jpeg

Gawo #334, July 24, 2024

Barnaba: Kutumikira Ndi Kulephela

Barnaba anali mtsogoleri wamphamvu ndipo taonapo zinthu zambiri zazikulu kuchokela mmoyo wake. Koma sanali osalakwitsa! Zinthu ziwiri zinalembedwa zomwe zikuonetsela zolakwitsa zake.

Machitidwe a Atumwi 15

36 Patapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, “Tiyeni tibwerere kuti tikaone abale ku mizinda yonse imene tinalalika Mawu a Ambuye ndipo tikaone mmene akuchitira.” 37 Barnaba anafuna kutenga Yohane, wotchedwanso Marko, kuti apite nawo. 38 Koma Paulo anaganiza kuti sichinali cha nzeru kumutenga Yohane chifukwa iye anawathawa ku Pamfiliya ndipo sanapitirire nawo pa ntchito. 39 Iwo anatsutsana kwambiri kotero kuti anapatukana. Barnaba anatenga Marko ndipo anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 40 Paulo anasankha Sila. Abale atawapempherera kwa Ambuye kuti alandire chisomo, ananyamuka. 41 Iye anadutsa ku Siriya ndi ku Kilikiya kupita akulimbikitsa mipingo.

Atatumikira pamodzi ngati gulu lamphamvu kwa zaka, Paulo ndi Barnaba sanagwilizane kuti  atamutenge Maliko pa ulendo  womwe unalipo! Mkangano waukulu osathawu ndi omaliza kuunva pa Barnaba mubuku la Machitidwe!

Kapena mkangano oziwika bwinowu usanachitike, panalinso kutsutsana pa nkhani ya mdulidwe ku Antiokea. Petulo anachita mwachinyengo ndipo anadzudzulidwa pagulu ndi Paulo. Polemba zomwe zinachitikazi, Paulo anatinso:

Agalatiya 2

13 Ayuda enanso anamutsata pochita zachinyengozi, kotero kuti ngakhale Barnaba anasocheretsedwa chifukwa cha chinyengo chawocho.

Mmene zilirimu, Barnaba ndi Petulo akuonetselatu kuti analakwitsa (werengani). Koma zolephela za Barnaba zikuonetsela kwa atsogoleri kuti ngakhale mukulephela kwathu, tikhoza Kutumikira ena.

Kulephela kwa Barnaba kumatumikila poonetsela kuti kulephela kumakhalapo.

Paulo anaganiza mwapamwamba za Barnaba mpaka anati "ndi Barnaba yemwe anasocheletsedwa". Akutanthauza kuti Barnaba anali munthu omalizila yemwe amayembekezela kuti sangapange kulakwitsaku! Koma Barnaba analakwitsa ndipo zikuotsa atsogoleri onse kuti aziyembekezela kulephela. Mwachidziwikile, sichimakhala cholinga kapena kukonzekela kulephela, koma tizidziwilatu. Atsogoleri ena amaona ngati kulephela ndi chizindikilo choti zakukanika, choncho amamva kukakamizika kuti aziphimbe, kukana kapena kusalabadila kulephela. Koma atsogoleri muutumiki amavomereza umunthu wawo ndi choonadi ichi choti atsogoleri onse amalephera. Amazipatsa okha chisomo ndi kupempha chisomo kuchokela kwa ena akalephela. Popanga zimenezi, amatumikira ena poonetsela kuti kulephela kumakhalapo.

Kulephela kwa Barnaba kumatumikila kuti kulephela sikutha kwako.

Nkhani ya Barnaba yomwe inasungidwa ikuthela pa kusamvana pakati pa iyeyo ndi Paulo koma ntchito yake sinathele Barnaba anatenga Marko pa ulendo wake wautumwi  ndipo pamene sitikudziwa zotsatila, mwachidziwikile tikuyembekezela kuti mipingo yomwe inadzalidwa inalimbikitsidwa ndiponso Ina inadzalidwa kudzela muntchito zawo. Atsogoleri ena amaona ngati kulephela ndi kutha kwa ntchito yawo koma atsogoleri otumikila amamvetsetsa kuti kulephela sipothela. Amaphunzila kupitiliza ulendo pa kulephela kulikonse  ndipo amatumikira poonetsa kuti kulephela sikutha.

Kulephela kwa Barnaba kumatumikila poonetsela kuti kulephela kutha kupangitsa kukula

Paulo ndi Barnaba onse anakula kudzela kusamvana kwawo. Paulo patsogolo pake anafunsa Marko kuti amuthandize( Onani 2 Timoteo 4:11). Barnaba anali ngati mtsogoleri wa gulu pomwe ankayenda ndi Marko. Mulungu anagwilitsa ntchito kusamvana kwawo kuti atumize magulu awiri mmalo mwa limodzi ndipo anabweletsa kukula mmipingo mwawo. Pa nkhani ya mdulidwe onse Barnaba ndi Petulo anaona zolephela zawo ndipo anakonza. Atsogoleri ena amaona ngati kulephela ndi kutha kwa kukula koma atsogoleri muutumiki amaona kulephela kwawo ngati mwai oti akule. Amafunsa chimene chinalakwika ndi chomwe angaphunzile. Amabweza, amasintha ndi kutengela ngati nkofunika kutero basi nkumapitiliza cholinga! Amatumikira magulu awo pokula kudzela mukulephela.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi kulephela kwa Barnaba kumatumikila bwanji kwa ine ngati mtsogoleri? Kodi ndingachitepo chani msabatayi kuti ndikhale motsatila Iyeyu pomwe ndikuchitapo kanthu pa zolephela zanga?
  • Kodi ndimaona kulephela kuti kumakhalapo pa utsogoleri wanga? Ngati ndi choncho, kodi ndimauza motani ena ? Ngati sichoncho, kodi izi zitha kukhudzana bwanji ndi momwe ndimaonela ndi kuchitila kwa ena pa kulephela kwawo?
  • Kodi ndinavomeleza kulephela kwambuyo kundilepheletsa kuchita zomwe ndimayenera kuchita? Ngati ndichoncho, kodi ndingatsatire ndondomeko ziti kuti ndibwelere munjila yoyenera?
  • Kodi ndimunjila ziti zomwe kulephela kwanga kwabweletsa kukula kumoyo wanga ndi ku utsogoleri wanga? Kodi ndindani akufunika kuti amve zomwe ndaphunzilazi ndipo ndiliti lomwe ndingagawane nawo nkhani yanga?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler,

 

Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Barnaba anatumikilira ndi khalidwe.

*Chofunika. Ophunzira amatsutsana ngati ulendo wa Petulo ku Antiokea unali oyambilira kapena otsilizira  nkumano wa akulu akulu ku Jerusalem usanachitike komwe nkhani ya mdulidwe inakambidwa ndikuthetsedwa ndi atsogoleri a mpingo. (Onani Machitidwe 15) Koma ngati ulendowo unali pambuyo pake, zolephela za Petulo ndi Barnaba zinali zoipa kwambiri. Koma kaya zinachitika liti onsewo analepherabe kukhala mmoyo olingana ndi mau a uthenga wabwino.

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024