo. Yesu analowa mudziko ngati Mfumu ndipo anapembezedwa moyenela. Koma chonsecho, Iye "Sanabwele kudzatumikilidwa, koma kuzatumikila, ndi kuzapeleka moyo Wake ngati chiombolo kwa ambiri" (Maliko 10: 45).
Kuchokela pa chiyambi penipeni, moyo Wake unazondotsa kumvetsetsa kwathu kwa utsogoleri. Ngakhale pano, ndikupitilira kulimbama ndi kukhala moyo weniweni wa utsogoleri otumikira mu moyo wa tsiku ndi tsiku. Khrisimasi ikutiitanila mwapang'onopang'ono ku kakhalidwe kameneko-kodzichepetsa, kokhulupilika, ndi kodzipeleka.
Chakhala cha mwai kuyenda limodzi nanu pambalipa, ngakhale munjila mochepa, kudzela mu ziphunzitso za kamozi pa masabata awili aliwonse. Zikomo pomazilandila ziphunzitso zimenezi mumoyo wanu, pomazilingalira, ndi pomagawananso ndi ena.
Ndilinso othokoza kozama kwa omwe amatumikila kuseli kwangaku. Linda Boll wakhala akumapanga editi ziphunzitso zimenezi kwazaka zambiri, ndipo ndili othokoza chifukwa cha ntchito yake yoonetsetsa ndi Gabriel Madrazo ndi Grace Kacheto mwaulele amapelekela nthawi yao kumasulira zolembedwazi mu chi Spanishi ndi Chichewa, kuchulukitsa kufikila ena patali zomwe sindikanatha kupanga pandekha. Mtendele wa Khristu udzadze mitima yanu mu Khrisimasi imeneyi, ndipo chaka chikubwelachi chikhale chokutengelani chifupi ndi Iye pomwe mukutumikila mokhulupilika pamalo pomwe wakuikanipo.
Ine wanu chifukwa cha Iye, |