|
Timoteo: Kukhala Wachitsanzo
Gawo #357, August 20, 2025
Timoteo anaphunzira koyambilira kuti kudzitsogolera yekha kumabwela asanakhale otsogolera ena. Asanaitane ena kuti atsatire, anayenela kukhala wachitsanzo pa njirayo. Onani mavesi awa:
1 Timoteyo 4
7 Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu.
1 Timoteyo 4
12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
1 Timoteyo 4
15 Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo. 16 Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.
Muchaputala chimenechi Paulo analimbikitsa Timoteo kuti akhale chitsanzo kwa omwe amawatsogolera, kuti "onetsa chitsanzo"kwa ena. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti utsogoleri ndi ntchito yamkati. Atsogoleri muutumiki asanauze ena amaonetsa kaye momwe zimayenela kuonekera. Pomwe Timoteo anatsatira malangizo a Paulo anakhala chitsanzo munjira zambiri zosiyanasiyana.
Timoteo anaonetsela kusungamwambo
Paulo anapeleka malangizo kwa Timoteo, "uziphunzitse wekha kukhala mwaumulungu. "Kuti atsogolere ena Timoteo ankayenela kukhala mtundu wamunthu woyenela_ wa umulungu. Izi sizikanatheka popanda chindunji ndi kusunga mwambo. Anthu opanga pulakatesi masewelo othamanga amayenera kuonela Kwa atsogoleri awo mmene akuchitila posungamwambo. Mwambo wamapulakatesi utha kukhala ovuta ndi otopetsa. Pali masiku ambiri omwe ochita masewelo othamanga amafuna atangokhala pa bedi kusiyana ndi kupita kukapanga mapulakatesi.
Atsogoleri ambiri amafuna kuti awoneke ngati atsogoleri amphamvu, koma sakhala ofuna kupeleka dipo la tsiku ndi tsiku limene limafunikira kuti akhale amphamvu. Amayang'ana njira zachidule zoti ziwathandize kutsogolera ena popanda kuzipititsa patsogolo machitidwe a Iwo eni. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti kusungamwambo ndiko dipo loti akhalire mtsogoleri wachitsanzo. Amakhala ofuna kupeleka dipo asanayesele kutsogolera. Amazipatsa mwambo okha kuti akhale munthu yemwe ndi oyenera asanafunefune kutsogolera ena.
Timoteo anaonetsa kukhala opatulika
Paulo analimbikitsa Timoteo kuti agonjetse chobetchela chokhala mtsogoleri wachichepele pokhala wachitsanzo kwa ena. Timoteo sakadasintha zaka zake, koma amatha kupanga zinthu zoti akhale munthu wachichepele okhwima kupambana onse ozungulira. Amakwanitsa kuzisiyanitsa yekha kuchoka ku khwimbi la ena amsinkhu wake pokula mu "kalankhulidwe, machitidwe, mchikondi, muchikhulupiliro ndi muchiyero. "Timoteo anaoetsela kupatulika, kuima padela kuchoka muchikhamu ndi kudzuka pamwamba pa chikhamu.
Atsogoleri ambiri amafuna kukwezedwa chifukwa cha udindo wawo ndi ulamuliro. Atsogoleri muutumiki amalakalaka kukhala apamwamba osiyana ndi ena kuti akhale pa anthu a zaka zosiyanasiyana. Pomwe akupanga izi amakhala okwima kwambili koposa a zaka zawo ndipo amatumikira ena ngati chitsanzo chopatulika.
Timoteo anaonetsa chitsanzo chakhama
Paulo anaitanira Timoteo ku khama " kuti aliyense awone kuti ukupita mtsogolo. " Timoteo anaphunzira kuti kukula kumafunika khama. Pomwe chinali chinthu chabwino kuti akhale mtsogoleri wachitsanzo wachichepele ankasowekela kuti akhale akukula mopitilira zomwe mwachidziwikile zimayenela zikhale motero kwa omwe amatsata moyo wake.
Atsogoleri ambiri amasiya kukula pomwe akuona ngati afikapo pokwanitsa kuchita ntchito. Koma atsogoleri muutumiki amakhala akhama kuti apitilize kukula munjira zomwe zimakhala chitsanzo kwa omwe awazungulira.
Zoti tilingalire ndi kukambirana:
· Kodi ndi dela liti la moyo wanga lomwe sindili chitsanzo chabwino kwa ena? Kodi ndingachite chani msabatayi kuti ndiyambe kuchitabwino mudela limeneli?
· Kodi ndimaonetsa kusintha kopitilira mmoyo mwanga ndi utsogoleri wanga zomwe ndi zachiziwikile kwa omwe andizungulira? Ngati sichoncho, Kodi ndikusoweka nditasintha pati?
· Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi ndingachite chani kuti ndiwalimbikitse kuti akhale achitsanzo kwa Iwo owazungulira? Kodi ndimunjira ziti zomwe ndingawavomeleze ndi kuwalimbikitsa omwe ali achitsanzo pakadali pano?
· Poonjezela kumavesi omwe tinagwilitsa ntchito muphunziro lino, onani mavesi otsatirawa: 1 Timoteo 2: 6; 2 Timoteo 1: 13-14; ndi 2 Timoteo 2: 16, 22. Kodi ndimfundo ziti zoonjezela zomwe mukupeza kuchokela mumavesi amenewa zowonetsa momwe Timoteo anaitanidwira kukhala wachitsanzo ndi magawo eni eni omwe amayenera kuti awonetse ena njira. |