|
Timoteo: Kuphunzila kudziletsa
Gawo #356, August 6, 2025
Pomwe anali kukula mukuthekela kwake kwa utsogoleri imodzi mwanjila zomwe Timoteo anayenela kuphunzila ndi mchitidwe odziletsa. Onani malangizo awa ochokela kwa Paulo opita kwa mtsogoleri wachichepele:
2 Timoteyo 1
3 Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga.
4 Ndikamakumbukira misozi yako, ndimalakalaka nditakuona kuti ndidzazidwe ndi chimwemwe.
2 Timoteyo 2
25 Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi. 26 Motero nzeru zawo zidzabweramo, ndipo adzathawa msampha wa mdierekezi, amene anawagwira ukapolo kuti azichita zofuna zake.
2 Timoteyo 2
16 Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera.
1 Timoteyo 4
7 Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu.
Ndime zimenezi zikuonetsa madela atatu amene Timoteo anaphunzira kudziletsa
Timoteo anaphunzira kubweza mkwiyo wake.
Paulo akukumbukira misonzi ya Timoteo ndipo akumupempha kuti azilangiza"mofatsa"pomwe angakakumane ndi yeselo loti atulutse mkwiyo. Chisoni ndi mkwiyo ndi ziwiri za momwe mtsogoleri aliyense amachitila pa zinthu zomwe amakumana nazo. Paulo sakudzudzula Timoteo kamba ka momwe amachitila, koma modekha akulimbikitsa kudziletsa, chimodzi mwa zipatso za Mzimu (onani Agalatiya 5: 22-23). Mkwiyo kapena utha kukhala chimodzi mwa zinthu zomwe ndi zowononga kwambili kwa atsogoleri. Palibe munthu yemwe amafuna kutsatira mtsogoleri yemwe sangathe kubweza kupsyamtima ndipo kulephela kuzibweza mudela limeneli zaletsa kuchita bwino kwa atsogoleri ambiri. Kupsyamtima kosagwilika ndi chiophyezo ku utsogoleri.
Koma atsogoleri muutumiki amazindikira ndi kuzibweza momwe amachitila pa zinthu. Sachitamantha kuonetsa misonzi yawo ndipo amaphunzila kusunga mkwiyo wawo pokana kuononga zinthu. Amazindikira kuti sangatumikile ena pomwe ali osaugwila mtima.
Timoteo anaphunzira kugwira lirime lake.
Taona kale kuti malangizo a Paulo kwa Timoteo oti azilangiza otsutsana naye "mofatsa.” Paulo anazindikila kuti zimafunika kudziletsa kwakukulu kuti munthu akalankhule modekha pomwe pali mtsutso okulunjika! Lirime kawirikawiri limaonetsa mkwiyo wamumtima polankhula ndipo silingatsogolere ku kulapa komwe kumalimbikitsidwa ndi lirime lodekha. Paulo akumuchenjezanso Timoteo za "mchitidwe opanda umulungu. . . zikhulupiliro zopanda umulungu ndi nthano zanchembele zakale. . . . " Apa akungotanthauza kuti mau opandapake ndiosathandiza. Pomwe mau olankhulidwa chifukwa cha mkwiyo chachiziwikile amakhala oyipa, malankhulidwe ena amakhala osathandiza ndipo Paulo akumuchenjeza Timoteo kuti azibweza lirime lake ndicholinga chopewa kulankhula kwamtundu umenewu. Atsogoleri ambiri ali ndi malirime omwe ali osapanganika ngati nyengo ndipo ndi oipa kwambili mmalo mothandiza. Koma atsogoleri muutumiki amafunafuna kudziletsa pa zomwe zimabwela kuchokela mkamwa mwawo kuti zisazakhale zowononga koma zothandiza nthawi zonse.
Timoteo anaphunzira kuongolela nthawi yake
Mbali ya malangizo a Paulo kwa Timoteo kuti "apewe nkhani zopanda pake" ndi " nthano zanchembele zakale" ndi kumuuza kwa chindunji koti azigwilitsa ntchito nthawi yake bwino. Apa ndi mmalo enanso Paulo anauza Timoteo kuti akhale wachangu pakuika chidwi chake pa nthawi ndi kukhala tchelu kuzinthu zofunika ndikupewa zowononga. Munthawi zina Paulo anauza Timoteo kuti " bwela mwachangu" pomwe munthawi zina asakhale "ndiphuma"( onani 1 Timoteo 5: 22 ndi 2 Timoteo 4: 9). Timoteo anayenela kuphunzila kukhala osunga nthawi yake bwino. Ngati malangizo awa akanapelekedwa lero tingathe kumva Paulo akuti, "osataya nthawi yako pa nkhani zopanda pake ndi pakutsatila zachisawawa za pa masamba amchezo!" Atsogoleri ambiri amalola za zii zanthawi ino zomwe zimawalepheletsa kagwilitsidwe kabwino kanthawi yawo. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kutsatira ndandanda wa zoti achite ndicholinga choti achite zinthu zomwe zimabwletsa phindu ku omwe amawatumikira.
Zoti tilingalire ndi kukambirana_
- Kodi pa magawo atatu awa(Kupsyamtima, lirime, nthawi) ndiati omwe ali ovuta kwaine kwambili kudziletsa pakadali pano? Lingalirani pa funso liri mmunsimu lokhudza dela limenelo:
- Kupsyamtima Kodi ndiliti lomwe ndinalephela kubweza ukali muutsogoleri wanga ndipo zinakhudza motani ubale wanga ndi ena?
- Lirime Kodi ndimagwilitsa ntchito motani lirime langa munjira zomwe zisali zothandiza kwa omwe ndimawatsogolera? Kodi ndingachite chani kuti ndilore Mulungu andithandize kwatunthu kuti ndikhale odziletsa mudela limeneli?
- Nthawi Kodi zomwe zimanditaitsa nthawi zazikulu ndi ziti? Kodi ndingachite chani kuti ndithe kukhala odziletsa mudela limeneli?
- Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi ndingawalimbikitse motani kuti athe kuyamba kudziletsa okha moposa muyezo omvela uphungu wakunja? Kodi pa madela atatuwa ndi dela liti lomwe ndizilikamba ndi atsogoleri anga?
- Poonjezela kumavesi omwe tinagwilitsa ntchito muphunziro lino, onani mavesi otsatirawa: 1 Timoteo 5: 22; 2 Timoteo 2: 4;4: 2, 9-12, 21. Kodi ndi nfundo zina ziti zoonjezela zomwe mukupeza kuchokela mumavesi amenewa owonetsa kuti Timoteo anaphunzilira kudziletsa?
Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Timoteo anakhalira chitsanzo kwa ena.
|