Gawo #338, October 02, 2024

Kutumikira Ndi Ulamuliro: Ugwiritseni Ntchito 

Atsogoleri muutumiki samazemba ulamuliro, amaugwilitsa ntchito kuti utumikire! Amaulandila ulamuliro ngati njira yomangilira ena, kupititsa bungwe minjira yomwe imayenera kuti ipite, ndi Zina zotero. Paulo, monga tinaonera muphunziro lapitali, anagwiritsa ulamuliro pomangilira ena. Tsopano, tiyeni tione pa mfundo yaifupi yomwe anapanga yomwe ndi yodzadza ndi mfundo za utsogoleri zokhudzana ulamuliro.

1 Akorinto 11

1 Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu.

Paulo molimbamtima ndi mosabweza mau akuwauza okhulupilira a ku Korinto kuti atsatire chitsanzo chake! Akugwiritsa ntchito ulamuliro wake kuti awatengele ku  njila yomwe akufunika kupita. Akutumikira pogwilitsa ntchito ulamuliro ndipo nkulankhula kwake kukupeleka zinthu zingapo momwe atsogoleri muutumiki amagwilitsira ntchito ulamuliro.

Kugwilitsa ntchito ulamuliro kumakhudzana ndi kuonetsa chitsanzo.

"Tsatirani chitsanzo changa,monga inenso..." Paulo akufotokoza momveka bwino kuti sakufuna kuti ena apange chinthu chomwe sakufuna kuchita. Akuwauza kuti achite chomwe akhala akumuona akuchita. Akupeleka chitsanzo pokhala pansi pa ulamuliro asanayambe kulamula. Ndi otsatira asanakhale mtsogoleri. Atsogoleri ena amapereka chitsogozo koma sapereka chitsanzo pa zomwe akufuna ena achite. Atsogoleri muutumiki choyamba amaonetsa njira kenaka amafunsa ena kuti atsatire. Ichi chikukakamiza atsogoleri muutumiki kuti choyamba aziunike miyoyo yawo asanaitane ena kuti atsatire. Amazindikira kuti akufunika kupanga chitsanzo  ngodya zawo, cholinga ndi ndondomeko za bungwe lomwe akutsogolera asanafunse molimbamtima ena kuti atsatire. Pomwe akupelewera, amazindikira kulephera kwawo ndipo amafunafuna kupita patsogolo. Potero, sachita manyazi kuwauza ena, "khala ndi kuyenda monga ine!" Atsogoleri muutumiki amaonetsela njira asanagwiritse ntchito ulamuliro kuwauza ena kuti atsatire. Amatumikira ena popereka njira yachitsanzo.

Kugwilitsa ntchito ulamuliro kumaonetsa chitsogozo

Paulo, mu mau awa ochepa amagwilitsa ntchito ulamuliro wake kuti upeleke chitsogozo kwa omwe amamutsatira "Tsatirani chitsanzo changa..." Sakuchita manyazi kuika milingo ya zomwe akuyembekezela kuchokela kwa otsatira ake. Pomwe akuchita izi, akubweretsa chindunji ndi chitsogozo chomwe akufuna anthu ake apite. Atsogoleri ena samafuna kulozela ena munjila  yomvekabwino. Amamva ngati kuti Kutumikira ena kumatanthauza kuyenda pamene aliyense wagwirizana nazo. Atsogoleri omwe amafuna chivomelezo kuchokela kwa aliyense sangapite patsogolo. Atsogoleri muutumiki amamvetsetsa kuti ulamuliro wawo unapatsidwa kwa iwo pachifukwa choti apereke chitsogozo. Mokondwela amasakasaka zinthu zoti apange ndi uphungu kuchokela kwa gulu lawo koma sanyalanyaza kuika momveka bwino njira yoti atsatire imene ikufunika. Amatumikira cholinga cha bungwe polozela njila yomwe ikufunika.

Kugwilitsa ntchito ulamuliro kumapangitsa kuchitika kwazinthu

Utsogoleri umakhudzana ndi kupangitsa zinthu kuti zitheke, kugwiritsa ntchito ulamuliro kumathandiza anthu kuti ayende munjila yofunikira. Langizo la Paulo pamenepa ndi muitano omveka bwino kwa okhulupilira a ku Antiokea kuti achite chinachake. Akupeleka chitsanzo cha moyo wa Iye mwini. Akulozela chitsogozo kuti kuyenda kukufunika. Pomwe akutumikira ndi machitidwe a utsogoleriwa ,akutakasa kuchitapo kanthu kuchokela kwa otsatira ake. Malangizo a Paulo pamenepa atha osaoneka ngati palibepo chitsanzo chake, koma akuti "Tsatirani" ngati kulamula, langizo. Ndi muitano wochitapo kanthu, otengela anthu ku chitsogozo.

Atsogoleri ena amagwilitsa ntchito udindo wawo powauza anthu zochita. Amagwiritsa ntchito mphamvu ya ndalama kapena zokopela anthu zina kuti zithandizile anthuwo kuchita zinthu. Koma atsogoleri muutumiki amagwilitsa ntchito ulamuliro wawo kutakasa ena kuchita. Pomwe atsogoleri muutumiki akuonetsa njira ndi kufotokoza bwino njila yoti itsatidwe, amatakasa kuchitika kwa zinthu! Omwe amatsatira amamvetsetsa zomwe akuyenela kuchita ndipo amalimbikitsika kuti apite chitsogolo. Mtsogoleri muutumiki ndi chopatsa mphamvu chomwe ndi chopatsa mphamvu ena! Amatumikira potakasa kuchita zinthu kuchokera kwa ena.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi ndingapereke chitsanzo chabwino motani ku cholinga, ngodya, ndi zokhumba za bungwe lomwe ndimatsogolera? Kodi izi zikukhudza bwanji kuthekela kwanga kotumikira gulu langa? Nditha kunena molimbamtima,"Tsatirani chitsanzo changa"?
  • Kodi ndikugwiritsa bwino motani ulamuliro wanga kuti upeleke chitsogozo kwa omwe ndikuwatumikira? Kodi ndine ofuna kutsogolera pomwe anthu akugwilizana ndi mfundo zanga kapena kutsogolera popanda kufunsila kwa ena? Kodi ndingachite chani kuti anthu amvetsetse kufunika kwa  chitsogozo chomwe chikufunika mu bungwe langa?
  • Kodi utsogoleri wanga umalimbikitsa motani ena kuti achite kanthu? Kodi pali njira zomwe ndimagwilitsira ntchito ulamuliro wanga kukakamiza ena kuti achite zinthu mmalo mowatakasa kuti achite zinthu?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona momwe atsogoleri muutumiki amapelekela ulamuliro.

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024