Gawo #343, January 8, 2025

Kusankha Kwa Utsogoleri Kwa Paulo: Awonetseni

Tinaona momwe Paulo anasankhila ndi kukonzekeletsa Timoteo, mmodzi mwa atsogoleri atsopano mugulu lake. Pomwe Paulo ankamuitana Timoteo kuti ayendele limodzi pa ulendo wa utsogoleri, ankayamba ndondomeko yadaladala yomuonetsa Timoteo kuti angatsogolere motani. Ankayenda limodzi, kugwira limodzi ntchito ndikukhala limodzi. Kudzela mu chitsanzo chake, Paulo amamuonetsa Timoteo kuti utsogoleri ndiotani. Patapita zaka, pomwe moyo wake unali pafupi kutha, Paulo analemba mau awa Kwa Timoteo otsimikiza kuti anali atatsiliza ntchito yake:

2 Timoteyo 3

10 Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga, 11 mazunzo anga, masautso anga.

Patapita zaka zambiri Paulo anatha kunena Kwa Timoteo kuti wamuonetsela zinthu 9 za moyo wake. Moyo wa Paulo unali buku lotsegula kwa Timoteo. Anaonetsela mbali zabwino ndi zowawa za utsogoleri. Ndi othekela kumuuza Timoteo kuti ankadziwa chilichonse Cha Iye ngati mtsogoleri. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kwa chitsanzo cha Paulo kufunika koonetsa omwe akuwatsogolera zabwino ndi zowawa za ulendo wa utsogoleri.

Atsogoleri muutumiki amaonetsela njira

Zinthu zina zokhudzana ndi utsogoleri zimafunika malangizo ndipo Paulo analankhula za "chiphunzitso changa." Koma Paulo anapyola mulingo wa malangizo nkufika pa chionetselo. Anamuonetsela Timoteo "njira ya moyo wake." Podzela pa chitsanzo chake anaonetsa Timoteo njira yodzalira mipingo mu madela achilendo, njira yomwe angatsogolere munyengo zovutitsitsa, njira yothana ndi kusiyana, njira yokuzila atsogoleri atsopano, ndi zina zotero. Paulo anamvetsetsa kuti kuthekela kochuluka kwa utsogoleri ndipomwe munthu wachigwira chinthu kuposa kuphunzitsidwa. Atsogoleri ena amauza ena zoti achite osawaonetsela momwe angachitile. Koma atsogoleri muutumiki amaonetsa ena; amakhala achitsanzo. Zimenezi sizikutanthauza kuti atsogoleri muutumiki azigwira okha ntchito iliyonse, koma amakhala ofuna kugwira ntchito ndi manja awo ndi kuonetsela gulu lake momwe amachitira. Amazindikira kuti kukuza atsogoleri ena kumafunika kuwaonetsera mmene zimachitikira.

Atsogoleri muutumiki amaonetsela cholinga

Paulo pokhala chitsanzo Kwa Timoteo sizinali pa zochotika za kunja kokha ayi, koma cholinga chake. Anakwanitsa kumuuza Timoteo kuti "amadziwa cholinga changa." Cholinga cha Paulo chinali mau oti 'chifukwa' kumbuyo kwa mau oti 'chiyani' Timoteo mosakaika anamva mwakawilikawili nkhani ya kutembenuka mtima kwa Paulo, ya kuitanidwa Kwa moyo wake ndi chapamtima pake chofikira dziko la amitundu. Timoteo anathandiza Paulo kulemba buku la Akolose pomwe Paulo akuti cholinga chake ndi "kupanga aliyense kuti akule kwatunthu mwa Khristu" (Akolose 1:28.) Paulo anafotokoza momvekabwino Kwa Timoteo chifukwa chimene ankapanga zomwe amapangazo. Atsogoleri ena amangoonetsela momwe ntchito ingagwilidwile. Koma atsogoleri muutumiki amafotokoza cholinga cha ntchitoyo ndi kumangilira zochotika zonse za utsogoleri ku masomphenya kapena cholinga cha bungwe.

Atsogoleri muutumiki amaonetsela dipo

Paulo sanangoonetsela kwa Timoteo zabwino zokhudza utsogoleri,koma anaululanso dipo la utsogoleri pomwe amamuonetsa Timoteo kuti utsogoleri umafuna "kupilira", "mazunzo", ndi "masautso". Timoteo anazionera yekha mtengo omwe Paulo analipira pa utsogoleri wake ndipo anatsekeledwapo kundende. (Onani Ahebri13:23) Atsogoleri ena amaitana ena poonetsa phindu lopezeka mu udindo kapena pa ntchito osaulula dipo. Koma atsogoleri muutumiki amaphunzila kufunika koonetsa omwe akuwatsogolera zabwino ndi zowawa za ulendo wa utsogoleri kuchokela pa chitsanzo cha Paulo. Poonetsela dipo amakonzekeletsa atsogoleri omwe akuphuka kumene kuti akhale ndi mopondela kuti atsilize ulendo.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi pali madela omwe ndimauza ena zoti achite koma sindinawaonetsele momwe angachitire? Kodi utsogoleri wanga ukuyendetsa mofanana chiphunzitso changa ndi chionetselo? Kodi omwe amanditsatila atha kunena kuti amadziwa za "njira ya moyowanga" kapena ndimabisa zomwe ndili kwa omwe ndimawatsogolera?
  • Kodi masomphenya a bungwe lomwe ndimatsogolera ndi omvekabwino kwa onse omwe amatsatira? Kodi ndimamangiliza cholinga cha bungwe langa ku zochotika zonse zokhudzana ndi utsogoleri zomwe ndimapempha ena kuti achite? Kodi ndingachite chani kuti ndichite bwino mudela limeneli?
  • Kodi ndimafotokoza bwino dipo la utsogoleri Kwa omwe ndikuwakuza kuti akhale atsogoleri kapena ndimayesela kubisa maululu anga ndi mavuto anga? Kodi nditha kukhala moona mtima bwanji pa za mtengo wa utsogoleri?

 

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Paulo anakuzila atsogoleri ake powapatsa mphamvu.

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online