|
Tiyeni Tilankhule Zandalama: Zifunefuneni
Muphunziro lapitali tinaona momwe atsogoleri muutumiki amapelekela ndalama zawo, poziona kuti ndi adindo oyang'anila zachuma zomwe zinapelekedwa mmanja mwao. Mfundo ya chiwili yomwe imatsogolera atsogoleri muutumiki munkhani zokhudzana ndi ndalama ndi zokhudzana ndi momwe amazipezela, kapena momwe mumapezela ndalama. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti popanda ndalama, sangakwanilitse zolinga zawo. Amazindikira kuti kukhala mdindo oyang'anila kwawo kumafunika udindo oganizila bwino za momwe ndalama zao amazipezela. Atsogoleri muutumiki amafuna ndalama kuti atumikile nazo ena. Ntchito zake ndimonga zabungwe, anthu a mugulu mwamwo, anthu owafikila, mavenda, ndi mudzi wao. Pomwe akuganizila za kupeza ndalama, amaganizila zamavesi ngati awa:
Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa. Miyambo 21: 6
Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu, koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi. Miyambo 14: 23
Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma, ukhale ndi nzeru ya kudziretsa. Miyambo 23: 4
Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse. Yakobo 5: 4
Mavesi amenewa, ndi ena, akuonetsa kuti pali njira zolondola komanso zolakwika zopezela ndalama ndi kukhazikitsa mfundo zotsogolera za momwe atsogoleri muutumiki amapezela ndalama.
Atsogoleri muutumiki amapeza ndalama pogwila ntchito bwino. "Kugwila ntchito molimbika kulikonse kumabweletsa zotsatila. . . "Atsogoleri muutumiki sakhala ndimantha a kugwila ntchito molimbika! Ndiofuna kupeleka nthawi ndi khama lomwe limafunika kuti apeze ndalama. Atsogoleri ena amagwilitsa ntchito udindo wao kuti asagwile ntchito, pokhulupilira kuti utsogoleri ndi kuuza ena kuti agwile ntchito. Koma atsogoleri muutumiki amamvetsetsa kuti amatsogolera bwino pogwila ntchito bwino. Amapeleka chitsanzo kwa ena ndikuzipeleka kwawo kogwila ntchito molimbika. Amaganiza ndi kupanga madongosolo a zachuma ndi zitsankho zomwe zimasowekela kugwila ntchito molimbika kuti zikwanilitsidwe. Amagwira ntchito ndicholinga chokhazikitsa mchitidwe wa umunthu pazachuma mubungwe lawo …
Atsogoleri muutumiki amapeza ndalama pobalansa bwino. Atsogoleri muutumiki amagwila ntchito molimbika komanso ali ndi "nzeru ya kudziketsa. "Atsogoleri ena samaleka kugwila ntchito molimbika pomwe ali mkati mosaka ndalama. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti kulumikizana pakati pa kugwila ntchito molimbika ndi phindu zitha kuwatengela ku kukhumudwa mwachangu kotero amaphunzila mmene angaonetsele kudziketsa. Amapeza njira zonenera kuti "zakwana" ndipo ngati ndi nthawi yakwana yoti asiye amachoka mu ofesi ndi kuthimitsa lamya yawo yammanja kapena makina a kompyuta yawo. Zimenezi zimawapatsa mpata okhala ndi nthawi yopezeka pabanja pawo, kupezeka muzochitika kuonjezelanso kufunika koti achite zolimbitsa thupi lawo ndi kugona. Chifukwa amazindikila okha ku
Atsogoleri muutumiki amapeza ndalama pokhalabwino ndianthu. Atsogoleri muutumiki amatumikila mabungwe awo pomakhala nao bwino anthu omwe ali mubungwemo. Atsogoleri ambili amaona anthu awo ogwila ntchito mongoti basi angowapangila phindu ndipo sakhudzika ndi za miyoyo yawo. Koma atsogoleri muutumiki amawalemekekeza omwe amagwila nao ntchito ndipo amakana kupanga ndalama kudzela mwaiwo. Amafunafuna kulipila malipilo omwe ali abwino kwinaku akulondela nkhani zachuma mwangwiro za bungwe. Atsogoleri muutumiki amamvetsetsa kuti kukhalabwino ndianthu makamaka kumabweletsa kupangaphindu kwa bungwe pochulukitsa kagwilidwe ntchito kao ndi zotulutsa zawo.
Zoti tilingalire ndi kukambirana
-Kodi moyo wanga ndichitsanzo chabwino cha kugwila ntchito molimbika? Ndimunjira iti yomwe chimenechi chimabweletsela zotsatila mu utsogoleri wanga? -Kodi ndinakhazikitsa njira zoyenela zachitezo mubungwe langa zotetezela ine ndi enanso kumayeselo ndi kulimbikitsa ugwiro mu Zandalama? Ngati sichoncho, kodi ndikufunika nditapanga chani? -Ndimunjira ziti zomwe ndimakhala ndi chiyeso chogwila ntchito mowonjeza? Kodi zimenezi zimabweletsa zotsatila zotani mu maubale anga ndi banja, anzanga ndi thanzi la ine mwini ndi kakhalidwe kanga? Kodi ndikufunika kusintha pati msabatai kuti ndiyambe kuonetsa kuziletsa? -Kodi anthu omwe ali pansi pa utsogoleri wanga ndingakhale nawo bwino motani? Kodi ndine olowamanja kwa iwo monga mofunikila? Kodi ndipati pomwe sinditha kupeleka phindu la ndalama kwa iwo, kodi ndimayang'ana njira Zina zomwe ndingawalemekezele ngati anthu ndi kuona kuti akulandila chisamaliro chabwino? -Onani mavesi owonjezela awa okhudzana ndi zachuma ndi adindo oyang'anila: Miyambo 1: 19, 6: 10-11, 13: 11; Luka 14: 18, 16: 9-11;Yakobo 5: 4; 2 Atesalonika3: 6, 10, 12. Kodi tikuphunzilapo Zina ziti zokhudzana ndi momwe timachitila pa nkhani zandalama ngati mtsogoleri muutumiki?
Muphunziro lotsatilari, tizaona mmene atsogoleri muutumiki amapelekela ndalama. |