Gawo #344, January 22, 2025

Kusankha Kwa Utsogoleri Kwa Paulo: Apatseni Mphamvu

Paulo mosamala anasankha omwe akanamutsatila, mwadaladala anawakonzekeletsa ku ntchito yomwe anawapatsa, ndipo anagwilitsa ntchito chitsanzo cha moyo wake ndi utsogoleri wake kuti awaonetse mmene angatsogolere. Ndondomeko zonsezo zinaika maziko oti Paulo ayambilepo pokuza kuthekela kwa utsogoleri mwa Timoteo ndi enanso omwe anali mugulu mwake Kenaka Paulo anapeleka mphamvu kwa Timoteo ndi ena kuti akuze kuthekela kwa utsogoleri paokha. Onani mau awa omwe analembedwa munthawi yomwe Paulo anali pafupi kufa ndipo atatha zaka 20 ali pa ubale ndi Timoteo.

2 Timoteyo 4

1 Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa omwe pamene adzaonekera ndi ufumu wake, ndikukulamula kuti: 2 Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa. 5 Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya mlaliki, gwira ntchito zonse za utumiki wako.

Paulo anampatsa mphamvu Timoteo kuti agwile ntchito zambiri za utsogoleri. Ndipo pansi pa utsogoleri wake Timoteo anakula nkukhala mtsogoleri wampingo, othana ndi mavuto, ndi othandizana kulemba makalata 6 omwe anazakhala mabuku. Chitsanzo cha Paulo chikutionetsela kuti atsogoleri muutumiki amagawana mphamvu, ali mu ulamuliro ndicholinga chopatsa ena mphamvu. Zotsatilazi zikuzilankhulira zokha.

Kupatsa mphamvu atsogoleri kumachulukitsa ukadaulo

Paulo akubetchela Timoteo kuti "alalikile, akonze, adzudzule..." Anali ataonetsela kale Kwa Timoteo ntchito zimenezi kuti achite chimodzimodzi. Paulo sanangokhala ndi chidwi chokhala ndi munthu omuthandiza kukwanilitsa cholinga chake; ankafuna kuti Timoteo akul. Kuti kukula kuchitike, Timoteo ankafuna mpata oti atambasule mapiko ake ake, kutsogolera payekha ndi kulakwitsa payekha. Paulo samachita mantha ndi kukula kwa Timoteo Iye pokhala mtsogoleri. Anali ndi cholinga choti Timoteo akule ndi kukhala waluso mu ntchito yake.

Atsogoleri ena amafuna kukhala okha omwe angagwire ntchito. Amaopyedwa kuti wina atha kukwanitsa kugwira kapenanso mwabwino kuposa iwowo. Koma atsogoleri muutumiki amafuna amafuna kuona aliyense akupatsidwa mphamvu kuti mwaluso lawo agwiritse ntchito kuthekela kwawo.

Kupatsa mphamvu atsogoleri kumachulukitsa anthu

Chifukwa Paulo anapatsa mphamvu gulu lake, ankatha kuchulukana. Pomwe Paulo anatsala pang'ono kuyamba ulendo wake wa utumwi, anakwanitsa kupita ku Athens kusiya Sila ndi Timoteo mbuyo mu Berea ndi Tesalonika. Atatsala pang'ono kuti alembe mau awa Paulo anauza Timoteo kuti apeleke Kwa ena zomwe anaphunzila kwa Iye(onani 2 Timoteo 2:2). Pompatsa mphamvu Timoteo, Paulo anakhudza unyinji wa mibadwo wa atsogoleri.

Atsogoleri ena amasakasaka kukuza gulu lawo powonjezela anthu oti agwile ntchito. Atsogoleri muutumiki amafunafuna kukuza anthu awo powapatsa mphamvu. Pomwe akuchita izi, amachulukitsa anthu.

Kupatsa mphamvu atsogoleri kumachulukitsa mphamvu

Pomwe Paulo analemba mau awa Timoteo anali ku Efisasi, kutsogolera mpingo omwe Paulo anadzala kumeneko. Paulo anazindikira kuti kupeleka mphamvu sikunanyozetse mphamvu yake koma inachulukitsidwa. Popatsa mphamvu Timoteo ndi ena Paulo anachulukitsa mphamvu yake.

Atsogoleri ena amakhulupilira kuti kupatsa ena mphamvu kuchepetsa mphamvu yao,kotero amagwilitsitsa ku mphamvu yawo ndi ulamuliro wawo. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti pomwe akupatsa mphamvu ena, mphamvu imachulukitsidwa.

Zoti tilingalire ndi kukambirana:

  • Kodi ndi ndani mugulu langa yemwe ndili naye cholinga pompatsa mphamvu kuti akule ngati mtsogoleri? Kodi chitsanzo cha Paulo chikundiuza motani kuti ndichulukitse Iwo amene angachite zomwe ndikuchita?
  • Kodi ndintchitobyanji yomwe ndikuchita pano yomwe wina wake mugulu langa akanatha kuchita kapena kuchita? Kodi nditsate ndondomeko ziti kuti munthu ameneyo ndimpatse mphamvu ndipo ndizachita liti zimenezi?
  • Kodi ndapatsa mphamvu atsogoleri ondizungulira mokwanila bwino kuti ndizaone phindu la utsogoleri wina obwela pomwe ayambe kupatsa mphamvu ena? Ngati ndi choncho, Kodi ndapatsa mphamvu motani kuchuluka uku? Ngati sichoncho, kodi ndingachite chani muchaka ichi kuti ndiyende motsalira izi?

Mpaka nthawi Ina,ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Dzina la Timoteo likuonekela monga othandizana kulemba pa 2 Akorinto, Afilipi, Akolose, 1 Atesalonika, 2 Atesalonika, ndi Filimoni.

Muphunziro lotsatirali, tizaona momwe Paulo anasankhila atsogoleri powaongola.

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Leaders Serve and Jon Byler. Copyright, 2025

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online