|
Timoteo: Kuphunzila kumenya nkhondo
Gawo #361, November 12, 2025
Atsogoleri onse amamenya nkhondo_ koma sionse atsogoleri amadziwa nkhondo zoti angamenye kapena kuti angawine bwanji nkhondo. Paulo anamupatsa Timoteo malangizo a momwe angatumikile wena pomenya nkhondo yopambana ndi kuwina nkhondo zoyenela.
Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo utagwiritsitsa chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino. Ena anazikana zimenezi motero chikhulupiriro chawo chinawonongeka. 1 Timoteyo 1: 18-19
Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa. Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. 1 Timoteyo 6: 11-12
Ena mwa malangizo a Paulo opita kwa Timoteo kuti atsutsane ndi chaumunthu cha mtsogoleri yemwe wakumana ndinkhondo. Koma atsogoleri muutumiki mosamalitsa omaonela pa zomwe Timoteo anaphunzira kwa Paulo ndi momwe anaphunzilira kumenyankhondo potenga njira yolondola ndi pa nthawi yoyenela.
Timoteo anaphunzira kumenyankhondo pobwelera ku chiyambi
Paulo analimulimbikitsa Timoteo kuti akumbukire "chikumbumtima chabwino" ndi mauneneli omwe ananenedwa za iye. "ndicholinga choti powakumbukila uthe kumenya nkhondo bwino. . . "Timoteo anaphunzira kumenyankhondo polingaliranso zomwe zinachitika zomwe zikanamuthandiza kuti akhalebe muzomwezo. Ankafunika kuti akumbukire kuti iyeyo ndindani, nchifukwa chani anaitanidwa, masomphenya omwe analinao potumikila monga mtsogoleri. Pomwe analingalira chiyambi, amatha kupeza yankho lenileni la nkhondo zoti angamenye ndi njira yoenela kutsata.
Atsogoleri ena akakumana ndinkhondo amathawa mmalo moti abwelere ku chiyambi. Ena amathamanga mwachangu kukamenya nkhondo koma amasowekela chofunika kwambili chomwe chimabwela polingaliranso masomphenya awo. Amathamangira munkhondo opanda kulingalira kuti iwowo ndindani kapena ndichifukwa chani akutsogolera. Atsogoleri muutumiki pokumana ndinkhondo iliyonse amamenya choyamba pobwelera kuchiyambi!Amabwelera mbuyo ku malo komwe amapeza kukhazikika ndi mphamvu. Amalingalira pa komwe akuchokera ndi komwe akupita. Amalingaliranso za cholinga chao chachikulu. Kenaka ndi chitsimikizo chabwino cha cholinga ndi chindunji, atha kumenya nkhondo.
Timoteo anaphunzira kumenyankhondo pothawa.
Paulo analimbikitsanso Timoteo kumenyankhondo pothawa"ku zonsezi"!Sizimaoneka ngati kulimbamtima kupewa nkhondo, Koma Timoteo anaphunzira kuti nkhondo zina munthu amapambana pozithawa!(onani mfundoyi)Ankafuna kuti asinthe kuchoka kumadela a mayeselo ndi zifooko.
Atsogoleri ena amayesetsa kumenya nkhondo iliyonse. Amangoyambapo basi kukhulupilira kuti ngati pali nkhondo, iwo atsogolere ndikupambana. Koma atsogoleri muutumiki amathawa nkhondo zina ndipo amapeza chigonjetso popewa zinthu zomwe zinawatengela ku njira yolakwika.
Timoteo anaphunzira kumenyankhondo potsatira.
Pa nthawi yomwe Paulo akumupempha Timoteo kuti athawe zinthu zina, akumuuzanso Timoteo kuti "tsatila"ena. Timoteo amaphunzila kumenyankhondo potsatira chomwe chinali chabwino ndi cholondola. Pomwe akathamangira kuzinthu izi, analimbikitsa kuthekela kwake kwa utsogoleri ndipo anali okwanitsa bwino kutumikira iwo amene ankawatsogokera.
Atsogoleri ena saphunzira samatsatila zolinga zoyenera. Amakhazikika pa zipambano zanthawi yochepa ndi kuchitabwino kwachangu. Amaika chipambano chawo pa"chiyambi" mmalo mwa chimaliziro. Koma atsogoleri muutumiki amamenyankhondo ndicholinga chazotsatila zapamwamba ndi zochita zomwe zizabweletsa chipambano chachikulu kwa omwe amawatumikilira.
Timoteo anatumikila bwino pomenya nkhondo bwino. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kutumikira omwe ali pansi pawo podziwa nthawi yobwelera kuchiyambi, yoyenela kuthawa, ndi nthawi yoyenela kumenyankhondo potsatira.
Zoti tilingalire ndi kukambirana
- Kodi ndingaphunzire bwanji kuthamanga kunjila yoyenela pomwe ndakumana ndinkhondo za muutumiki? Kodi ndikufunika kubwelela kuchiyambi paziti zomwe zingawathandize kuti ndiyimebwino? Kodi ndikufunika kuthawa zinthu ziti? Kodi ndizinthu ziti zomwe ndikufunika kutsatira? Kodi chimachitika ndichani pomwe ndikutsatira ndisanabwelere mbuyo kapena kuthawa?
- Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi ndingachite chani kuti ndiwalimbikitse kuti akweze kuthekela kwawo komenyankhondo bwino? Kodi ndikufunika kuwakumbutsa ena kuti abwelere ku maziko awo? Kodi pali njira zomwe ndikufunika kuwalimbikitsa kuti athawe madela awo a zifooko? Kodi ndingawaitanile bwanji agulu langa kuti athamangire zomwe zili zabwino?
- Poonjezela kumavesi omwe tagwilitsa ntchito muphunziro limeneli, onani mavesi otsatirawa: 1 Timoteo 1: 18, 6: 6-11, 20-11; ndi 2Timoteo 2:22. Kodi ndimfundo ziti zoonjezela zomwe mukupeza mumavesi amenewa za momwe Timoteo amamenyela nkhondo pothawa?
Pomwe tikumalizitsa mutu uwu wa moyo wa Timoteo, ndikufuna ndilemekeze ntchito yaikulu ya omwe amatumikila amagwila ntchito yonseyi kuti muzilandila ziphunzitso zimenezi!Milonica Stahl-Welt ndi Linda Boll omwe amaonetsa luso lawo lokonza mofunika kukonza kuti ma email akhale apamwamba. Ndi Brian Drewery yemwe amapanga zonse zokhudzana ndi tekinoloje kuti zimenezi zizipezeka pa website ndi kuti zikupezeni Inu. Ntchitozi zikutheka chifukwa cha ambili omwe, monga iwo, amatumikila kuseliku!
Ngati mwasangalala ndi ziphunzitso zimenezi, dinani apa kuti mulandile maphunziro onse pamodzi.
Muphunziro lotsatilari, tiyamba kuona mutu wa mtsogoleri muutumiki ndi ndalama. |