Timoteo: Kulipila Dipo la Utsogoleri
Gawo #351, May 14, 2025
Timoteo anali wa njala yofuna kuphunzila koma anazindikiranso kuti kukula muutsogoleri kumabwela modula. Anali ofuna kupeleka dipo lomwe linkafunika kuti limuumbe kukhala mtsogoleri wamphamvu yemwe akanadzakhala mtsogolo. Onani malemba awa okhudza zamoyo wake:
Machitidwe a Atumwi 16
3 Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mʼderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki.
2 Timoteyo 1
7 Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga. 8 Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu.
1 Timoteyo 4
12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
Mavesi amenewa, ndi ena ambiri, akuonetsa za dipo lomwe Timoteo amayenera kuti apeleke kuti akhale mtsogoleri yemwe tikumusilira lero.
Timoteo anapeleka dipo la kuzipeleka kwatunthu.
Asanasiye khomo lake, Timoteo adaphunzira kuti utsogoleri si okhudzana ndi Iye komanso siokhidzana ndi moyo wamtebelele koma umakhudzana ndi kukhala okonzeka ndi ofuna kutumikira ena. Ululu wa mdulidwe unali opyola kuthupi, unkatanthauza kuti anali ofuna kupeleka moyo wake wabwino ofewa chifukwa cha iwo amene ankafuna kuti awatumikire. Pamene anthu azikamionela pansi chifukwa cha unyamata wake, azikapereka chikhumbokhumbo chake ndi kubwezamoto nkulengeza chomwe ali. Timoteo amaphunzila phunziro lapachiyambi lomwe atsogoleri onse muutumiki pakadutsa nthawi amazaphunzira_pamtima pa utsogoleri ndi nkhalidwe wa mtima ofuna kuzipeleka kwatunthu. Atsogoleri ena sali ofuna kusiya zokhumba zawo, maloto awo, ndi kuzikundikila kwawo chifukwa cha iwo amene amawatumikira. Koma atsogoleri muutumiki amapeleka dipo la kuzipeleka kwatunthu, osati kamodzi koma tsiku lirilonse.
Timoteo analipilira dipo la kufikila madela ena
Pomwe Timoteo adavomela kumujoina Paulo, chinali chinthu chatsopano chokondweletsa koma mbali Ina chinali chamtengo wodula. Kuyenda kufikila mizinda yatsopano sizinali zinthu zongotopetsa zokha, makamaka pamene anawathamangitsa mtauni ndi myala! Ulendo umenewu unali oti Timoteo afikile madela ena ndi kukula munjira zomwe sizikanakhala zamoyo ofewa.
Ankayenela kuti asunthe ndi kulowela madela ena ndikusiya moyowabwino wa panyumba pake ndi malo obadwila. Ankafunika kuti "asakhale wamantha " kuti akhale mtsogoleri olimba. Ankatha kufikila madela ena kuchoka pabwino pomwe anali ndi kukumana zobetchela zatsopano komanso milingo yaikulu ya udindo pomwe anali kukhwima ali pansi pa chitsogozo cha Paulo. Ankatha kupeleka dipo la kuphunzila kulandila chidzudzulo ndi uphungu zomwe Paulo anapitilira kupeleka ngakhale ngati mtsogoleri okwana bwino. Ankafunika kufikila pena mmachitidwe ake kuti akhale chitsanzo cha ena.
Atsogoleri ena amafuna udindo ndi ulamuliro opanda kukhala kufuna Kulipila dipo lofikila madela ena mu kukula kwa iwo eni. Koma atsogoleri muutumiki amavomeleza kuti utsogoleri ndi ulendo wa kukula kopitilira ndi kutukuka. Atsogoleri muutumiki amaika chidwi pa kuzifikitsa madela ena asanauze ena zochita.
Timoteo anapeleka dipo lozunzika.
Timoteo anapeleka dipo lozunzika kuthupi ndipo anaikidwa mundende nthawi ina. (Onani Ahebri 13: 23) Koma anavutikanso pamodzi ndi Paulo pamene anali kusautsidwa munthawi zambiri. Anazunzika pakusiyanitsidwa ndi banja lake, kusakhala moyo wabwino pa kuyenda kwake kopitilira, ndi kumusumila milandu yabodza. Kawirikawiri, ankazunzikanso kuthupi. (Onani 1 Timoteo 5:3).
Ambiri amabwelera mbuyo kusiya utsogoleri akakumana ndi mazunzo ndipo amapanga chiganizo chotsata njira yotsika mtengo. Koma atsogoleri muutumiki amavomeleza kuti kuzunzika ndi dipo la utsogoleri ndipo kumagwila ntchito yolimbitsa makhalidwe awo ndi kuwapanga kukhala ochitabwino mukutumikila ena.
Zoti tilingalire ndi kukambirana
- Kodi ndi dipo lotani lomwe ndapeleka kale kuti nditsogolele? Kodi pali ndondomeko Zina zomwe nditsatire ngati mtsogoleri zomwe zakhala zikuoneka zodula kwambili kuti ine ndizitsate? Kodi zifunika ndiziti kwa ine kuti ndikhale ofuna kupeleka dipo? Angandithandize ndani kuti ndipange chimenechi?
- Kodi ndi munjira ziti zomwe ndalolera kupeleka zikhumbokhumbo zanga, maloto kapena kuzikundikila kwanga musabatayi? Kodi zimenezi zikhudza bwanji utsogoleri wanga?
- Kodi ndi munjira ziti zomwe ndikupititsa madela ena kuthekela kwanga ngati mtsogoleri? Kodi pali kufunika kosintha?
- Kodi ndikakumana ndi mazunzo muutsogoleri wanga ndizitani nanga Kodi izi zizikhudza bwanji kukula kwanga?
- Kodi ndingachite chani kuti ndithandize omwe ndimawatsogolera kuti akhale ofuna kupeleka dipo la utsogoleri?
- Poonjezela ku mavesi omwe tinagwilitsa ntchito muphunziro lino, onani mavesi otsatirawa; 2 Timoteo 2: 3, 3:12, ndi 4:5. Kodi ndi nfundo zina ziti zoonjezela zomwe mukupeza kuchokela mumavesi amenewa za momwe Timoteo analipilira dipo la utsogoleri wake?
Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Timoteo anafotokozela bwino za maitanidwe ake. |