Kusankha Kwa Utsogoleri Kwa Paulo: Atsatileni
Gawo #347, March 19, 2025
Atsogoleri muutumiki amapatsa mphamvu ena ndipo amakhala okondwa kuona anthu akukula ndi kumasulidwa, koma sakhala akhungu ku chofunika cha kuyankha. Pomwe Paulo ankagwira ntchito ndi Timoteo ndi ena mu kasankhidwe kake ka utsogoleri, anawamasula, komanso anawatsatira ndi cholinga choti awonetsetse ngati amayenda munjila yoyenela. Munthawi yake yoyambilira ya kukula kwake Timoteo ankamutsatira Paulo, kukhala ndi kugwilira ntchito pamodzi. Kenako, Paulo anamasula Timoteo kuti akakhale m'busa wa ku Efisasi. Timoteo tsopano ankatsogolera pa Iye yekha koma Paulo sadamusiye yekha. Paulo adamutsatira, polemba makalata Kwa Timoteo omwe ankapeleka kuyankha koyenela ndi chitsogozo.
1 Timoteyo 4: 15-16
15 Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo. 16 Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.
Timoteo munthawi imeneyi anali payekha koma sanali yekha. Paulo ankapitiliza kumpatsa upangili ndi uphungu pa ulendo wake wa utsogoleri. Ndipo zinali zopindula!
Afilipi 2: 22
22 Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha, chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake.
Atsogoleri muutumiki amaphunzila phindu lotsatira omwe amawapatsa mphamvu kuchokela kwa chitsanzo cha Paulo.
Kutsatira atsogoleri kumabweletsa udindo oyang'anira.
Paulo anazindikira kuti Timoteo "wafika pokuphsya." Izi zikusonyeza kuti panali nthawi ya mayeso ndi kusiyanitsa kwa mulingo kwa utsogoleri wake pomwe anali kukula pansi pa chitsogozo cha Paulo. Paulo anamumasula Timoteo kuti akatsogolere pa iye yekha koma anaotsetsa kuti anali akumuyang'anilabe pa ntchito yomwe ankagwira.
Atsogoleri ena amawamasula omwe ali pansi pawo ndi kutengapo udindo ochepa kapena osatengapo udindo. Ena amangopeleka maudindowa kwa ena koma chidwi chimakhala chochepa kwambili pa zomwe mtsogoleri oyamba kumeneyo akupanga. Atsogoleri muutumiki munjila yopambana amaonetsetsa kuti kupeleka mphamvu ndi kuyang'anira zikuyendela pamodzi bwinolomwe. Amamasula, koma osamutaya, mtsogoleri oyamba kumene. Amatsatira pokhala oyang'anira komwe kuli kofunikila malinga ndi mulingo wa utsogoleri yemwe amumasulayo.
Kutsatira atsogoleri kumafulumizitsa kukula
Kutsatira mtsogoleri oyamba kumene moyenelera kumafulumizitsa kukula kwawo!Tate muzimu amakhalà ndi kuthekela komufotokozela zochitika za moyo ndi nzeru munjira zomwe zimathandiza mtsogoleri wachichepeleyo kuti aziyenda chitsogolo mwachangu pa maulendo apaokha a utsogoleri. Timoteo akadatha kuphunzila zinthu zina pa iye yekha kudzela munjila yongoyeselera. Koma Paulo ankamutsatira Timoteo kuti afulumizitse kukulako.
Ankayembekezela kuti aliyense awone Timoteo "akupita patsogolo." Atsogoleri ena amamasula ena ndi kuyembekezela kuti aphunzire pa iwo okha. Atsogoleri muutumiki amatsatira Iwo amene akuwakuza kuti atakase kapena afulumizitse kukula wawo.
Kutsatira atsogoleri kumatulutsa atsogoleri apamwamba ndi abwino.
Chotsatila cha Paulo kukhala tate munzimu mopitilira mumoyo wa Timoteo chinali "choti Timoteo wafika pokuphsya." Kasankhidwe ka utsogoleri ka Paulo kanatulutsa mtsogoleri weniweni yemwe ankayenda ndi Paulo monga mwana. Zotsatila ndi zoti Timoteo anali mtsogoleri wapamwamba_ kwambili. Atsogoleri ena amamasula ena kuti akhale pa Iwo okha ndipo amakhala ndi chiyembekezo cha zamwamba. Atsogoleri muutumiki amapitiliza kutumikira iwo amene akuyamba kumene pomawatsatira kuti atsimikize zotsatila za pamwamba.
Zoti tilingalire ndi kukambirana
- Kodi ndili ndi mtsogoleri wachikulire kapena Tate yemwe amanditsatira kuti awone momwe ndikupangira muulendo wanga wa utsogoleri? Ngati ndichoncho, kodi ndingachite chani kuti ndionetse kuyamika kwa iwo lero pa zomwe aikiza mumoyo wanga? Ngati sichoncho, kodi ndindani yemwe ndingamupemphe kuti azindiyan'gana pakukula kwanga muutsogoleri ndipo ndiliti lomwe ndizayankhule Kwa Iwo za izi?
- Kwa atsogoleri omwe ndikuwakuza, kodi mchitidwe wanga ndi owamasula koma osamawayan'ganira kapena kuwathandizilako pang'ono? Kodi ndikufunika ndisinthe pati kuti ndichite mwamulingo oyenela?
- Kodi ndinakhalapo ndi zokambilana zokhudza malire a kuyang'anira ndi omwe ndimawamasula kuti amuke akagwire ntchito zosiyanasiyana? Kodi ndikumabwezako mulingo wa kuyang'anira omwe umayembekezeka pomwe atsogoleri a pansi panga akukula ndi kuumbika?
- Kodi ndimachita chani kuti ndionetsele kwa omwe ndimawatsogolera kuti pomwe aima paokha, sali okha?
- Kodi ndi atsogoleri amtundu wanji omwe akukula pansi pa chitsogozo changa? Kodi ndingaphunzirepo chani kuchokela Kwa Paulo kuti nditulutse atsogoleri amulingo wapamwamba?
Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Paulo anasankhila atsogoleri ake powalimbikitsa. |