Paulo anasankha Timoteo kuti aziyendela limodzi pa ulendo komanso kuti azakhale mtsogoleri wamtsogolo. Koma akadali ku Lusitra Paulo anazindikira kuti panafunika zokonzelela Timoteo asanafike poyenda ndi gulu.
Machitidwe a Atumwi 16
3 Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mʼderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki.
Atsogoleri ambiri amakono salabadila za mdulidwe ngati mbali ya pulogalamu yokuza atsogoleri! Koma titha kuphunzira zambiri kuchokela kwa chitsanzo cha Paulo cha momwe atsogoleri muutumiki amaxhitila pokonekeletsa omwe asankhidwa kukhala mugulu lawo.
Atsogoleri muutumiki amakonzekeletsa ena poika poyela dipo.
Timoteo mwachidziwikile anamva kuwawa pathupi lake pomwe amadulidwa ndipo pa mulingo umodzi omwe unakwanilitsa cholinga cha Paulo. Koma pa mulingo ozamilapo, Paulo amaphunzitsa Timoteo kuti utsogoleri umakhudzana ndi kupweteka komanso nsembe. Paulo asanatenge sitepe yake yoyamba pa ulendo, ankafunika kuti naye apelekepo dipo ndipo Paulo ankafuna kuti awonetsetse kuti Timoteo waikamo "khungu nayenso". Ankafuna angoona zolinga za Timoteo. Kodi Timoteo ankangofuna chabe polowa ndi chochita pamoyo wake? Kapena anali okonzeka kupeleka dipo la utsogoleri? Nkuthekatu Paulo anali ataphunzilapo phunzilo lowawa kuchokela pa zomwe anakumana nazo ndi mtsogoleri wina wachichepele, Marko,yemwe anapita pa ulendo oyamba. Marko anabwelera pomwe zinthu zinafika povuta. (Onani Machitidwe 13:5,13;15:36-41) Mwanjila iliyonse, Paulo anaonetsetsa kuti Timoteo wamvetsetsa kuti utsogoleri ndi ulendo omwe umanyamula dipo.
Atsogoleri ena amayesetsa kulimbikitsa atsogoleri omwe akuphuka kumene kuti alowe muutsogoleri poika chindunji chawo pa phindu kapena ubwino okhala mtsogoleri ndipo amatsindika pa mphotho. Koma atsogoleri muutumiki amaika kuwawa kwake Kwa utsogoleri pa ndandanda ndipo amazindikira kuti ngati mtsogoleri watsopano sangadutse mulingo,sanakonzeke kukhala mtsogoleri. Akhoza kupeleka ntchito yovuta kuti awone ngati mtsogoleri watsopanoyu angadzuke ndikufikila kuvutolo ndi cholinga chabwino. Atsogoleri muutumiki amakonzekeletsa ena poika poyela dipo.
Atsogoleri muutumiki amakonzekeletsa ena pothana ndi chotchinga.
Ngati Paulo analola Timoteo,muyuda, kuti akhale osadulidwa, zikanakhala mlamdu waukulu kwa Ayuda onse. Pomwe Paulo ankakana kuti anthu amitundu Ina sankafunika mdulidwe, sadafune kuti kuthekela Kwa Timoteo kofikila ena kupondelezedwe. Choncho, anathana ndi chotchingacho chomwe chinali pa Timoteo ndipo chinali chovuta kwambili. Atsogoleri ena amasiya zotchinga kapena amayembekezela mtsogoleri wachichepele kuti aphunzile zonse paokha. Koma atsogoleri muutumiki amafunafuna njira zochosela zotchingazo. Pomwe ululu uli ofunika kuti zolinga zitsimikizike, atsogoleri muutumiki amasakasaka kuthana ndi zikhomo zilizonse zomwe zitha kulepheletsa kagwilidwe ka ntchito kabwino ka mtsogoleri yemwe ali watsopano.
Atsogoleri muutumiki amakonzekeletsa ena popeleka zofunika kuti achitebwino
Poona kufunika koti Timoteo adulidwe Paulo amamupatsa zida kuti achitebwino ngati mtsogoleri. Timoteo akadapanda kudulidwa sakadatha kumalowa mmasunagoge momwe Paulo nthawi zonse ankalowa poyamba akafuna kuti adzale mpingo. Komanso sakadatha kuzatsogolela bwino mpingo omwe unali ndi okhulupilira a chi Yuda. Choncho,ndi mdulidwe, Paulo anamukonzekeletsa Timoteo kuti apambane.
Atsogoleri ena amaika chidwi chawo pa chipambano cha iwo okha ndipo amaona gulu lawo ngati njira yothandizila. Koma atsogoleri muutumiki amaika chidwi pa zomwe gulu lawo limafuna ndipo amawapatsa zida zofunika kuti achitebwino. Atsogoleri muutumiki amaika mulingo wa kupambana kwawo poona kupambana Kwa ena. |