Gawo #337, September 18, 2024

Kutumikira Ndi Ulamuliro: Chivomelezeni

Atsogoleri muutumiki amalemekeza ulamuliro wa omwe ali pamwamba pawo komanso amavomeleza ulamuliro omwe waikidwa mwa iwo. Amazindikira ndi kuvomeleza kuti udindo uliwonse wa utsogoleri opelekedwa umayendela pamodzi ndi ulamuliro ogwira ntchito yomwe ikuyembekezeka pa udindowo. Paulo anayankhula monvekabwino za ulamuliro wake monga Iye mtumwi.

2 Akorinto 10

8 Tsono ngakhale nditadzitama momasuka za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa woti tikukuzeni osati kukuwonongani, ndithu sindidzachita manyazi.

Paulo anali ndi kumvetsetsa kwabwino kwa ulamuliro wake ndipo anachivomeleza chimenechi kuti ndi mphatso yopelekedwa Kwa Iye kuchokela kwa Mulungu kuti akwanilitse cholinga chomwe  Mulungu anampatsa. Akuthandiza atsogoleri muutumiki kuti apange chimodzimodzi.

Kuvomeleza ulamuliro kumathandizila kufunsidwa pazomwe wachita.

"Ulamuliro Mulungu anatipatsa..." Paulo anazindikira kuti ulamuliro umenewu unachokela kwa Mulungu ndipo kotero kuti amayankha kwa Mulungu momwe anagwiritsila ntchito ulamuliro umenewu. Chochokela kwa Mulungu ndi chabwino ndipo chizigwilitsidwa ntchito ku zolinga Zake. Atsogoleri ambiri, makamaka omwe anavulazidwa mbuyumu pogwiritsidwa ntchito molakwika kapena omwe anatsogolera ena omwe anavulazidwapo munjila yoteleyi amathawa ulamuliro ndi kusiya kugwiritsa ntchito ulamuliro wawo. Amakhala ndinkhawa yaikulu pankhani yogwiritsa ntchito ulamuliro molakwika kotero kuti amaphonya kugwiritsa ntchito ulamuliro pa cholinga chomwe chili chabwinobwino.

Atsogoleri ena amaona kuti ndichovuta kuvomeleza ulamuliro wawo chifukwa zimaonetsa ngati akufunafuna mphamvu mwa iwo eni. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti mautsogoleri onse ovomelezeka amachokera kwa Mulungu, ndipo amayankha kwa Iye pa momwe anagwiritsila ntchito ulamulirowo. Komanso amazindikira kuti azayankha kwa Iye ngati alephela kugwilitsitsa ntchito ulamuliro omwe anapatsidwawo! Atsogoleri muutumiki amavomereza ulamuliro chifukwa amazindikira kuti ali pansi pa ulamuliro.

Kuvomeleza ulamuliro kumapangitsa chindunji

"Ulamuliro Ambuye anatipatsa kuti ukumangilire osati kuti  ukakuononge.." Paulo anafotokoza momveka bwino pa za chindunji cha ulamuliro wake,unali omangilira ena, osati kuwaononga. Chidwi cha ulamuliro ndi choti omwe akutumikiridwa apindule ndi yemwe ali mu ulamuliro. Atsogoleri ambiri agwiritsa ntchito ulamuliro poononga anthu kapenanso pakumanga maufumu awo.

Paulo akufotokoza momveka bwino kuti ulamuliro ukhale ndi cholinga cha pa ena. Ulamuliro unaikidwa ndi cholinga cha Mulungu kuti ukhale dalitso Kwa ena.Amakana kuvomela kusadalirika kwa ulamuliro komwe kunalipo ngati chifukwa cholephelera kuti agwiritse ntchito ulamuliro wawo. Amakhala ozipereka kugwila zonse mkati mwa mphamvu ndi ulamuliro wawo kuti amangilire ena . Umenewo nde ulamuliro otumikila.

Kuvomeleza ulamuliro kumazutsa kutsimikizika mtima

Paulo anavomeleza ulamuliro wake,ndipo zinamupatsa tutsimikizika pa udindo wake. Kutsimikizika mtima kwake kutha kuoneka ngati kuzikweza chifukwa anafika pa mulingo onena mozitukumula za ichi." Sindidzachita mantha za ichi." Akuyamba ndi kumalizitsa vesili akulengeza  chitsimikizo chake pa ulamuliro wake. Koma komaliza kwa malankhulidwe ake akuonetsa bwino kuti sakungofuna kukopa chidwi cha anthu mumpingo pa udindo wake wapadeladelawo. Chitsimikizo cha Paulo chagona pa kumvetsetsa kwake pa komwe ulamuliro unachokela ndi cholinga chomwe anamupatsila. Pomwe nkhani izi zamveka bwino kuzidalira si kuzikweza kapena kuzikuza, koma ndi koma ndi njira chabe yoyenelera yakuvomeleza. Atsogoleri onse amafunika kutsimikizika mtima kuti atsogolere. Kutsimikizika kwawo kumatakasa ena kuti atsatire. Atsogoleri muutumiki amavomereza ulamuliro wawo ndipo amakhala ndi chitsimikizo pomwe akuwugwiritsa ntchito muzolinga zomwe unapatsidwila Kwa iwo.  Amapereka chilimbikitso kwa ena kuti atsatire pomwe akuvomereza kuti udindo wawo umawapatsa ulamuliro otumikila.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi ulamuliro wanga wambuyomu waumba bwanji maonedwe anga a udindo wanga? Ndimunjila iti yomwe chitsanzo cha Paulo chikundilimbikitsa kuti ndizindikire ndi kuvomeleza ulamuliro wa Umulungu?
  • Kodi ndikuona ulamuliro wanga kuti ukuchitachita pansi pa ulamuliro wa  Mulungu yekha? Kodi izi zikuotseledwa bwanji mu utsogoleri wanga?
  • Kodi ulamuliro wanga kawirikawiri umamangilira ena kapena umawapasula? Kodi ndingapereke zitsanzo ziti za momwe ndaonetsela izi musabata yapitayi?
  • Kodi ndili ndi chitsimikizo motani ngati mtsogoleri? Kodi ndimunjila ziti zomwe ndi  zogwirizana ndi momwe ndimaonela ulamuliro wa ine mwini? Kodi ndikuyenera kusintha pati kuti ndikhale ndi chitsimikizo chomwe Paulo anaonetsa?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona momwe atsogoleri muutumiki amagwilitsira ntchito ulamuliro.

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024