Atsogoleri muutumiki, ngati atsogoleri ena onse, ali ndi ulamuliro komanso amagwilitsa ntchito ulamuliro. Ulamuliro ndi mphamvu yopelekedwa yomwe imawapatsa ufulu ochita monga mwa udindo wawo ngati mtsogoleri. Koma atsogoleri ambiri amatenga nkhani ya ulamuliro mwa njila yosakhala bwino. Kodi ulamuliro ndi wabwino kapena ayi? Kodi zimayendelana bwino motani ndi mchitidwe otumikila ena? Muphunziro limeneli tiunikila momwe atsogoleri muutumiki ulamuliro amaonela ndi kugwilitsila ntchito ulamuliro. Poyamba, pongoonako pang'ono pamoyo wa Davide zikuonetsela kuti atsogoleri otumikila amapatsa ulemu ulamuliro omwe uli pamwamba pawo. Davide anadzodzedwa kukhala mfumu, koma Saulo anali akadali pampando ndipo ankathamangitsa Davide ndi gulu lake. Kawili konse, Davide anali ndi mwayi osavuta oti aphe Saulo ndi kutenga ufumu. Mu imodzi mwa nthawizi, Davide anadula pambali pa mkanjo wa Saulo.
1 Samueli 24
5 Atachita izi, Davide anatsutsika mu mtima chifukwa anadula msonga ya mkanjo wa Sauli.
6 Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.”
7 Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka.
Kuziletsa kwa Davide kukuonetselatu poyela ulemu wake pa ulamuliro wa Saulo ngakhale kuti Saulo ankafunafuna kumupha.Davide amazindikira kuti Saulo anali mfumu ndipo amalemekeza udindo wake ngakhale sankagwilizana ndi zochita za mfumu. Kuyankha Kwa Davide kukuonetsela atsogoleri muutumiki zotsatila za ulemu kwa omwe akuwalamulira pamwamba pawo.
Ulemu ku ulamuliro umamanga khalidwe
Nthawi imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri mmoyo wa Davide pomwe anali kuthamangitsidwa ndi mfumu Saulo. Inali nthawi yomwe khalidwe lake linayesedwa ndi kuumbidwa munjila zamphanvu kwambili. Chofunika kwambili, Davide amaphunzila kuti asanakhale muulamuliro, ankayenela kukhala kuphunzira kukhala pansi pa ulamuliro. Zimenezi nthawi zonse ndi phunziro lovuta kwambiri kwa atsogoleri ndipo zovutanso kwambiri pomwe munthu yemwe ali muulamuliro asali mtsogoleri wabwino! Koma atsogoleri muutumiki amapereka ulemu kwa ulamuliro omwe ulipo ndipo amalola Mulungu kuti awumbe khalidwe lawo pomwe akuonetsa ulemu wawo kudzela mumawu awo ndi ntchito zawo.
Ulemu ku ulamuliro umamanga chidaliro
Davide anachita zinthu ndi ulemu ku ulamuliro chifukwa chinali chinthu chabwino kutelo. Koma otsatira ake analinso kuona. Pomwe amaona ulemu wa Davide kwa Saulo anakula mu chidaliro chawo pa Davide. Anaona kuti anali "ovutika ndi chikumbumtima" atadula mkanjo wa Saulo. Anamunva akumufotokoza mdani wake ngati "odzodzedwa wa Mulungu". Pomwe ankamuonetsetsa kwambiri, anazindikira kuti Davide anali mtsogoleri yemwe akanadalira. Atsogoleri muutumiki amamanga chidaliro ndi omwe akuwatsata pomwe akupeleka ulemu kwa ku ulamuliro omwe uli pamwamba pawo.
Ulemu ku ulamuliro umamanga anthu
Machitidwe a Davide anabetchela ndi kuumba omwe ankamutsatira. Ngakhale sanali kugwilizana ndi zomwe ankachita ulemu wa Davide kwa Saulo kuwathandizila kukula. Davide amawathandiza kuwakuza powadzudzula pomwe zomwe ngodya zawo sizinagwilizane ndi zake. Pomwe anthu akewa anachitila umboni kumvela kwa Davide kwa Saulo, nawonso anayamba kukhala omvela kwambili kwa Davide. Anthuwa akatumidwa kunkhondo amatha kupita ndikukapanga chipambano chachikulu kwa Davide. Anadziwa kuti chifukwa Davide anali ndi ulemu kwa ulamuliro, sakadatha kugwilitsitsa ntchito ulamuliro molakwika atakhala pampando. Atsogoleri muutumiki amatumikira omwe akuwatsata popatsa ulemu ulamuliro omwe uli pamwamba pawo. Popanga zimenezi amamanga anthu owazingulira. |