Gawo #339, October 16, 2024

Kutumikira Ndi Ulamuliro: Upelekeni

Atsogoleri muutumiki samasunga ulamuliro, amaupeleka! Amatsatira chitsanzo cha Yesu yemwe mau ake omaliza anali okhudzana ndi ulamuliro.

Mateyu 28

18 Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.

19 Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,

20 ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”

Yesu anakwanitsa kunena moona mtima, "Ulamuliro onse kumwamba ndi dzikolapansi wapatsidwa Kwa ine." Koma pomwe anangotsiliza kunena mauwa, anapeleka ulamuliro wake kwa ophunzira ake. anapeleka chitsanzo champhamvu kwa atsogoleri onse muutumiki.

kupeleka ulamuliro kumaonetsa chidaliro

Kuti Yesu apereke ulamuliro kwa kagulu kochepa aka kunaonetsa chidaliro chozama mwa iwo komanso zomwe anaikiza yekha mumiyoyo yawo.

Yesu ankadziwa zolakwa zawo. Koma, anawadalira kuti apititse cholinga chake kudziko lonse. Atsogoleri ena amaona kuti ulamuliro wawo ngati chinthu chawo chopezela mpata koma osachipeleka. Amakakamila kugwila ntchito yonse okha. Sagwila ntchito yokuza kapena kukhwimitsa gulu lawo. Amayembekezela ungwilo mwa otsatira awo asanawapatse ulamuliro. Koma atsogoleri muutumiki amayamba ndi chikhumbo chopeleka ulamuliro ngati chinthu chachangu ndi choyenela mwamtima onse. Amasakasaka mwai othandiza gulu lawo kuti likule ndi kuyeselera kuwapatsa ntchito zina ndi Zina. Amayembekezela zolakwitsa zina ndi zina mkatimo ndipo amawalongosolera zolakwitsa. Koma amatumikira podalira omwe akuwatsogolera. Amaona kuthekela ndi kukhumba kuona kuthekelako  kukukuzika mwa iwo kenaka kuwamasula amuke. Atsogoleri muutumiki amatumikira podalira omwe amawatsogolera.

Kupeleka ulamuliro kumapangitsa kufunsidwa pazomwe wachita

Ngakhale Yesu analankhula mau awa pomwe amachoka padziko lapansi, anakumbutsanso ophunzila "Ndili nanu nthawi zonse...." Chimenechi chinali chitonthozo chakupezeka komanso chowakumbutsa kuti pomwe ulamuliro wake anaupeleka, panalinso udindo omwe anawasiyila powatuma. Amayembekeka kuti apite ndi "kukapanga ophunzila...kubatiza....Kuphunzitsa..." Yesu sanawapatse ulamuliro kuti azikachita mulimonse momwe afunira. Anawapatsa malangizo omvekabwino ndipo azawafunsa kuti ayankhepo pa zomwe anachita. Atsogoleri ena amapereka ulamuliro popanda kalondolondo ndipo amaona ngati kutero ndekuti ndikuwadalila anthuwo kothelatu. Koma atsogoleri muutumiki amaphatikizilapo kalondolondo pomwe akupeleka ulamuliro. Amafotokoza bwino zomwe akuyembekezela pa ulamuliro omwe apatsidwawo ndiponso kuti ayembekezele kufunsidwa. Amatumikira popeleka ulamuliro ndi kuphatikizanso kuyankhapo.

Kupeleka ulamuliro kumatsimikizila kuchuluka

Njira yomwe Yesu anapelekela ulamuliro inapangitsa otsatira ake "kupita ndi kukapanga ophunzila ku maiko onse." Anamanga kuchulukitsa kupeleka kwake Kwa ntchito. Atsogoleri ena amagwira ntchito molimbika kuti bungwe lawo likule. Koma atsogoleri muutumiki amaonetsetsa kukula ndi kuchuluka popereka ulamuliro kwa omwe akuwatsogolera. Amazindikira kuti ngati akakamile kugwila ntchito yonse okha, ntchito yonse sizagwirika. Atsogoleri muutumiki amaonetsetsa kuchulukitsa popeleka ulamuliro.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi ndimulingo uti wa kudalira omwe ndili nawo mwa atsogoleri amaudindo akuluakulu omwe ali mugulu langa? Kodi ndingachite chani kuti ndionetsele  kukhulupilira kwanga mwa iwo? Kodi ndimatha kupeleka ulamuliro mwachangu Kwa omwe ndimawatsogolera?
  • Pomwe ndapeleka ulamuliro kodi ndimafotokoza momveka bwino zomwe zikuyembekezeka kuti achite? Kodi ndimasintha munjila yoyenelera mulingo wa udindo pomwe anthu a mugulu langa akukula ndi kukhwima?
  • Kodi utsogoleri wanga umapeleka kuchulukitsa kwatunthu kofunikila kubungwe kwanga? Kodi ndikulamulira munjila ziti kuti ndilimbikitse kukula ndi kuchuluka kwa maudindo a utsogoleri?
  • Mulingalirenso mozama maphunziro okhudza ulamuliro (maphunziro 336-339). Munjira iti yomwe ndingagawane mfundo zimenezi ndi omwe ndimawatsogolera?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona za nthawi ya Khrisimasi.

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online