Gawo #340, November 13, 2024

Yosefe, Kutumikira Mwa Chete

Munyengo iyi ya Khrisimasi okhulupilira dziko lonse lapansi amalingalira za nkhani yozizwitsa ya Mulungu kulowa mudziko lapansi ngati mwana. Ndinkhani yodzadza ndi Angelo, maloto, zozizwa ndi chidwi. Pakatikati pa nkhani tikupeza Yosefe ndi Maria pa ulendo wa ku Betelehem, kupeza khola lomwe anakagona pomwe Yesu anabandwa. Pomwe pali zinthu zambili munkhaniyi ndi maphunzilo ambili a utsogoleri, tiyeni tione mbali ya Yosefe munkhaniyi. Modabwitsa, tilibe mau aliwonse osungidwa ochokela mwa munthu ameneyu. Anatumikila mwa chete!(Welengani nkhaniyi mu Mateyu 1_2 ndi Luka 2.) Izi sizikuzonyeza kuti  sanalankhule, kungoti palibe chinthu chomwe analankhula chinasungidwa. Uchete wake ukubetchela atsogoleri muutumiki kuphunzila Kutumikira ndi chete.

Kutumikira mwachete kumasonyeza kumvetsela

Uchete wa Yosefe unamulimbikitsa kuti amvetsele ndi kumvetsela bwino! Pomwe anali kuganizila momwe angayankhile kwa chibwenzi chake chapakati anamvetsela pomwe Mulungu anali kumulankhula  ku maloto.(Mateyu 1:18_21)zikadakhala zovutilapo kwa Iye kumva kulankhula Kwa Mulungu akanakhala kuti walankhula mokweza zomwe amafuna kuti apange. Pulani inali kale mmaganizo mwake, koma sinatuluke mkamwa mwake ndipo anakwanitsa kumvetsela ndi kusintha mapulani ake. Anamvetselanso pomwe maloto ake anamuwuza kuti apite ku Igupto popewa mkwiyo wa Herodi. Anaonetsela bwino mau omwe Yakobo, nkutheka kuti ndimwana wake, analemba mtsogolo mwake, "Tsogolerani ndi makutu anu, tsatirani ndi lilime lanu, ndipo lolani mkwiyo uvutike okha pambuyo"(Yakobo 1:19) Nkutheka Yakobo anaphunzila izi kuchokela kwa bambo ake.

Atsogoleri ambiri amaika chindunji pa kulankhula ndipo amatenga nthawi yawo yaitali ndi kulankhula osati kumvetsela.Yosefe akuwaphunzitsa atsogoleri muutumiki kuti kukhala chete kumalimbikitsa kumvetsela.Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti pomwe akulankhula sakumvetsela.

Kutumikira mwachete kumakweza ena

Mateyu 2

9, Atamva mawu a mfumu, ananyamuka ulendo wawo, ndipo taonani nyenyezi anayiona kummawa ija, inawatsogolera mpaka inayima pamwamba pa nyumba yomwe munali mwanayo.10, Pamene iwo anaona nyenyeziyo, anasangalala kwambiri. 11, Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira .

(Mateyu 2:9-11a) Yosefe sanatchulidweko ngakhale pomwe anzelu akummawa anakawayendela! Ndipo mmalo ambili Maria akutchulidwa poyamba ndi kulemekezedwa kwambili. Yosefe kawilikawili akuonetsa machitidwe a mtsogoleri wamphamvu. Anatenga Maria kukhala mkazi wake atamva kuchokela kwa mgelo. Anamutcha Yesu ndipo anakamuonetsa mkachisi. Anatsogolera banja lake ku maulendo amaiko akunja. Koma anachita izi ndi mau ochepa, palibe mau omwe anasungidwa Kwa ife. Kukhala chete kwake kunakweza ena!

Atsogoleri ambiri amazikweza pamwamba okha polankula kwambili. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kuti akakhala chete za iwo okha, ena akhoza kuwala. Amakhala achangu poyamikila ena paguli lawo mmalo moti ayike chidwi chawo pa iwo eni. Amazindikira kuti kulankhula kawilikawili kumakweza olankhulayo pomwe chete amakweza ena.

Kutumikira mwachete kumalimbikitsa kudzichepetsa

Itatha nkhani ya Yosefe mukachisi atafika zaka 12, sitikumvanso kutchulidwa kwina kwa Yosefe. Maria nthawi Zina akutchulidwa Yosefe asanatchulidwe ndipo nthawi zina osatchulidwako nkomwe Yosefe anatumikira ndi chete ndipo sanapange zionetselo zokhudzana ndi kusalandila matamando kwake pa utsogoleri. Uchete umenewu ukusonyeza kudzichepetsa kwake. Kuthekela kwake komvetsela ndi kukweza ena kukuonetsa mtima odzichepetsa wa mtsogoleri otumikila.

Atsogoleri ambiri amalankhula ndipo amaonetsetsa kuti aliyense alipafupi adziwe zomwe akwanilitsa ndi kusintha komwe apangitsa mudziko. Koma atsogoleri muutumiki mwa duu ndi kawilikawili mwachete amatumikira ndi kudzichepetsa. Chete amalimbikitsa kudzichepetsa poika atsogoleri pamalo osaonekela. Kukhala chete kwa Yosefe ndi chitsanzo chabwino Kwa atsogoleri onse muutumiki. Chitsanzo chake modziwikilatu sizikupeleka tanthauzo loti tisamalankhule. Koma akutilimbikitsa Kutumikira kwambili polankhula mochepa.

Zoti tilingalire ndi kukambirana:_

  • Kodi ndi mochuluka bwanji momwe ndimatsogolera ndi chete? Kodi moyo wa Yosefe ukundiuza kuti ndizipanga chani mu utsogoleri wanga?
  • Kodi ndine wachangu polankhula kapena kumvetsela? Kodi zimenezi zikukhudza bwanji utsogoleri wanga? Kodi ndichite chani kuti ndilimbikitse kuthekela komamvetselanso?
  • Kodi pali njila yomwe posachedwapa ndazikweza ndekha polankhula? Kodi ndingachite chani kuti ndizikweza ena mwakawilikawili?
  • Kodi kuchuluka kwa kulankhula komwe ndimachita kumaonetsa chani zamtima wanga? Kodi zimaonetsela kuzikweza kapena kudzichepetsa?

Mpaka nthawi Ina, Ina wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiyambapo mutu okhudzana ndi utsogoleri wa Paulo.

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online