Kodi munaganizapo kuti zizakhala bwanji mukazapita? Atsogoleri onse amasautsidwa ndi funso limeneli mkati mwawo kapena amangozitaya kuti mmene zizakhalilemo kaya. Muphunziro Ili,tiona kasankhidwe ka Paulo ku funso limeneli ndi njira yomwe anakhazikitsila ndondomeko ya kasankhidwe ka atsogoleri ake poonetsetsa kuti ntchito yake izapitilire akadzapita.
Kapena kuposa wina aliyense,ukadaulo wa utsogoleri wa Paulo unapangitsa kufala kwa chipembedzo Cha chi Khristu ku dziko lonse la Chi Roma. Sanagwire ntchito yekha;anakhazikitsa ndondomeko za kasankhidwe kautsogoleri zomwe zinachulukitsa mphamvu yake. Imodzi mwa zodziwitsa za izi ndi Timoteo, mtsogoleri yemwe anamusiya kukhala oyang'anila mpingo omwe Paulo anadzala ku Efisasi. Muphunzilori tiona momwe Paulo anakuzila Timoteo ndi kuphunzira momwe atsogoleri onse muutumiki angakhazikitsile ndondomeko zosankhila utsogoleri. Poyamba tiona momwe Paulo anasankhila Timoteo ndi chomwe tingaphunzile munjila zomwe Iye anatsata
Machitidwe a Atumwi 16
1 Paulo anafika ku Derbe ndi Lusitra, kumene kumakhala ophunzira wina dzina lake Timoteyo. Amayi ake anali Myuda wokhulupirira, koma abambo ake anali Mgriki.
2 Abale a ku Lusitra ndi Ikoniya anamuchitira iye umboni wabwino.
3 Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mΚΌderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki.
Kusankha atsogoleri kumafunika maso otseguka
Paulo anabwela ku Derbe kenaka ku Lusitra,komwe ophunzila dzina lake Timoteo amakhala. Paulo ankadziwa kuti kupitilira kwa ntchito yake kumafunika ena ,kotero amafufuza anthu omwe akanatha kumujoina pa ulendo wake. Maso ake anali otseguka ndiye pomwe ankaonetsetsa ophunzila a ku Lusitra anaona Timoteo. Atsogoleri ena amangokhala maso awo pa masomphenya awo ndipo saganiza za momwe zinthu zizakhalire Iwo akazachoka. Amalephera kuona zomwe ena akhoza kuchita. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti chifukwa ntchito yawo ndiyofunikira kwambiri kudziko,amafuna thandizo la Mulungu kuti apeze ena omwe azamange pa maziko awo ndi kupitiliza masomphenya awo.
Kusankha atsogoleri kumafunika kuzipeleka kupanga ubale
Paulo anaona Timoteo ndipo "anafuna kumutenga paulendo". Anali ndi chokhumba osati choti angowonjezela wantchito wa mugulu lawo,koma amafunafuna munthu oyendanaye limodzi paulendo. Paulo anali odzipeleka kupanga ubale omwe unali okuza ndi kuwumba Timoteo kuti akule ndi kuti akhale mtsogoleri oyima payekha .Anazindikira kuti kuwumba atsogoleri ndichithu chomwe chimafunika kuikiza nthawi yake , maphunziro, ndi ziphunzitso zotsatila zisanayambepo kuchuluka. Atsogoleri ena amafuna anthu athandize koma sakuwatenga limodzi nao paulendo.Amangofuna chabe anthu omwe awathandizile kukwanilitsa masomphenya awo. Atsogoleri muutumiki amasankha ena kuti akhale oyenda nawo limodzi paulendo ndipo amakhala okonzeka kuikiza mozama mwa munthu ameneyo.
Kusankha atsogoleri kumafunika kuunika mosamalitsa
Okhulupilira a ku Lusitra ndi Ikoniya analankhula zabwino za Iye(Timoteo). Paulo anali osamala pomuunika Timoteo asanamuitane kuti ajoine gulu lawo.Anali atamva kale za Timoteo asanafike ku Derbe komanso nkutheka anali atakumanapo kale mbuyo pomwe ankayendela ndi Barnabas (onani Machitidwe 14:6-23).Pa kuyendela kumeneko anakhazikitsa mpingo omwe amai ake a Timoteo ndi Agogo ake analowa.Munkhani iliyonse, ankamvetsela mosamala kwa ena,omwe ankamudziwa bwino Timoteo,anali kulankhula za Iye.Anaunika khalidwe lake pamodzi ndi ena ndiponso anaona ubwino ndi kuipa kwa kukhala kwake paudindo.Atsogoleri ena amaitana ena chifukwa akupezeka koma atsogoleri muutumiki amagwilitsa ntchito kuunika mpemphero asanafunse ena kuti awajoine . Kenaka amakhala okonzeka kumanga kasankhidwe ka atsogoleri awo posankha mtsogoleri kuti awajoine. |