|
Tiyeni Tilankhule Zandalama: Zipelekeni
Gawo #362, November 26, 2025
Atsogoleri muutumiki, ngati atsogoleri ena onse, amapanga nkhani zandalama tsiku lina lililonse. Zisankho zimafunika kuti zichitike zomwe zimakhudzana ndi ndalama mu ntchito zonse zapamoyo wamunthu komanso zokhudza utsogoleri. Atsogoleri muutumiki amawumba kuganiza kwawo ndi kupanga ziganizo kwawo pankhani zokhudzana ndi ndalama pogwilitsa ntchito chikhumbokhumbo chotumikira ndi kudalitsa ena. Mu mutu uwu, tiona mfundo zokhazikika zitatu zomwe zimatsogolera atsogoleri muutumiki momwe amaonela ndalama ndikupanga zisankho zokhudza ndalama. Mfundo yoyambilirayo ikuoneka yovuta kumvetsa koma ndiyofunikila kwambili-atsogoleri muutumiki amazipeleka ndalamazawo! Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti ndalama zomwe amazilamulira sizawo, iwo amangochita mongoyang'anira. Onani mavesi awa:
‘Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanganso, ’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. Hagai 2: 8
Komanso udzafanizidwa ndi munthu amene ankapita pa ulendo, ndipo anayitana antchito ake nawasiyira chuma chake. Mateyu 25: 14
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi. Mateyu 6: 24
Atsogoleri muutumiki amalakalaka kutsata mfundo zimene zikupezeka muzimenezi ndi mumalemba ena ofanana ndi amenewa popeleka ndalama zao.
Atsogoleri muutumiki amapeleka ndalama pozindikula udindo wao oyang'anila.
Haggai molimbamtima analengeza kuti Mulungu ndi mwini wake odziwikilatu wa chuma chonse. Mufanizo la matalenti Yesu akuphunzitsa kuti amapeleka zinthu kwa wina aliyense payekha payekha kuti aziyang'anile mmalo mwake. Kaonedwe kameneka kamasintha momwe atsogoleri muutumiki amaonera ndalama, kuti sizawo, iwo ndi ongoyang'anira chabe.
Atsogoleri ena amatengeka ndi ndalama -kuzitenga, kuzisunga, ndikunjoya nazo. Chidwi chawo ndi chamkati, ndipo amapanga ziganizo zawo zokhudzana ndi ndalama potsamila pa phindu lomwe angazipangile okha. Koma atsogoleri amapeleka ndalama, amazindikira kuti ali muutsogoleri ndicholinga chotumikira ena. Izi amapanga ngakhale pa ndalama zoti ndizawo kapena zabungwe. Pomwe akupeleka ulamuliro pokhala oyang'anila, amamva ufulu wamtima okhutitsidwa.
Atsogoleri muutumiki amapeleka ndalama pozindikila utsogoleri wawo.
Kwa omwe amaona udindo wawo kukhala oyang'anila amapeza kumasuka komanso udindo-ogwilitsa ntchito ndalama zomwe awadalila nazo. Atsogoleri ambili amagwilitsa ntchito utsogoleri wao ndicholinga chopeza ubwino kwa iwo eni, chidwi pa zomwe ziwapindulire ngati munthu. Koma atsogoleri muutumiki anamvetsetsa kuti monga oyang'anila, ndalama zomwe akuyang'anilazo zili ndi cholinga chapamwamba kuposa phindu kapena chopezapo, chimenechi ndi cholinga chotumikila bungwe ndi kulingalira zokhumba za Mulungu ndi masomphenya. Akadali kuitanidwabe pacholinga chotsogolera ndi kugwilitsa ntchito ndalama munjira yomwe mwini wake akufuna, ndipo amatumikila mabungwe awo potenga udindo oyang'anila bwino ndalama.
Atsogoleri muutumiki amapeleka ndalama pozindikila mayeselo awo.
Yesu akuchenjeza za mphamvu yoophya yomwe ndalama itha kubweletsa mmoyo mwathu. Ndalama ndithudi itha kusanduka mulungu wathu. Atsogoleri ambili amalora ndalama kukhala ndi ulamuliro onse mu moyo wawo ndipo amachitha chilichonse kuti azikhalabe ndi zambili. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti chikondi chapandalama chitha kuwatengela kutali ku kutumikira mwabwino banja lawo, mmidzi mmwawo, ndi mmabungwe. Amapeleka ndalama ndicholinga choti atsogolele mwangwiro, modzichepetsa ndi kuyang'anila kuti zichitile ubwino omwe amawatumikilira.
Zoti tilingalire ndi kukambirana:
- Kodi ndakhala ndikuziyang'ana motani ndalama komanso zinthu zobweletsa ndalama, ngati mwiniwake kapena oyang'anila? Kodi zabweletsa motani kusiyana mu utsogoleri wanga?
- Pomwe ndikutsogolera ndikupanga ziganizo zokhudza ndalama, kodi ndimaonetsela mtima ozikonda kapena otumikira? Kodi ndingapeleke chitsanzo chanji cha chisankho chomwe ndapanga msabata yapitayi chowonetsela zimenezi?
- Ndimunjira ziti zomwe ndalama imandipatsa mayeselo ofuna kuleka kutumikira? Kodi ndimachita, kapena ndingachite bwanji kuti nditchinjilize mtima wanga motsutsana ndi chimenechi?
- Onani mavesi otsatirawa okhudzana ndi zachuma ndi udindo: masalimo 50: 10, Mateyu 25: 14-30;Luka 12: 42-48. Kodi ndizinthu zina ziti zomwe mukuphunzila za momwe mumachitila nde ndalama ngati mtsogoleri muutumiki?
Muphunziro lotsatilari, tiona momwe atsogoleri muutumiki amapezela ndalama. |